Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zidziweni Bwino Mbira Zam’mapiri

Zidziweni Bwino Mbira Zam’mapiri

Zidziweni Bwino Mbira Zam’mapiri

Ndinamva kulira kokweza kwambiri ngati kwa likhwelu la mnyamata amene akuitana mnzake, kungoti linali lokwera kwambiri. Likhwelulo linamveka m’mapiri monsemo, koma silimadziwika kuti likuchokera pati. Kenako ndinaona kanyama kenakake kakuthawira pa una umene unali chapafupi. Nditafufuza msangamsanga m’buku langa lofotokoza za nyama, ndinazindikira kuti nyama ndinaonayo inali mbira yam’mapiri.

PATAPITA masiku angapo ndinazidziwa bwino kwambiri mbirazi. Ndinadziwa miyala imene zimakonda kuwotherapo dzuwa, kumene kuli mauna awo, ndiponso zimene zimachita kuti zizitha kukhala m’malo ovuta kukhalamo a m’mapiri.

Zimagwirizana Komanso N’zatcheru

Moyo wa m’mapiri ndi wovuta kwambiri kwa mbirazi chifukwa m’nyengo yachisanu, kunja kumazizira kwambiri ndipo madzi amatha kuundana kwa miyezi ingapo. Komanso mbirazi zili ndi adani ambiri, ena ouluka m’mlengalenga ndi ena okhala m’mapiri momwemo. Choncho zimafunika kugwirizana, kukonzekera bwino, komanso kukhala tcheru.

Mbirazi zimakonda kukhala m’magulu. Nthawi zambiri pa gulu lililonse pamakhala makolo ndi ana awo. Gulu lililonse limakhala ndi mauna angapo. Una umodzi umakhala ngati nyumba yawo ndipo mauna enawo zimathawiramo zikaona chinthu choopsa. Nthawi zina mbirazi zimakumba mauna awo pansi pa miyala ikuluikulu. Pamalo amene zimakumba maunawa pamakhala pabwino kwambiri kuwothera dzuwa komanso kuonera adani.

Mbira zam’mapiri ndi zaukhondo kwambiri. Zimakhala ndi una wapadera umene zimagwiritsa ntchito ngati chimbudzi. Kumapeto kwa una umene zimakhala, kumakhala malo ogona aakulu omwe zimayalapo udzu. Mbira yaikazi imaberekera pamalo amenewa. Malowa amakhalanso otentha bwino ndipo m’nyengo yozizira, mbira zonse zimagona pamenepa zitatsamiranatsamirana kuti zizimva kutentha.

Mwina ntchito yofunika kwambiri imene mbirazi zimachita zikakhala pagulu ndi yaulonda. Mbira zina zikamasakasaka chakudya, mbira yaikulu imakhala ikulondera. Kuti ione ngati kukubwera adani, imaimirira ndi miyendo yam’mbuyo n’kuponya maso uku ndi uko. Mbirazi zimaopa kwambiri mphamba, ankhandwe komanso anthu. Zikangoona adaniwa, zimayamba kulira pofuna kuchenjezana. Mphamba ndiye mdani wamkulu wa mbira pa mbalame zonse. Choncho mbira yolondera ija ikangoona mphamba, imalira mosiyana kwambiri ndi mmene imalirira ikaona adani ena. Mbirazo zikangomva kulira kwa mbira yolondera ija, nthawi yomweyo zimathawa n’kukabisala. Pasanapite nthawi yaitali, zonse zimakhala zitalowa m’mauna awo.

Mbira, makamaka zazing’ono, zimafunika kukhala zomvera chifukwa mphamba zimakonda kwambiri kudya tiana ta mbira. Mdaniyo akayandikira kwambiri, mbira yolondera ija imathamangira pauna wapafupi n’kulowa limodzi ndi mbira zina zija. Kenako pakapita kanthawi kochepa, mlondayo amatulutsa mutu kuti aone ngati mdaniyo wapita, koma amachita zimenezi mochenjera.

Zimene Zimachita Kunja Kukatentha Kapena Kukazizira

M’mapiriwa mumapezeka udzu wambiri womwe mbirazi zimadya. Nyengo ya kumalowa si yotentha kwambiri. Kukazizira, mbirazi zimakonda kukhala m’miyala n’kumawothera dzuwa koma kukatentha zimavutika chifukwa zili ndi ubweya wambiri. Pachifukwa chimenechi, mbirazi zimakonda kuyendayenda m’mawa kwambiri ndi madzulo.

Mbirazi zilibe vuto losowa tulo chifukwa zimatha kugona kwa miyezi pafupifupi 6. Pa nthawi yomwe zili m’tulo, mtima wawo umagunda kamodzi kapena kawiri basi pa mphindi iliyonse. Thupi lawo limazizira kwambiri. Choncho, mbirazi zimafunika kukonzekera kuti zikwanitse kugona nthawi yaitali chonchi. Pokonzekera nyengo yozizira, mbirazi zimadya kwambiri m’nyengo yotentha kuti zinenepe n’cholinga choti thupi lawo likhale ndi mafuta ambiri odzagwiritsa ntchito m’miyezi yozizira imene zimakhala zikugona.

Mbira zazing’ono zimakonda kusewera ndipo nthawi zambiri zimakhala zikuthamangitsana. Pa ulendowu, ndinaona mbira zina zitatu zazing’ono zikutsetsereka pa chimwala chachikulu. Mbirazi zinkachita masewera omenyana. Mbira zazikulu komanso zazing’ono zimapatsana moni pogunditsana mphuno zawo ndipo zagulu limodzi zimakonzanakonzana ubweya. Kunja kukazizira, zimatsamirana kuti zimve kutentha.

Nyama zimenezi zimakonzekera zam’tsogolo komanso zimakhala tcheru pofuna kupewa zinthu zoopsa. (Yobu 12:7) Mwina anthu akhoza kuphunzira zambiri kuchokera ku nyama zimenezi.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Mbirazi zimachititsa kuti kumapiri kuzikhala kosangalatsa kwambiri, ndipo kugwirizana kwawo kumasonyeza kuti zinalengedwa ndi Mlengi wanzeru.—Salimo 50:10

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Mbira zina zikamasakasaka chakudya, mbira yaikulu imakhala ikulondera