Kodi Mulungu Ndi Mphamvu Chabe?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Mulungu Ndi Mphamvu Chabe?
ANTHU ambiri akaona zinthu zogometsa komanso zochititsa mantha za m’chilengedwe, amayamba kukhulupirira kuti kunjaku kuli Mulungu. Kodi inunso mumagoma mukaona zinthu zodabwitsa m’chilengedwe komanso mukaona mmene thupi la munthu linapangidwira mwanzeru kwambiri?
Ngati zinthu zam’chilengedwe zimakugometsani, ndiye kuti mwina mumakhulupirira kuti kuli Mulungu amene anapanga zimenezi. Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti Mulunguyo amakhala m’mapiri, m’mitengo, m’mlengalenga ndi m’malo ena. Ena amakhulupirira kuti mizimu ya makolo amene anafa, yabwino kapena yoipa, imaphatikizana n’kupanga mzimu wamphamvu kwambiri, wotchedwa Mulungu.
Zikhulupiriro zonsezi zimafanana pa mfundo imodzi yakuti Mulungu wangokhala mphamvu chabe ndipo alibe umunthu uliwonse. Anthu ena zimawavuta kukhulupirira kuti Mulungu amaganiza, amakhudzidwa ndi zinthu, amakhala ndi zolinga ndiponso ali ndi zinthu zimene amakonda. Kodi Mulungu ndi mphamvu chabe? Baibulo, lomwe ndi limodzi mwa mabuku opatulika akale kwambiri ndiponso limene anthu ambiri ali nalo masiku ano, limayankha funso limeneli momveka bwino.
Timadziwa Kuti Mulungu ndi Wotani Tikaona Mmene Tinapangidwira
Baibulo limanena kuti anthu analengedwa ndi makhalidwe ofanana ndi a Mulungu. Lemba la Genesis 1:27 limati: “Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake, m’chifaniziro cha Mulungu anam’lenga iye.”
N’zoonekeratu kuti mawuwa sakutanthauza kuti anthu oyambirira anali ofanana ndendende ndi Mulungu. Baibulo limatiphunzitsa kuti Mulungu ndi mzimu, pomwe anthufe tinalengedwa kuchokera ku fumbi. (Genesis 2:7; Yohane 4:24) Ngakhale kuti pali kusiyana koteroko pakati pa Mulungu ndi anthu, kudziwa bwino zimene anthu amachita kungatithandize kukhala ndi chithunzi cha mmene Mulungu alili.
Anthu amatha kusonyeza mphamvu m’njira zosiyanasiyana komanso kuganizira mofatsa zinthu zimene akufuna kuchita. Pochita zimenezi amasonyezanso makhalidwe monga kukoma mtima, kuganiza bwino, nzeru, ndiponso kukonda chilungamo. Anthu amathanso kusonyeza zimene zili mumtima mwawo monga chikondi, chidani, mkwiyo, ndi zina zotero. Koma amasonyeza makhalidwe amenewa mosiyanasiyana ndipo zimenezi n’zimene zimachititsa kuti munthu aliyense akhale wosiyana ndi mnzake.
Kodi zikanakhala zomveka kuti Mulungu alenge anthu mogometsa kwambiri ngati iye akanakhala mphamvu chabe yomwe imangoyendayenda kudziko lamizimu? Ngati anthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu, ndiye kuti anthuwo ayenera kufanana ndi Mulungu m’njira zambiri. Taganizirani mfundo zotsatirazi:
Mulungu ali ndi dzina. Pa Yesaya 42:8, Baibulo limati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” Mulungu amafuna kuti anthu adziwe dzina lake. Baibulo limanenanso kuti: “Dzina la Yehova lidalitsike, kuyambira tsopano mpaka kalekale. Kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera, dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.” (Salimo 113:2, 3) Choncho, atumiki a Mulungu amagwiritsa ntchito dzina lake chifukwa amakhulupirira kuti iye si mphamvu chabe.
Mulungu alibe wofanana naye. Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu alibe wofanana naye. (1 Akorinto 8:5, 6) Baibulo limati: “Ndinudi wokwezeka, inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. . . . Palibe Mulungu wina koma inu nokha.” (2 Samueli 7:22) Limafotokozanso kuti Yehova ndi “Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi. Palibenso wina.”—Deuteronomo 4:39.
Yehova Mulungu amadana ndi zoipa. Mphamvu chabe singathe kudana ndi chinthu. Choncho Mlengi wathu si mphamvu chabe chifukwa Baibulo limatiuza kuti iye amadana ndi zinthu monga “maso odzikweza, lilime lonama, manja okhetsa magazi a anthu osalakwa, mtima wokonzera ena ziwembu, mapazi othamangira kukachita zoipa, mboni yachinyengo yonena mabodza, ndi aliyense woyambitsa mikangano pakati pa abale.” (Miyambo 6:16-19) Apa tikuona kuti Mulungu amadana ndi makhalidwe amene amapweteketsa anthu ena. Tikuonanso kuti Mulungu amatisamalira chifukwa amadana ndi zinthu zimene zingatipweteketse.
Yehova ndi Mulungu wachikondi. Baibulo limafotokoza kuti Mulungu “anakonda kwambiri dziko.” (Yohane 3:16) Limasonyezanso kuti Mulungu ali ngati bambo wachikondi kwambiri amene amafunira zabwino ana ake. (Yesaya 64:8) Anthu akamaona kuti Mulungu ndi Atate wawo wachikondi, zinthu zimawayendera bwino kwambiri.
Mukhoza Kukhala Bwenzi la Mulungu
Taona kuti Baibulo limaphunzitsa kuti Mlengi si mphamvu chabe, chifukwa ali ndi dzina ndiponso umunthu. Amatha kusonyeza mphamvu zake m’njira zosiyanasiyana ndipo amayamba waganiza kaye asanachite zinthu. Pochita zimenezi amasonyezanso makhalidwe abwino monga kukoma mtima, nzeru ndi chilungamo. Iye sali kutali kwambiri ndi ife ndipo tikhoza kukhala naye pa ubwenzi. Iye ananena kuti: “Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”—Yesaya 41:13.
Mulungu analenga anthu ndi cholinga. Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Tikadziwa kuti Yehova ali ndi umunthu ndipo si wofanana ndi wina aliyense, zimakhala zosavuta kuti tikhale naye pa ubwenzi. Zikatero, timasangalala ndi madalitso amene iye amapereka kwa mabwenzi ake.—Deuteronomo 6:4, 5; 1 Petulo 5:6, 7.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
● Kodi Mulungu ali ndi dzina?—Yesaya 42:8.
● Kodi milungu ilipo yambirimbiri?—1 Akorinto 8:5, 6.
● Kodi n’zotheka kuti anthu akhale pa ubwenzi ndi Mulungu woona?—1 Petulo 5:6, 7.
[Chithunzi patsamba 29]
Kodi zikanatheka kuti Mulungu atilenge ifeyo mogometsa ngati mmene anatilengeramu ngati iyeyo ali mphamvu chabe?