Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kabuku Kothandiza Kwambiri kwa Ophunzira Baibulo

Kabuku Kothandiza Kwambiri kwa Ophunzira Baibulo

Kabuku Kothandiza Kwambiri kwa Ophunzira Baibulo

Kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma’ n’kothandizadi. Kabukuka kali ndi mapu komanso zithunzi zokongola zosonyeza malo amene kunachitikira zinthu zikuluzikulu zotchulidwa m’Baibulo, zomwe zinachitika pa zaka zoposa 2,000. Mulinso chithunzi chosonyeza mabwinja a mzinda wakale wa Beere-seba, kumene Abulahamu ankakhala. Komanso muli chithunzi cha msewu waukulu wa Aroma umene ophunzira a Khristu ayenera kuti ankadutsamo chakumapeto kwa zaka zapakati pa 100 ndi 200 C.E.

Anthu ambiri amene amawerenga mabuku athu anenapo kuti kabuku kameneka n’kothandiza kwambiri. Wina analemba kuti: “Ndikuchita kusowa mawu okuthokozerani. Ndakhala ndikulakalaka nditaona chithunzi cha malo amene Yesu anadutsa komanso malo amene anthu akale otchulidwa m’Baibulo ankakhala.” Winanso ananena kuti: “Ndakhala ndikufuna kabuku ngati kameneka kwa nthawi yaitali. Kamathandiza kuti Baibulo lizisangalatsa kuwerenga komanso uzilimvetsa.”

Mukhoza kuitanitsa kabuku ka masamba 36 kameneka polemba adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili patsamba 5 m’magazini ino. Kabukuka kakupezeka m’zinenero 79. Kuyambira pamene kabukuka kanatuluka, timabuku pafupifupi 10 miliyoni tasindikizidwa.

❑ Ndikupempha kuti munditumizire kabukuka.

❑ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.

[Chithunzi patsamba 32]

Beere-seba

[Chithunzi patsamba 32]

Msewu wa Aroma

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Beer-sheba, Roman road, and brochure cover: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.