Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Himogulobini Inapangidwa Mogometsa Kwambiri

Himogulobini Inapangidwa Mogometsa Kwambiri

Himogulobini Inapangidwa Mogometsa Kwambiri

“Kupuma kumaoneka ngati kophweka, koma zikuoneka kuti kupuma, komwe ndi chizindikiro chakuti munthu ali moyo, kumatheka chifukwa cha maatomu osiyanasiyana. Maatomu amenewa amapezeka mu molekyu inayake yaikulu, yomwe mkati mwake mumachitika zinthu zodabwitsa.”—Anatero Max Perutz, amene analandira nawo mphoto ya Nobel mu 1962 chifukwa chochita kafukufuku wokhudza himogulobini.

KUPUMA n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi moyo, ngakhale kuti ambirife sitikhala pansi n’kuganizira kuti kodi zimatheka bwanji kuti tizitha kupuma. Komabe, kupuma pakokha sikokwanira kuti tikhale ndi moyo. Pamafunikanso himogulobini, yomwe inapangidwa modabwitsa kwambiri ndi Mlengi wathu. Himogulobini ndi molekyu imene imapezeka m’maselo ofiira a magazi. Maselowa alipo okwana 30 thililiyoni m’thupi mwathu, ndipo amatenga mpweya wa okosijeni m’mapapo n’kuupititsa mbali zosiyanasiyana za thupi lathu. Popanda himogulobini, tikhoza kufa nthawi yomweyo.

Kodi himogulobini imatha bwanji kunyamula mpweya wa okosijeni pa nthawi yoyenera, kuusunga bwinobwino, kenako n’kuutulutsa pa nthawi yoyeneranso? Kuti zimenezi zitheke, pamachitika zinthu zosiyanasiyana zogometsa.

Himogulobini Ili Ngati Kagalimoto Konyamula Anthu

Himogulobini tingaiyerekezere ndi kagalimoto kakang’ono ka zitseko zinayi, konyamulanso anthu anayi. Kagalimoto kameneka kamakhala mkati mwa selo lofiira la magazi, lomwe tingaliyerekezere ndi chigalimoto chachikulu. Kagalimotoka sikakhala ndi woyendetsa chifukwa kamanyamulidwa ndi chigalimoto chachikulucho. Mkati mwa selo lofiira limodzi mumakhala mamolekyu ambirimbiri a himogulobini.

Ulendo wa mamolekyu amenewa umayamba maselo ofiira akafika m’mapapo. Mapapowa tingawayerekezere ndi malo okwerera galimoto. Tikakoka mpweya, timamolekyu ta okosijeni tambirimbiri timafika m’mapapo mwathu ndipo timakhala ngati tafika pamalo okwerera galimoto n’kumadikirira galimoto yoti tikwere. Kenako pasanapite nthawi yaitali, timamolekyu timeneti timalowa m’maselo ofiira a magazi, amene ali ngati zimagalimoto zikuluzikulu zonyamula timagalimoto ting’onoting’ono. Pa nthawiyi, zitseko za mamolekyu a himogulobini amene ali mkati mwa selo lofiira lililonse zimakhala zotseka. Koma pasanapite nthawi yaitali molekyu imodzi ya okosijeni imadzipanikiza mpaka kukwanitsa kulowa mu himogulobini.

Kenako, pamachitika zinthu zina zochititsa chidwi. Mkati mwa selo lofiira lija, himogulobini imayamba kusintha kaonekedwe. Mukangolowa molekyu imodzi ya okosijeni ija, zitseko zonse zinayi za himogulobini zimayamba kutseguka zokha. Kenako mamolekyu ena atatu a okosijeni amalowa mosavutikira, ndipo zikatere kagalimotoko kamakhala kuti kadzaza. Zimenezi zimachitika mofulumira kwambiri moti munthu akamamaliza kukoka mpweya, pafupifupi mipando yonse ya timagalimoto ting’onoting’ono tonse ta himogulobini timene tili mu selo lofiira, imakhala itadzaza ndi mamolekyu a okosijeni. Mu selo lofiira limodzi lokha la magazi mumakhala mamolekyu a himogulobini opitirira 250 miliyoni, amene amanyamula mamolekyu a okosijeni pafupifupi 1 biliyoni. Nthawi yomweyo, maselo ofiira amayamba ulendo wokapereka okosijeni kumbali zina za thupi lathu zomwe zikufunikira okosijeni. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi n’chiyani chimathandiza kuti mpweya wa okosijeni umene uli mkati mwa selo lofiira la magazi usatuluke usanafike kumene ukufunikira?’

Yankho la funso limeneli ndi lakuti mamolekyu a okosijeni akafika mkati mwa molekyu iliyonse ya himogulobini, amakadziphatika ku maatomu a aironi. Koma dziwani kuti nthawi zambiri mpweya wa okosijeni ukakumana ndi aironi ndi madzi, pamachitika dzimbiri. Dzimbiri likachitika, mpweya wa okosijeni uja umatsekeredwa malo amodzi moti sungayendenso. Ndiye kodi zimatheka bwanji kuti molekyu ya himogulobini izitha kuphatikiza aironi ndi okosijeni m’magazi, mmene mumakhalanso madzi, koma dzimbiri osachitika?

Mmene Himogulobini Imagwirira Ntchito

Kuti timvetse zimene zimachitika, tiyeni tione mmene himogulobini imagwirira ntchito. Mu molekyu imodzi ya himogulobini mumakhala maatomu osiyanasiyana 10,000 a hayidirojeni, kaboni, nayitilojeni, safa ndi okosijeni. Maatomu onsewa anasanjidwa bwinobwino n’kukhala mozungulira maatomu anayi a aironi. N’chifukwa chiyani maatomu anayi okha a aironi amafunika kuzunguliridwa ndi maatomu ambirimbiri chonchi?

Maatomu a aironi amenewa amakhala osakhazikika ndipo amafunika kuwateteza chifukwa ngati atamangoyendayenda mkati mwa selo, akhoza kuwononga zinthu zambiri. Choncho atomu iliyonse ya aironi imakhala mkati mwa kanthu kenakake kamene kamakhala ngati mpanda. Popeza maatomu a aironi alipo anayi, mipandayi iliponso inayi. Mipanda inayi imeneyi inasanjidwa mkati mwa molekyu ya himogulobini m’njira yoti okosijeni athe kufika kumene kuli maatomu a aironi, koma madzi asathe kufikako. Ndipo chifukwa cha zimenezi, dzimbiri silichitika.

Mmene Okosijeni Amalowera M’thupi Lonse

Maselo ofiira akachoka m’mitsempha ikuluikulu n’kulowa m’timitsempha ting’onoting’ono mkatikati mwa thupi lathu, amakafika kumalo osiyana kwambiri ndi kumene achokera. Malo atsopanowa amakhala otentherapo komanso amakhala ndi okosijeni wochepa. Ndiponso amakhala ndi asidi wambiri chifukwa cha kuchuluka kwa mpweya woipa. Zinthu zimenezi zimachititsa himogulobini kudziwa kuti ndi nthawi yotulutsa mpweya wa okosijeni uja.

Mamolekyu a okosijeni akatuluka mu himogulobini, molekyu ya himogulobini imatseka zitseko zake kuti okosijeni uja asabwererenso mkati mwa himogulobini koma akhale kunja, kumene akufunikira kwambiri. Kutseka zitsekozi kumathandizanso himogulobini kuti ikamabwerera kumapapo isanyamule mwangozi okosijeni wina. M’malomwake, imanyamula mpweya woipa wambiri kuchokera mbali zosiyanasiyana za thupi kuti ipite nawo kumapapo.

Maselo ofiira, omwe pa nthawiyi amakhala alibe okosijeni, akafika kumapapo, himogulobini imatulutsa mpweya woipa umene inanyamula uja. Kenako imayambiranso kutenga mpweya wa okosijeni kuti ikaupereke kumbali zosiyanasiyana za thupi. Zimenezi zimachitika maulendo masauzande ambiri kwa masiku pafupifupi 120 amene selo lofiira la magazi limakhala ndi moyo.

Tingathe kuona kuti himogulobini si molekyu wamba. Mogwirizana ndi mawu amene ali kumayambiriro kwa nkhani ino, himogulobini ndi “molekyu . . . yaikulu, yomwe mkati mwake mumachitika zinthu zodabwitsa.” Ndithudi, timagoma ndiponso timathokoza kwambiri Mlengi wathu chifukwa cha nzeru zake zakuya, zimene zimatithandiza kuti tikhale ndi moyo.

[Bokosi/Tchati patsamba 28]

ZIMENE MUNGACHITE KUTI HIMOGULOBINI IZIGWIRA BWINO NTCHITO

Anthu akamati, ‘Magazi achepa m’thupi,’ kwenikweni amakhala akutanthauza kuti m’magazi mulibe himogulobini wokwanira. Ngati mu himogulobini mulibe maatomu anayi a aironi, ndiye kuti maatomu ena 10,000 amene amapezekamo amakhala opanda ntchito. Choncho, m’pofunika kwambiri kuti munthu azidya zakudya zoyenera n’cholinga choti akhale ndi aironi wokwanira. Kumanjaku tasonyeza zakudya zina zimene zili ndi aironi wambiri.

Kuwonjezera pa kudya zakudya zokhala ndi aironi wambiri muyeneranso kutsatira malangizo awa: 1. Nthawi zonse muzichita masewera olimbitsa thupi. 2. Musamasute fodya. 3. Muzipewa kukhala pafupi ndi munthu yemwe akusuta fodya. Kodi n’chifukwa chiyani utsi wa fodya uli woopsa kwambiri?

N’chifukwa chakuti utsi wa fodya umakhala ndi poizoni, amene amapezekanso mu utsi wa galimoto kapena utsi wa mbaula. Anthu amafa mwangozi chifukwa cha utsi umenewu ndipo anthu ena amadzipha dala pogwiritsa ntchito utsiwu. Utsiwu ukafika mu himogulobini umaphatikizana ndi maatomu a aironi mwachangu kwambiri kuposa mmene umachitira mpweya wa okosijeni. Choncho utsi wa fodya umapha munthu mosavuta chifukwa umalepheretsa munthu kupeza okosijeni wokwanira.

[Tchati]

ZAKUDYA ZIMENE ZILI NDI AIRONI WAMBIRI

Nyemba zouma

Chiwindi

Mphodza

Sipinachi

Nyama ya nkhumba

Nyama ya nkhukutembo

Mazira

Nyama ya ng’ombe

Nyama ya nkhuku

[Chithunzi patsamba 26]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Puloteni

Okosijeni

Atomu ya aironi

Mpanda wa aironi

Molekyu ya okosijeni imadziphatika ku himogulobini m’mapapo, mmene mumakhala okosijeni wambiri

Molekyu imodzi ya okosijeni ikadziphatika ku himogulobini, molekyu ya himogulobini imasintha pang’ono. Zimenezi zimathandiza kuti mamolekyu ena atatu a okosijeni adziphatike ku himogulobini msangamsanga

Himogulobini imatenga mpweya wa okosijeni m’mapapo n’kuupititsa kumbali zosiyanasiyana za thupi kumene ukufunikira