Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhala Wokhumudwa?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhala Wokhumudwa?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhala Wokhumudwa?

“Munthu aliyense zikamusokonekera, ndimayesetsa kum’thandiza kuti ayambenso kusangalala. Koma kenako ndimapita kunyumba n’kukadzitsekera m’chipinda mwanga n’kuyamba kulira, ngakhale kuti anthu ambiri sadziwa kuti ndimachita zimenezi.”—Anatero Kellie. *

“Ndikakhumudwa ndimakonda kukhala ndekha. Anthu ena akandiitana kuti tipite kwinakwake, ndimayesetsa kupeza chifukwa chokanira. Komanso ndimaonetsetsa kuti anthu a m’banja mwathu asadziwe kuti ndakhumudwa. Iwo amangoganiza kuti ndili bwinobwino.”—Anatero Rick.

KODI munayamba mwakhalapo ndi maganizo ofanana ndi a Kellie kapena Rick? Ngati ndi choncho, musafulumire kuganiza kuti muli ndi vuto. Zoona zake n’zakuti aliyense amakhumudwa nthawi zina. Ngakhale amuna ndi akazi ena okhulupirika otchulidwa m’Baibulo ankakhumudwa.

Nthawi zina mungadziwe chimene chakuchititsani kuti mukhale wokhumudwa, koma nthawi zina simungachidziwe. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Anna, anati: “Nthawi zina zinthu zimene zimakukhumudwitsa zimakhala zazing’ono. Munthu akhoza kukhumudwa nthawi ina iliyonse ngakhale pamene alibe mavuto alionse. N’zovuta kumvetsa koma zimachitika.”

Kaya mukudziwa chimene chayambitsa vuto lanu kapena ayi, kodi mungatani ngati mumangokhala wokhumudwa?

Mfundo yoyamba: Uzani munthu wina. Baibulo limati: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo m’bale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.”—Miyambo 17:17.

Kellie: “Ndikauza munthu wina vuto langa, ndimapepukidwa kwambiri chifukwa ndimaona kuti tsopano winawake akumvetsa zimene zikundichitikira. Ndimaona ngati ndinali m’dzenje lakuya ndipo wina wandiponyera chingwe n’kunditulutsamo.”

Yesani izi: Lembani m’munsimu dzina la “bwenzi” limene mungaliuze zakukhosi kwanu mukakhumudwa kwambiri.

․․․․․

Mfundo yachiwiri: Lembani mmene mukumvera. Ngati nthawi zambiri mumakhala wokhumudwa, mwina mungachite bwino kulemba mmene mukumvera. M’masalimo ena, Davide analemba zinthu zina zosonyeza kuti pa nthawiyo anali wokhumudwa kwambiri. (Salmo 6:6) Kulemba zimenezi kungakuthandizeni ‘kusunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira.’—Miyambo 3:21.

Heather: “Kulemba mmene ndikumvera kumandithandiza kuti ndimvetse bwinobwino zimene zikundichitikira. Ukalemba mmene ukumvera n’kudziwa zimene zikuchititsa kuti uzimva choncho, umapepukidwa.”

Yesani izi: Ena amalemba m’buku zimene zikuwachitikira tsiku lililonse. Ngati mutakhala ndi buku lotereli, kodi mungalembemo zotani? Mukakhumudwa, muzilemba mmene mukumvera komanso zimene mukuganiza kuti zikuchititsa kuti mukhumudwe. Pakatha mwezi, werenganinso zimene munalemba kuti muone ngati mmene mukumvera panopa zikusiyana ndi mmene munkamvera pa nthawiyo. Ngati pali kusintha, lembani zimene zakuthandizani.

Mfundo yachitatu: Muzipemphera. Baibulo limanena kuti mukauza Mulungu nkhawa zanu, “mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afilipi 4:7.

Esther: “Ndinkayesetsa kufufuza zinthu zimene zinkachititsa kuti ndizikhumudwa, koma sindinapeze chilichonse. Kenako ndinapempha Yehova kuti andithandize kukhala wosangalala chifukwa ndinali nditatopa n’kumangokhala wokhumudwa popanda chifukwa chilichonse. Pemphero ndi limene linandithandiza. Musamanyalanyaze kupemphera chifukwa pemphero ndi lamphamvu.”

Yesani izi: Gwiritsani ntchito Salmo 139:23, 24 monga chitsanzo cha mmene mungapempherere kwa Yehova. Muuzeni zakukhosi kwanu ndipo m’pempheni kuti akuthandizeni kudziwa zimene zimachititsa kuti muzikhumudwa.

Kuwonjezera pa mfundo zili pamwambazi, mukhozanso kupeza mfundo zina zothandiza m’Mawu a Mulungu. (Salmo 119:105) Kuwerenga nkhani zolimbikitsa zopezeka m’Baibulo kungakuthandizeni kuti muziganizira zinthu zolimbikitsa, muzikhala wosangalala komanso kuti muzichita zinthu zabwino. (Salmo 1:1-3) Nkhani zosangalatsa ndiponso zolimbikitsa zopezeka m’buku la Machitidwe zingakuthandizeninso kwambiri. Mfundo zina zimene zingakuthandizeni kuti muzilimbikitsidwa mukawerenga Baibulo mungazipeze powerenga Zitsanzo Zabwino 9 m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Zina mwa zitsanzo zimenezi ndi Yosefe, Hezekiya, Lidiya ndi Davide. Patsamba 227, mungaone zimene mtumwi Paulo anachita kuti athane ndi maganizo okhumudwitsa amene ankakhala nawo nthawi zina chifukwa cha kupanda ungwiro.

Koma bwanji ngati mukupitirizabe kukhala wokhumudwa pambuyo poyesetsa kuchita zonsezi?

Ngati Mukupitirizabe Kukhala Wokhumudwa

Ryan anati: “Nthawi zina kukacha m’mawa ndimaganiza zongogonabe chifukwa ndimaopa kuti ndikadzuka ndikumana ndi zinthu zinanso zokhumudwitsa.” Ryan amadwala matenda ovutika maganizo. Pali achinyamata ambiri amene amadwalanso matenda amenewa ndipo kafukufuku wasonyeza kuti wachinyamata mmodzi pa achinyamata anayi alionse amadwala matenda ovutika maganizo pa nthawi inayake pa moyo wake.

Kodi mungadziwe bwanji ngati mukudwala matenda ovutika maganizo? Zizindikiro zina ndi monga izi: Kusinthasintha, pena kukhala wosangalala kwambiri ndipo penanso wokhumudwa kwambiri; kusafuna kucheza ndi anthu; kusafuna kuchita chinthu chilichonse; kusintha kadyedwe ndi kagonedwe; kumangoganizira kuti ndiwe munthu wosafunika kapena kumangodziimba mlandu pa zinthu zoti sunalakwe.

N’zoona kuti pafupifupi aliyense nthawi zina amatha kusonyeza chizindikiro chimodzi kapena zingapo mwa zizindikiro zimenezi. Komabe ngati mupitirizabe kusonyeza zizindikiro zimenezi kwa milungu ingapo, mungachite bwino kupempha makolo anu kuti mukaonane ndi dokotala. Dokotala angakuthandizeni kudziwa ngati mukudwala matenda ovutika maganizo, kapena ayi. *

Ngati mukudwala matenda ovutika maganizo, palibe chifukwa chochitira manyazi. Anthu ambiri akapatsidwa mankhwala kuchipatala amayamba kupeza bwino, mwina kuposa mmene akhala akumvera m’mbuyo monsemu. Choncho, kaya mumakhala wokhumudwa chifukwa chakuti muli ndi matenda ovutika maganizo kapena pa zifukwa zina, muziganizira mawu otonthoza amene amapezeka pa Salmo 34:18. Lembali limati: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.”

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha maina ena m’nkhani ino.

^ ndime 23 Achinyamata ena akamangokhala okhumudwa, amaganiza zongodzipha. Ngati mwaganizapo zodzipha, uzani mwamsanga munthu wachikulire amene mumamudalira.—Onani Galamukani! ya May 2008, masamba 26 mpaka 28.

ZOTI MUGANIZIRE

Kodi kulira kumathandizadi?

“Ine sindilira chisawawa, koma ndimaona kuti kulira kumandithandiza ndikakhumudwa kwambiri. Ndikalira, ndimayamba kuganizanso bwinobwino ndipo ndimakhalanso ndi chiyembekezo chakuti zinthu ziyamba kuyenda bwino.”—Anatero Leanne.

Kodi ena angakuthandizeni bwanji ngati mwakhumudwa?

“Ndikakhumudwa, ndimayesetsa kuti ndisakhale ndekhandekha. N’zoona kuti nthawi zina ndimafunika kukhala ndekha kuti ndiganizire mmene ndingathetsere vuto langa, komanso mwina kuti ndilire. Koma pambuyo pa zimenezi, ndimaona kuti ndikufunika kukhala ndi anthu ena n’cholinga choti ndiiwale zimene zandikhumudwitsazo.”—Anatero Christine.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 21]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

“Nthawi zambiri ndimakhala wokhumudwa ndikamaganizira kwambiri za ineyo. Koma ndikamathandiza anthu ena, ndimasiya kuganizira za ineyo ndipo zimenezi zimandithandiza kuti ndiyambirenso kusangalala.”

“Ndikamachita masewera olimbitsa thupi pafupipafupi, sindikhala wokhumudwa nthawi zambiri chifukwa ndimayamba kusangalala ndi mmene ndilili. Ndiponso ndikamaliza kuchita masewerawo, ndimakhala nditatopa kwambiri moti sindikhalanso ndi mphamvu zoganizira zinthu zokhumudwitsa.”

[Zithunzi]

Drenelle

Rebekah

[Chithunzi patsamba 22]

Munthu amene amangokhala wokhumudwa amakhala ngati ali m’dzenje lakuya. Koma atachita khama komanso anthu ena atamuthandiza, angatulukemo