Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Madalitso Oposa Chuma (March 2009) Munkhaniyi munagwira mawu a Kostas, akuti: “Mulungu safuna kuti tizidzikundikira chuma chambiri.” Ine ndimaganiza kuti Yehova sanaike malire pa kuchuluka kapena kuchepa kwa chuma chimene mtumiki wake angakhale nacho, malinga ngati munthuyo akuika Mulungu patsogolo. Kodi n’kulakwa kukhala ndi chuma n’kumatumikira Yehova mokhulupirika?

J. D., United States

Yankho la “Galamukani!”: Baibulo silinena kuti kukhala ndi chuma n’kulakwa. Ndipo atumiki ambiri a Mulungu akale anali olemera. (Genesis 25:5; 26:12-16; Yobu 1:1-3) Komabe, anthu amene ali ndi chuma afunika kukumbukira kuti ‘kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pamoyo wake, sikuchokera kwa Atate, koma ku dziko.’ (1 Yohane 2:16) Komanso mtumwi Paulo anati: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.” Iye anafotokoza kuti chifukwa chonyalanyaza zinthu zauzimu pofunafuna chuma, “ena asocheretsedwa kuchoka pa chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pa thupi pawo.” (1 Timoteyo 6:10) Komabe, Mawu a Mulungu sanena kuti anthu olemera ayenera kudziimba mlandu chifukwa chakuti ali ndi chuma chambiri kuposa ena. Akhristu amalimbikitsidwa kukhala “owolowa manja, okonzeka kugawana ndi ena,” kaya akhale ndi zambiri kapena zochepa.—1 Timoteyo 6:18.

Salankhula Koma Timamvana (October 2008) Ndinalimbikitsidwa kwambiri nditawerenga nkhani imeneyi, imene ikunena za Hillary, amene amadwala matenda otchedwa Rett. Mdzukulu wanga wa zaka zisanu satha kuona, kumva, kuyenda, kulankhula, kapena kukhala pansi. Ndimamuimbira nyimbo, kumuwerengera, kumulankhula, ndi kumusisita, ndipo ndili ndi chikhulupiriro kuti zimenezi zimamukhudza mwanjira inayake. Ndinalira nditawerenga mawu a amayi ake a Hillary akuti: “Ngakhale kuti sindimva zimene akunena, Yehova amamva.” Mawuwa anandithandiza kuzindikira kuti ngakhale kuti mdzukulu wangayu sangathe kulankhula, Yehova amamva mawu amene amanena mumtima mwake.

M. A., Japan

Mwana wanga wamkazi ali ndi zaka 43, koma nkhaniyi inali yoyamba kufotokoza bwinobwino matenda ake ndiponso zimene zinachititsa kuti alumale. Ndinamvera chisoni kwambiri Hillary, mayi ake, ndiponso mchemwali wake. Ngakhale kuti kumene ndikukhala n’kutali kwambiri ndi kumene iwowo amakhala, ndikutha kumvetsa mavuto awo ndipo ndikuwayamikira kwambiri chifukwa cha chikhulupiriro chawo, chikondi chawo, ndi kupirira kwawo.

T. Y., Ghana

Kuchotsa Mimba Si Njira Yabwino (June 2009) Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani zimene munalemba zokhudza kuchotsa mimba. Pamene ndinali ndi zaka za m’ma 20, ndinachotsa mimba, ndipo ndimadandaula kwambiri mpaka lero chifukwa cha zimene ndinachitazi. Ndikanakhala kuti panopa sindikudziwa choonadi, bwenzi ndilibe chiyembekezo chilichonse. Ndimayamikira kwambiri kuti ndili ndi chiyembekezo ndiponso chifukwa chodziwa kuti Yehova amakhululuka.

Sitinalembe dala dzina lake, United States

Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Kodi Ndingatani Ngati Mayi Kapena Bambo Anga Amwalira? (August 2009) Panopa ndili ndi zaka 22 zokha, ndipo bambo anga anamwalira mofulumira komanso mosayembekezereka moti zinandisokoneza kwambiri. Monga momwe nkhaniyi inafotokozera, n’zomvetsa chisoni kuti iwo sadzakhalapo pa zochitika zofunika kwambiri pa moyo wanga. Ngakhale kuti papita zaka zitatu tsopano, zikuvutabe kuti moyo wanga ubwererenso mwakale. Komabe nkhaniyi inanditonthoza kwambiri. Mfundo zimene inafotokoza zinandithandiza kwambiri, ngakhale kuti poyamba zinali zovuta kuzitsatira. Pitirizani ntchito yabwino imene mukuchita.

N. P., France