Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Akatswiri ochita kafukufuku ku Canada ankafuna kufufuza mmene kuonera zinthu zolaula kumakhudzira amuna. Munthu wina amene anachita nawo kafukufukuyo anati: “Tinkafuna kuyamba ndi kufufuza amuna azaka za m’ma 20 amene sanaonerepo zithunzi zolaula, koma sitinapeze ngakhale mmodzi.”—UNIVERSITY OF MONTREAL, CANADA.

Nyumba yaitali kwambiri padziko lonse, yotchedwa Burj Khalifa, inatsegulidwa m’mwezi wa January ku Dubai. Nyumbayi ndi yaitali mamita 828, ili ndi nyumba zosanja zokwana 160 ndipo munthu amatha kuiona kuchokera pa mtunda wa makilomita 95.—GULF NEWS, UNITED ARAB EMIRATES.

“Kusintha kwa chipembedzo cha Chiyuda n’kopanda phindu ngati kusinthako sikukugwirizana ndi mmene zinthu zikusinthira panopa. Posachedwapa, mapemphero achiyuda anawasintha. Panopa akupemphereranso anthu amene anawachita opaleshoni yowasintha kuti azioneka ngati aamuna kapena aakazi.”—THE NEW YORK TIMES MAGAZINE, U.S.A.

Ana Ovutika Kulankhula

Masiku ano makolo ambiri sakhala ndi nthawi yokwanira yocheza ndi ana awo pa nthawi yachakudya, kapena yowawerengera mabuku asanagone, kusiyana ndi kale. Nyuzipepala ya Times ya ku London, inati: “Ana akuyamba sukulu ya pulayimale koma akulankhula zosamveka ngati kamwana ka chaka chimodzi ndi theka, ndipo chiwerengero cha ana amene amakanika kungolankhula mawu ochepa chabe koma omveka bwino chikuwonjezereka.” Nyuzipepalayi inanenanso kuti ku Britain, “ana 18 pa 100 alionse azaka zisanu (omwe ndi oposa 100,000) amalephera kulankhula zomveka zogwirizana ndi msinkhu wawo.” Choncho, ana ambiri amene amalephera kumvetsa malangizo kapena kunena zimene akufuna amakhala ngati “alendo m’kalasi mwawo momwe,” chifukwa sadziwa chimene chikuchitika.

Posachedwapa Matchalitchi a ku Ireland Adzasowa Ansembe

Nyuzipepala ya ku Ireland yotchedwa The Irish Times inati: “Zimene tikuona panopa n’zakuti ansembe mu mpingo wa Katolika akutha.” Zaka 50 zapitazo, ku Ireland n’kumene kunali chiwerengero chachikulu kwambiri cha ansembe kuposa dziko lina lililonse. Panopa, ansembe ambiri ku Ireland akukalamba, ndipo ansembe amenewa akangokwanitsa zaka 75 zomwe munthu amasiyira ntchito ya unsembe, maparishi ena adzakhala opanda ansembe. Ena akuti vutoli linayamba pamene mpingo wa Katolika unaletsa kugwiritsa ntchito mankhwala olera. Mpingowu unaletsa zimenezi m’chaka cha 1968 m’chikalata chimene Papa analembera mabishopu a mpingowu. Nyuzipepala ija inanena kuti kalata imeneyi inachititsa kuti anthu “ayambe kukayikira ziphunzitso za tchalitchichi” ndipo kenako anayamba kuona kuti “atsogoleri a mpingowu sakuyendetsa bwino zinthu.”

Malo Amene Kampasi Imaloza a Kumpoto kwa Dziko Akusuntha

Mu 1831, anthu anatulukira kuti kampasi ikamaloza kumpoto kwa dziko, nthawi zonse inkaloza malo enaake kumpoto kwa dziko la Canada. Malowa ali pa mtunda wa “makilomita 2,750 kuchokera kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi,” inatero nyuzipepala ya ku France ya Le Figaro. Chisanafike chaka cha 1989, malo amene kampasi imaloza anayamba kusuntha n’kumayandikana ndi kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi. Malowa ankasuntha ndi makilomita 5 mpaka 15 pa chaka. Malinga ndi akatswiri ena asayansi ku Paris, panopa malowo akusuntha ndi “makilomita 55 pa chaka” ndipo mu 2007, malowa anali pamtunda wa makilomita 550 okha kuchokera kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi. Nyuzipepala ija inanena kuti tikatengera mmene malowa akusunthira panopa, pofika chaka cha 2020, kuwala kumene kumaonekera usiku pamwamba pa malo amene kampasi imaloza kumpoto, “kuzionekera kwambiri ku Siberia, osati ku Canada.”