Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingakwanitse Bwanji Zolinga Zanga?

Kodi Ndingakwanitse Bwanji Zolinga Zanga?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingakwanitse Bwanji Zolinga Zanga?

PA ZINTHU zili m’munsizi, ndi chiti chimene mungakonde kukhala nacho?

● Kukhala wolimba mtima

● Kukhala ndi anzanu ambiri

● Kukhala wosangalala

Zoona zake n’zakuti mukhoza kukhala ndi zitatu zonsezi. Koma kodi zingatheke bwanji? Chinsinsi chake chagona pa kukhala ndi zolinga ndi kuyesetsa kuzikwaniritsa. Taganizirani zinthu zili m’munsizi:

Kukhala wolimba mtima Munthu akakhala ndi zolinga zing’onozing’ono n’kuzikwaniritsa, amalimba mtima kuti akhozanso kukwaniritsa zolinga zikuluzikulu. Amalimbanso mtima kuti akhoza kuthana ndi mavuto amene amakumana nawo tsiku ndi tsiku monga kukakamizidwa ndi anzake kuti achite zinthu zoipa. Komanso anthu ena akaona kuti ndinu munthu wolimba mtima, amayamba kukulemekezani. Chifukwa cha zimenezi, ena angasiye kulimbana nanu kwambiri. Mwinanso akhoza kuyamba kusirira khalidwe lanu.—Yerekezerani ndi Mateyu 5:14-16.

Kukhala ndi anzanu ambiri Anthu amasangalala kucheza ndi anthu amene amakhala ndi zolinga pa moyo wawo komanso amene amayesetsa kuzikwaniritsa. Anthu akayamba kucheza nanu chifukwa choona kuti muli ndi zolinga, nthawi zambiri anthuwo amakuthandizani kuti mukwaniritse zolinga zanu.—Mlaliki 4:9, 10.

Kukhala wosangalala Kunena zoona, moyo sukoma ngati munthu akusowa chochita kapena ngati palibe chilichonse chimene chikumusangalatsa. Koma munthu akakhala ndi zolinga n’kuzikwaniritsa, amakhutira kuti wachita chinachake. N’chifukwa chake mtumwi Paulo anati: “Sikuti ndikungothamanga osadziwa kumene ndikulowera.” (1 Akorinto 9:26) Ndiponso musaiwale kuti mukakwaniritsa zolinga zikuluzikulu, m’pamenenso mumasangalala kwambiri.

Kodi mwaganizira zinthu zimene mungachite pa moyo wanu? Dulani ndi kupinda tsamba limene lili kumanjaku, ndipo tsatirani malangizo amene ali pomwepowo. *

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Malangizowo angakuthandizeni pa zolinga zimene mungazikwaniritse m’milungu kapena m’miyezi yochepa. Komabe, mfundo zake zingagwirenso ntchito pa zolinga zikuluzikulu.

ZOTI MUGANIZIRE

● Kodi n’zotheka kukhala ndi zolinga zambirimbiri nthawi imodzi?—Afilipi 1:10.

● Kodi kukhala ndi zolinga pa moyo wanu kumatanthauza kuti muzikonzeratu chimene mukufunika kuchita pa mphindi iliyonse?—Afilipi 4:5.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 25, 26]

Zimene mungachite kuti mukwanitse zolinga zanu

DZIWANI ZOLINGAZO Miyambo 4:25, 26 1

“Musamaope kukhala ndi zolinga zikuluzikulu. Ngati ena akwanitsapo, inunso mukhoza kukwanitsa.”—Anatero Roben.

1. Ganizirani zolinga zimene mungathe kukhala nazo. Popanga zimenezi, muzingokhala ngati mukusewera. Musavutike n’kuganiza kwambiri. Muzingolemba cholinga chilichonse chimene chakubwererani m’mutu. Lembani zinthu zimene mungakwanitse kuchita, mwina zokwana 10 kapena 20.

2. Ganizirani mofatsa cholinga chilichonse pachokha. Pa zolinga zimene mwalembazo, ndi chiti chimene mukuona kuti mungasangalale kwambiri kuchichita? Nanga chovuta kwambiri n’chiti? Kodi ndi chiti chimene mukuona kuti munganyadire kwambiri mutachikwaniritsa? Kumbukirani kuti zolinga zabwino kwambiri ndi zimene inuyo mumaona kuti ndi zofunika kwambiri.

3. Sankhani zofunika kwambiri. Choyamba, sankhani zolinga zimene mungazikwanitse m’masiku ochepa. Kenako sankhani zolinga zina zimene mungazikwanitse m’milungu kapena m’miyezi ingapo. Sanjani zolingazo, kuyambira ndi zimene mukufuna kuzikwanitsa mwamsanga.

Zitsanzo za Zolinga Zimene Mungakhale Nazo

Anzanga Ndipeze mnzanga mmodzi wamkulu kapena wamng’ono kwa ine. Ndiyambirenso kucheza ndi mnzanga amene ndinkacheza naye kale.

Moyo wathanzi Ndizichita masewera olimbitsa thupi kwa mphindi zosachepera 90 pa mlungu. Ndizigona maola osachepera 8 tsiku lililonse.

Sukulu Ndiyesetse kuti ndizikhoza masamu. Ndizikana anzanga akamandinyengerera kuti ndibere mayeso.

Moyo wauzimu Ndiziwerenga Baibulo kwa mphindi 15 tsiku lililonse. Mlungu uno ndiuzeko mnzanga mmodzi zimene ndimakhulupirira.

Ganizirani Mmene Mungazikwanitsire Miyambo 21:5 2

“Kukhala ndi zolinga n’kwabwino, koma umafunikanso kuganizira mmene ungazikwanitsire. Apo ayi, palibe chimene ungakwanitse.”—Anatero Derrick.

Pa cholinga chilichonse chimene mwasankha, chitani zotsatirazi:

1. Lembani cholinga chanu.

2. Ikani tsiku loti mudzakhale mutachikwaniritsa. N’zovuta kuti mukwaniritse cholinga chanu ngati simunaike nthawi yoti mudzakhale mutachikwaniritsa.

3. Ganizirani zimene mungachite kuti muchikwaniritse.

4. Ganizirani zinthu zimene zingakulepheretseni. Ndiyeno pezani njira zozithetsera.

5. Tsimikizani kuti mukwanitsa zivute zitani. Dzitsimikizireni nokha kuti muyesetsa kukwaniritsa zolinga zanu. Kenako sainani ndi kulemba deti la tsikulo.

Ndiphunzire Chitchaina n’cholinga choti ndizidzatha kulalikira anthu olankhula Chitchaina pofika pa July 1

Zimene ndingatsatire

1. Ndipeze buku lophunzitsa chilankhulocho.

2. Ndiziphunzira mawu 10 atsopano mlungu uliwonse.

3. Ndizimvetsera pamene anthu ena akulankhula Chitchaina.

4. Ndipemphe munthu wina kuti azindithandiza kudziwa ngati ndikutchula bwino mawu komanso ngati ndikutsatira malamulo a chilankhulocho.

Zinthu zimene zingandilepheretse

Palibe munthu wapafupi amene amalankhula Chitchaina

Kodi mavuto amenewa ndingathane nawo bwanji?

Ndizimvetsera zinthu zachitchaina pa adiresi ya www.pr418.com. kapena ndizimvetsera ma CD a Mboni za Yehova achitchaina

․․․․․ ․․․․․

Sainani Deti

Yambani Kuchitapo Kanthu Yohane 13:17 3

“N’zosavuta kuti munthu utengeke ndi zinthu zina n’kuiwala zolinga zako. Choncho ndi bwino nthawi zonse kukumbukira zolinga zako n’kupitiriza kuchita zinthu zimene zingakuthandize kuzikwaniritsa.”—Anatero Erika.

Yambani mwamsanga. Dzifunseni kuti, ‘Kodi lero ndingachite chiyani kuti ndiyambe kukwanitsa cholinga changa?’ Ndi zoona kuti simungadziwe zonse zoyenera kuchita, koma zimenezi zisakulepheretseni kuti muyambepo. Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, “woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.” (Mlaliki 11:4) Pezani chimene mungachite lero, kaya chikhale chaching’ono bwanji.

Muziunika zolinga zanuzo tsiku ndi tsiku. Musamaiwale kufunika kwa cholinga chilichonse chimene muli nacho. Muzichonga zinthu zimene mwakwanitsa kuchita zokuthandizani kukwanitsa cholinga chanu kuti mudziwe zimene zatsala.

Muzitha kusintha. Ngakhale kuti mwina munakonza dongosolo labwino kwambiri lokwaniritsira zolinga zanu, nthawi zina mungafunike kusintha. Palibe vuto kuchita zimenezi. Si bwino kungoti kakaka pa zinthu zimene munakonza kuti muchite. Muzingoyesetsa kuchita zimene mungathe kuti mukwanitse cholinga chanucho.

Yerekezerani mmene zinthu zingakhalire. M’maganizo mwanu, yesani kuona kuti mwakwanitsa kale cholinga chanu ndipo mukusangalala. Kenako, bwererani m’mbuyo n’kuona chilichonse chimene munachita kuti mukwanitse cholingacho. Mukatero, yambanipo.

[Chithunzi]

Kungokhala ndi pulani ya nyumba si kokwanira. N’chimodzimodzinso ndi zolinga. Mumafunika kuchita khama kuti mukwanitse zolinga zanu

[Bokosi/Zithunzi patsamba 25]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA 4

Ngati munthu alibe chilichonse chimene akuchita kapena chimene akuyembekezera kuchita m’tsogolo, amangokhumudwa ndi chilichonse. Koma akakhala ndi zolinga n’kuzikwaniritsa, amamva bwino kwambiri.—Anatero Reed.

Musamadziimbe mlandu ngati simukukwaniritsa zolinga zanu ndendende mmene mumafunira kapena pa nthawi imene mumafuna kuti zichitike. Maganizo amenewo ndi osathandiza. Inuyo muzingopitiriza kuchita zimene mungathe.—Anatero Cori.

Yesani kulankhula ndi anthu amene anakwaniritsa zolinga zofanana ndi zanu. Iwo angakulimbikitseni komanso angakupatseni malangizo amene angakuthandizeni. Mungapemphenso anthu a m’banja mwanu kuti akuthandizeni kukwaniritsa zolinga zanu.—Anatero Julia.

[Chithunzi patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Dulani motsatira timadonthoti

Pindani