Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalidwe Labwino Limene Aphunzitsi Amachita Nalo Chidwi

Khalidwe Labwino Limene Aphunzitsi Amachita Nalo Chidwi

Khalidwe Labwino Limene Aphunzitsi Amachita Nalo Chidwi

● Irena ndi mtsikana wa sitandade 8 ndipo amakhala m’mudzi winawake wotchedwa Kurtovo Konare m’dziko la Bulgaria. Mayi ake anapatsa aphunzitsi ake buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza pamsonkhano wa makolo ndi aphunzitsi.

Tsiku lina, aphunzitsiwo anaitana Irena kuti apite kutsogolo. Iwo ananyamula buku lija m’manja mwawo ndipo anamuuza kuti: “Lero uphunzitse ndi iweyo. Ndasankha mutu woti uwerenge ndipo ndikufuna kuti ufotokoze mmene banja lanu limagwiritsira ntchito mfundo zimene zafotokozedwa m’mutuwo.” Mutu umene aphunzitsiwo anasankha unali wakuti, “Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera ‘Kulemekeza Atate Ŵanga ndi Amayi Ŵanga’?”

Pamene Irena ankapita kutsogoloko, ana ena m’kalasimo anayamba kunena kuti makolo ake anali osiyana kwambiri ndi makolo ena. Aphunzitsi aja atamva zimenezi, anawafunsa kuti: “Kodi mukudziwa zimene zimachititsa kuti banja lawo likhale losiyana ndi mabanja ena? N’chifukwa chakuti akuphunzira Baibulo. Ine ndaphunzitsapo achimwene ake angapo, ndipo pa zaka zonse zimene ndakhala ndili mphunzitsi, sindinaonepo ana a khalidwe labwino ndiponso aulemu ngati amenewa.”

Kenako aphunzitsiwo anapempha Irena kuti ayambe kuwerenga. Irena atawerenga ndime imene imafotokoza kuti Mulungu anapatsa makolo udindo wokhazikitsa malamulo m’banja, aphunzitsiwo anamufunsa kuti: “Irena, kodi m’banja mwanu mumatsatira bwanji zimenezi? Kodi mumaona kuti muyenera kumvera chilichonse chimene makolo anu akukuuzani?”

Irena anafotokoza kuti: “Aliyense m’banja mwathu akhoza kukhala ndi maganizo ake pa nkhani inayake. Koma Baibulo limanena kuti ana ayenera kulemekeza makolo awo ndi kuwagonjera, ndipo n’zimene timachita. Komabe, timakambirana limodzi nkhanizo, ndipo aliyense wa ife amakhala ndi mpata wofotokoza maganizo ake.” Pamapeto pa phunzirolo, aliyense anakhutira ndi zimene Irena anafotokoza.

Mukhoza kuitanitsa bukuli polemba adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.