Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Diso la Nkhanu Yooneka Ngati Chiswamphika

Diso la Nkhanu Yooneka Ngati Chiswamphika

Panagona Luso!

Diso la Nkhanu Yooneka Ngati Chiswamphika

● Nkhanu yooneka ngati chiswamphika imeneyi imapezeka m’nyanja ya Pacific pafupi ndi gombe lina ku Australia, pamalo otchedwa Great Barrier Reef. Nkhanuyi ili ndi maso ogometsa kwambiri pa nyama zonse. Dr. Nicholas Roberts ananena kuti: “Maso a nkhanuyi ndi odabwitsa zedi ndipo amagwira ntchito mogometsa kwambiri kuposa chipangizo chilichonse chimene anthu apanga.”

Taganizirani izi: Nkhanuyi imatha kuona bwinobwino ngakhale zinthu zowala mothobwa m’maso zimene anthu sangathe kuziona bwinobwino. Zinthu zimathobwa m’maso chifukwa chakuti kuwala kwasokonezedwa mwanjira inayake. Kuwala kukasokonezedwa, kumatha kuyenda m’mizere yowongoka kapena yokhotakhota. Mosiyana ndi nyama zina, maso a nkhanuyi amatha kusintha kuwala kothobwa m’maso kuti iziona bwinobwino, kaya kuwalako kukuyenda m’mizere yowongoka kapena yokhotakhota. Zimenezi zimathandiza nkhanuyi kuti izitha kuona zinthu zimene nyama zina sizingathe kuona.

Mawailesi a DVD amachita zofanana ndi zimenezi. Kuti wailesiyi ithe kuimba zimene zili mu DVD, imafunika kusintha kuwala kumene kukuyenda m’mizere yowongoka kuti kuziyenda m’mizere yokhotakhota, kenako n’kukusintha kuti kuyambenso kuyenda m’mizere yowongoka. Koma maso a nkhanuyi amachita zoposa pamenepa. Mawailesi ambiri a DVD amasintha kuwala kofiira kokha ndipo ena apamwamba kwambiri amatha kusinthanso kuwala kwa buluu. Koma maso a nkhanuyi amatha kusintha kuwala kwa mitundu yonse imene imaoneka pa utawaleza.

Akatswiri ofufuza akukhulupirira kuti potengera maso a nkhanuyi, anthu akhoza kupanga mawailesi a DVD apamwamba kwambiri otha kuimba ma DVD okhala ndi zinthu zambiri mkati mwake kuposa ma DVD a masiku ano. Roberts anati: “Chochititsa chidwi kwambiri n’chakuti maso a nkhanuyi amachita zonsezi mosavutikira ngakhale pang’ono. Amagwira ntchito bwino kwambiri kuposa chipangizo chilichonse chimene tayeserapo kupanga.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi maso ogometsa a nkhanu yooneka ngati chiswamphika imeneyi anangokhalapo okha, kapena alipo amene anawapanga?

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Courtesy Stephen Childs