Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Lilime la Mbalame ya Choso

Lilime la Mbalame ya Choso

Panagona Luso!

Lilime la Mbalame ya Choso

● Asayansi akamafufuza zinthu ngati DNA, magazi ndi zinthu zina zamadzimadzi, nthawi zina amatenga timadontho ting’onoting’ono kwambiri ta zinthu zimenezi n’kutiika pakagalasi kakang’ono koti kakhoza kungokwana m’manja, kuti azifufuze bwinobwino. Asayansiwa amagwiritsa ntchito tizipangizo tinatake timene timayamwa kapena kupopa timadzito, koma nthawi zambiri tizipangizoti sitithandiza kwenikweni. Kodi pali njira ina yabwino kwambiri yonyamulira timadontho ting’onoting’ono ta zinthu zamadzimadzi? Dr John Bush, wa payunivesite ya MIT (Massachusetts Institute of Technology), anati: “Njira yabwino ilipo kale m’chilengedwe.”

Taganizirani izi: Mbalame ya choso sivutika pomwa timadzi tam’maluwa. Mlomo wa mbalameyi ukangokhudza timadzi totsekemerati, timadzito timapinda mlomo wa mbalameyi ndipo lilime lake limakhala ngati kapaipi. Kenako timadzito timangoyenda tokha mosavutikira. Choncho mbalameyi siwononga mphamvu zake chifukwa timadzito timakwera tokha pa lilime la mbalameyo mpaka kukafika m’kamwa. Mbalamezi zikamamwa timadziti, zimatha kutsopa maulendo okwana 20 pa sekondi imodzi.

Anthu ena anati malilime a mbalamezi ali ngati “mapaipi omwera madzi amene amadzipanga okha.” Palinso mbalame zina zakunyanja zimenenso zimamwa madzi mwa njira imeneyi. Ponena za mmene mbalamezi zimamwera, pulofesa wina wa payunivesite ya Stanford ku California, U.S.A, dzina lake Mark Denny, anati: “Njirayi imaphatikiza sayansi yosiyanasiyana mogometsa kwambiri . . . Mukanauza munthu aliyense wa luso la zopangapanga kapena katswiri wa masamu kuti apeze njira zoti mbalame zizimwera madzi, sakanaganizira za njira yabwino kuposa imeneyi.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Lilime la mbalame ya choso ndi laling’ono kwambiri koma limatha kutsopa timadzi totsekemera tam’maluwa mwamsanga kwambiri ndiponso mosavutikira. Kodi mukuganiza kuti lilimeli linangokhalapo lokha, kapena alipo amene analipanga?

[Mawu a Chithunzi patsamba 23]

© Richard Mittleman/Gon2Foto/Alamy