Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chiyani Chimayambitsa Kusungulumwa?

Kodi N’chiyani Chimayambitsa Kusungulumwa?

Kodi N’chiyani Chimayambitsa Kusungulumwa?

KUSUNGULUMWA n’kosiyana ndi kukhala wekhawekha. Buku lina lotanthauzira mawu linanena kuti, kusungulumwa kumatanthauza “kukhala wosakondwa chifukwa chosowa munthu wocheza naye.” Mosiyana ndi zimenezi, munthu amatha kuchita kusankha kuti akhale yekha.

Nthawi zina munthu angakonde kukhala yekha. Ambiri amafuna kukhala okha kuti apemphere kapena kuti aganizire mozama nkhani inayake, ngati mmene ankachitira Yesu Khristu. (Mateyo 14:13; Luka 4:42; 5:16; 6:12) Koma mosiyana ndi kukhala wekha, kusungulumwa n’kopweteka. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingayambitse kusungulumwa?

Kukhala M’mizinda Ikuluikulu

M’mizinda ikuluikulu anthu ambirimbiri amakhala m’dera limodzi mothithikana. Komabe n’zodabwitsa kuti anthuwa amakhala osungulumwa. Izi zili choncho chifukwa chakuti anthu ambiri amatanganidwa kwambiri ndipo zimenezi zimachititsa kuti asamacheze komanso asadziwane n’komwe ndi anthu amene akukhala nawo pafupi. Iwo amangoonana ngati alendo. Komanso anthu amenewa sakhulupirirana ndiponso safuna kuti anthu ena adziwe zimene iwowo akuchita.

Kusaganizirana Pantchito

Chifukwa cha mmene makampani ndi mabizinezi ena akuluakulu amayendetsera zinthu, anthu ambiri ogwira ntchito, kaya akhale mabwana kapena anthu wamba, amakhala osungulumwa. Izi zili choncho chifukwa chakuti anthuwa amadziona kuti ndi osafunika ndiponso amakhala opanikizika nthawi zonse.

Komanso makampani ambiri amakonda kusamutsasamutsa anthu awo ndipo zimenezi zimachititsa kuti iwo azikhala ndi nkhawa ndiponso azisowa ocheza nawo. Magazini ina inafotokoza kuti ku France, anthu ambiri ogwira ntchito m’makampani akuluakulu amadzipha. Magaziniyi inati anthuwa amaona kuti “chifukwa cha kusayenda bwino kwa chuma, akugwira ntchito mopanikizika kwambiri.”—International Herald Tribune.

Anthu Ambiri Sakulankhulana Pamasom’pamaso

Pulofesa Tetsuro Saito wa ku Japan, anati: “N’zodziwikiratu kuti kutsogoloku, anthu azilephera kulankhulana pamasom’pamaso chifukwa chogwiritsa ntchito kwambiri mafoni am’manja ndi zipangizo zina zolankhulirana.” Nyuzipepala ina inanena kuti ku Australia, “zipangizo zamakono . . . zikuchititsa kuti anthu asamakhudzidwe ndi zimene zikuchitikira anthu ena. Anthu akungolemberana mauthenga apakompyuta kapena apafoni m’malo molankhulana pamasom’pamaso.”—The Sunday Telegraph.

Mtsikana wina wa zaka 21 amene amakhala ku France, dzina lake Rachel, ananena kuti nthawi zambiri amakhala wosungulumwa. Iye anafotokoza kuti: “Anthu amachita ulesi kuti abwere kudzakuona chifukwa amaganiza kuti akhoza kungokutumizira uthenga pa foni, pa kompyuta, kapena kucheza nawe pa Intaneti. Koma zimenezi zimangokuchititsa kuti ukhale wosungulumwa kwambiri.”

Kusamukasamuka

Mavuto azachuma achititsa kuti anthu ambiri aziganiza zosamuka n’cholinga choti akafufuze ntchito ina kapena apite kwina n’kukapitiriza kugwira ntchito yawo yomweyo. Koma munthu akasamuka amasiyana ndi anthu am’dera lake komanso anzake. Amathanso kusiyana ndi anthu a kusukulu kwake kapena anthu ena a m’banja mwake. Anthu amene asamukawa amadziona ngati mtengo umene wazulidwa n’kukabzalidwa malo ena koma mizu yake yatsala m’mbuyo.

Francis amakumbukira bwino tsiku limene anafika ku France kuchokera ku Ghana. Iye anati: “Ndinali wosungulumwa kwambiri chifukwa chakuti anthu ankalankhula chinenero chimene ine sindinkamva, ndinalibe anzanga, komanso kunali kozizira kwambiri.”

Behjat nayenso anafotokoza mmene anamvera atangosamukira kumene ku England. Anati: “Zinkandivuta kwambiri kuti ndizolowere chikhalidwe china. Ndinadziwana ndi anthu angapo, koma ndinalibe anzanga apamtima kapena achibale oti ndingamakambirane nawo zinthu zofunika kapena kuwaululira zakukhosi kwanga.”

Imfa ya Wokondedwa Wathu

Mwamuna kapena mkazi akamwalira, wotsalayo amakhala wosungulumwa kwambiri. Zimenezi zimachitikira makamaka anthu amene akhala akudwazika mwamuna kapena mkazi wawoyo kwa nthawi yaitali. Wodwalayo akamwalira, munthu wotsalayo amasoweratu chochita.

Mkazi wina wamasiye amene amakhala ku Paris, dzina lake Fernande, anati: “Chimene chimandipweteka kwambiri n’chakuti sindingathenso kuululira zakukhosi mwamuna wanga, yemwe anali mnzanga wapamtima.” Nayenso Anny anafotokoza kuti amamusowa kwambiri mwamuna wake “makamaka pamene akufuna kusankha zochita pa nkhani zofunika, monga zokhudza thanzi lake.”

Kutha kwa Ukwati, Kupatukana, Kusowa Womanga Naye Banja

Ukwati ukatha kapena anthu akapatukana, amasungulumwa kwambiri ndiponso amadziona ngati olephera. Poyamba anthu ankaganiza kuti ana savutika banja la makolo awo likatha, koma panopa azindikira kuti ana ndi amenenso amavutika kwambiri. Akatswiri ena akuti ana ambiri amene makolo awo anasiyana, amadzakhala anthu osungulumwa akakula.

Komanso anthu amene sakupeza munthu woyenerera woti n’kumanga naye banja, nthawi zambiri amakhala osungulumwa. Iwo amakhumudwa kwambiri anthu akamawafunsa mafunso opanda nzeru, monga akuti, “Bwanji osapeza banja kuti muzisangalala?”

Nawonso makolo amene akulera okha ana amasungulumwa kwambiri. Pali zinthu zambiri zimene makolo amasangalala nazo, koma amakumananso ndi mavuto ambiri. Makolo amene akulera okha ana amalimbana okha ndi mavutowo.

Ukalamba Ndiponso Unyamata

Nthawi zambiri anthu okalamba amakhala osungulumwa, ngakhale pamene akusamalidwa bwino ndi anthu a m’banja mwawo. Achibale kapena anzawo amatha kubwera kudzawaona nthawi ndi nthawi, koma masiku amene sikunabwere aliyense, iwo amakhala osungulumwa kwambiri.

Nawonso achinyamata amakhala osungulumwa. Chifukwa cha kusungulumwa, ambiri amakonda kuonera TV, kuchita masewera apakompyuta, kapena kuchita zinthu zina nthawi yaitali pakompyuta ali okhaokha.

Mavutowa akukulirakulira. Kodi pali njira yowathetsera? Nanga munthu angatani kuti asamakhale wosungulumwa kwambiri?

[Mawu Otsindika patsamba 5]

“Ndinkasungulumwa kwambiri chifukwa chakuti anthu ankalankhula chinenero chimene sindinkamva, ndinalibe anzanga, komanso kunali kozizira kwambiri”