Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Amene Mungawakhulupirire

Anthu Amene Mungawakhulupirire

Anthu Amene Mungawakhulupirire

Santiago amakhala ku Argentina ndipo ali ndi galimoto yaing’ono imene amachitira bizinezi yonyamula anthu. Tsiku lina munthu wina anaiwala chikwama m’galimoto yakeyo. Santiago ataona chikwamacho, nthawi yomweyo anadziwa kuti akuyenera kukachibweza kwa mwiniwake, ndipo anakachibwezadi. Zimene anachitazi zinali zachilendo chifukwa m’chikwamamo munali ndalama zambiri, zoposa madola 32,000.

TAGANIZIRANI mmene zinthu zikanakhalira ngati anthu onse padzikoli akanakhala okhulupirika. Moyo ukanakhala wosiyana kwambiri ndi mmene ulili panopa. Bwenzi mukusiyira mwana wanu munthu wina kuti azimuyang’anira popanda kuopa chilichonse. Komanso sibwenzi mukufunikira kukiya zitseko za nyumba yanu. Kodi alipo anthu amene mungawakhulupirire chonchi?

Phindu Lotsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino

Mtumwi Paulo, ponena za iyeyo ndi Akhristu anzake, anati: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) Izi n’zimene Mboni za Yehova zimayesetsa kuchita. Zimayesetsa kutsatira mfundo zimene zafotokozedwa m’Baibulo pa Yesaya 33:15. Lembali limati: “Pali munthu amene amayenda m’chilungamo nthawi zonse, amene amalankhula zowongoka, amene amakana kupeza phindu mwachinyengo, amene salola kuti manja ake alandire chiphuphu.” Anthu ena akuyesetsa kutsatira mfundo zimenezi. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

‘Kulankhula zowongoka.’ Domingo, yemwe ndi wa Mboni za Yehova, amagwira ntchito pa famu inayake ya kokonati m’dziko la Philippines. Iye anati: “Anthu ambiri sauza mabwana awo chilungamo. Mwachitsanzo, akakolola kokonati, amauza bwana wawo nambala yabodza ya matumba amene akolola. Amachita zimenezi kuti agulitse matumba enawo.”

Domingo ndi banja lake anatsala pang’ono kuthamangitsidwa pa famu inayake chifukwa chakuti ankakana kunena nambala yabodza ya matumba a kokonati amene akolola. Domingo anati: “Tinauza bwana wathu kuti ngakhale atatiopseza kuti atichotsa ntchito, sitinganame. Pamapeto pake bwana wathuyo ananena kuti Mboni za Yehova ndi anthu abwino amene munthu ungawakhulupirire, ndipo anatipatsa malo ena owonjezera kuti tizilimapo.”

‘Kukana kupeza phindu mwachinyengo.’ Pierre, yemwe ndi mkulu woyang’anira za misonkho m’chigawo china cha dziko la Cameroon, wakhala akupeza mipata yambirimbiri yopezera ndalama mwachinyengo. Pa nthawi ina atapatsidwa ntchito yoti azilipira ndalama anthu aganyu, anaona kuti zinazake sizinali bwino. Iye anati: “Ndalama za anthu oti ntchito yawo inatha kapena anamwalira zinkabwerabe. M’malo moganiza zotenga ndalamazo, ndinkalemba bwinobwino mayina a anthu onse oterowo n’kusunga ndalama zawozo pamalo otetezeka kwambiri.”

Kodi kenako chinachitika n’chiyani? Pierre anati: “Patatha zaka ziwiri, kunabwera anthu odzafufuza mmene ndalama za malipiro a anthu zakhala zikuyendera. Ndinamva bwino kwambiri pamene ndinkawapatsa mayina onse a anthu amene ndinkalemba aja limodzi ndi ndalama zawo, zimene pa nthawiyi zinali zitachuluka kwambiri. Anthu odzafufuza za ndalamawo anandiyamikira kwambiri chifukwa chochita zinthu mwachilungamo.”

● ‘Kupewa kulandira ziphuphu.’ Ricardo ndi loya ndipo amagwira ntchito mumzinda wa Rio de Janeiro, ku Brazil. Ntchito yake ndi yochitira umboni zikalata zosiyanasiyana zikamasainidwa. Pa zaka zimene wakhala akugwira ntchito imeneyi, anthu ambiri ayeserapo kumupatsa ziphuphu kuti awathandize. Iye anati: “Pa nthawi ina, loya wina anayesera kundipatsa chiphuphu. Iye anatumiza wailesi ya ma CD kunyumba kwanga ine ndisakudziwa. Masiku amenewo, mawailesi oterewa anali atangobwera kumene ndipo ankaoneka apamwamba kwambiri.”

Kodi Ricardo anachita chiyani? Iye anati: “Ine ndi mkazi wanga tinagwirizana kuti tisatsegule n’komwe mphatsoyo. Ndinapita ku ofesi ya loyayo, ndipo ndinakaika mphatsoyo pa desiki pake. Iye anadabwa kwambiri chifukwa si zimene ankayembekezera. Ndinapezerapo mwayi womufotokozera zifukwa zimene ndinabwezera katundu wakeyo. Sekilitale wake anachita chidwi kwambiri ndi zimene ndinachitazi.”

Ngakhale kuti anthu a Mboni za Yehova si okhawo amene amayesetsa kuchita zinthu zachilungamo, gulu lawo limadziwika kuti ndi la anthu okhulupirika. Zimenezi n’zimene zinachititsa kampani inayake ya ku Poland imene ili ndi masitolo ogulitsa zovala kuti izilemba ntchito anthu a Mboni za Yehova okhaokha. Bwana wina wamkulu wa kampaniyi anati: “N’zoona kuti kulikonse mukhoza kupezako anthu achilungamo, koma Mboni za Yehova zili ndi mfundo zabwino zimene zimakhulupirira, ndipo zimayesetsa kutsatira mfundo zimenezi.”

N’zotheka Munthu Wosauka Kukhala Wokhulupirika

Anthu ambiri amaona kuti n’zovuta kuti munthu wosauka azichita zinthu mwachilungamo. Mwachitsanzo, tchanelo cha TV cha CNN chinaulutsa nkhani inayake yokhudza mnyamata wina wa zaka 14 wa ku Nigeria. Mnyamatayu ntchito yake ndi kubera anthu ndalama pa Intaneti. Atamufunsa chifukwa chimene amachitira zimenezi, mnyamatayo anayankha kuti: “Kodi mukufuna kuti ndizitani? Ndimadyetsa mchemwali wanga, mayi anga, ndi bambo anga. Munthu akavutika amalolera kuchita chilichonse.”

Baibulo sililonjeza kuti anthu ochita zachilungamo adzalemera, koma limawatsimikizira kuti adzapeza zimene amafunikira tsiku lililonse. Lemba la Yesaya 33:16 limati: “Iye adzapatsidwa chakudya ndipo madzi ake sadzatha.”

Komabe, anthu ena angafunse kuti: ‘Kodi kuchita zinthu zachilungamo kungathandize bwanji anthu amene ali pa umphawi wadzaoneni? Mwachitsanzo, kungathandize bwanji anthu amene amalephera ngakhale kupeza chakudya cha tsiku ndi tsiku?’

Taganizirani za Berthe, mkazi wamasiye wa ku Cameroon amene amagulitsa mumsika zakudya zinazake zopangidwa kuchokera ku chinangwa, zomwe amazipanga ngati timitengo. Berthe anati: “M’paketi iliyonse mumayenera kukhala timitengo 20. Anthu ambiri amaikamo timitengo 17 kapena 18, koma ineyo ndimaika tokwanira chifukwa sindifuna kubera anthu.”

Kodi bizinezi ya Berthe ikuyenda? Masiku ena siyenda bwino. Iye anati: “Nthawi zina ndimatha tsiku lonse osagulitsa kanthu. Zikatero, ndimauza anthu ogulitsa zakudya kuti andikongoze chakudya chifukwa sindinagulitse kalikonse. Iwo amandikongozadi chifukwa amadziwa kuti ndikangopeza ndalama ndibweza ngongoleyo. Amachita zimenezi chifukwa amandikhulupirira, koma zimatenga nthawi kuti anthu afike pomukhulupirira munthu.”

Mulungu ndi Woyenera Kumukhulupirira

Tikaona kuti munthu amachita zimene amalonjeza, timamukhulupirira kwambiri. Yoswa, amene anali mtsogoleri wa Aisiraeli, ponena za Mulungu anati: “Palibe lonjezo ngakhale limodzi limene silinakwaniritsidwe, pa malonjezo onse abwino amene Yehova analonjeza . . . Onse anakwaniritsidwa.” (Yoswa 21:45) Kodi nafenso Mulungu watichitira zinthu zimene zingatipangitse kumukhulupirira?

Malonjezo a Mulungu ndi odalirika kwambiri moti amawayerekezera ndi mvula. (Yesaya 55:10, 11) Kodi pali chimene chingalepheretse mvula kugwa, kunyowetsa nthaka komanso kumeretsa mbewu? Palibe. Mofanana ndi zimenezi, palibe chimene chingalepheretse malonjezo a Mulungu kukwaniritsidwa.

Limodzi la malonjezo amenewo limapezeka pa 2 Petulo 3:13. Lembali limati: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” Mulungu ali ndi cholinga chodzawononga anthu onse amene amachitira anzawo zinthu zopanda chilungamo. Kodi mungakonde kudziwa zambiri zokhudza momwe Mulungu adzakwaniritsire cholinga chimenechi? Ngati mungakonde, funsani Mboni za Yehova zakwanuko, kapena lembani kalata n’kuitumiza ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]

PHINDU LOCHITA ZINTHU MWACHILUNGAMO

Lucio, yemwe ndi wa Mboni za Yehova ndipo amakhala ku Philippines, akanatha kuchita zachinyengo. Iye anapeza ndalama zokwana madola 27,500 m’kabati inayake yakale, mu ofesi ya bwana wake imene anauzidwa kuti aikonze. Ndalamazo zinali za bwana wakeyo, ndipo pa nthawiyi anali atapita kwinakwake kukagwira ntchito ya kampani. Lucio anati: “Ndinali ndisanaonepo n’komwe ndalama ya dola.”

Bwana wake atabwera, Lucio anamupatsa ndalamazo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Lucio anati: “Bwanayo anandikweza pa ntchito. Komanso anandipatsa chipinda choti ndizikhalamo ndi banja langa lonse. Ngakhale kuti moyo ndi wovuta kwambiri ku Philippines, ndikuona kuti Yehova Mulungu akutisamalira chifukwa chomvera malamulo ake.”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

SIKELO YOSABERA ANTHU

Moïse amagulitsa nsomba mumsika winawake ku Douala, m’dziko la Cameroon, ndipo anthu ambiri amawadziwa malo ake ogulitsira nsomba. Iye anati: “Malo anga ogulitsira malonda ndinawapatsa dzina lakuti ‘Sikelo’ chifukwa sikelo zanga ndi zina mwa sikelo zochepa kwambiri mumsikawu zosabera anthu. Ndikudziwa kuti anthu amandiyesa nthawi ndi nthawi. Akandiuza kuti akufuna kilo imodzi ya nsomba, ndimawapatsadi kilo imodzi. Koma akapita kwina n’kukayezanso nsombazo, pa masikelo enawo amapeza kuti zikupitirira kilo imodzi. Akatero, amadziwa kuti sindinawabere. Anthu ambiri amandiuza kuti, ‘Timabwera kwa inu chifukwa ndinu achilungamo.’”

[Chithunzi patsamba 7]

“Tinauza bwana wathu kuti ngakhale atatiopseza kuti atichotsa ntchito, sitinganame.”—Domingo, wa ku Philippines.

[Chithunzi patsamba 7]

“Anthu odzafufuza za ndalamawo anandiyamikira kwambiri chifukwa chochita zinthu mwachilungamo.”—Pierre, wa ku Cameroon.

[Chithunzi patsamba 7]

“Loya wina anayesera kundipatsa chiphuphu. . . . Ine ndi mkazi wanga tinagwirizana kuti tisatsegule n’komwe mphatsoyo.”—Ricardo, wa ku Brazil.

[Chithunzi patsamba 7]

Nthawi zambiri Berthe amakhala tsiku lonse osagulitsa kanthu. Koma anthu ena ogulitsa zakudya amamukongoza chakudya chifukwa amadziwa kuti akangopeza ndalama awabwezera.