Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndinakulira M’banja Losakhulupirira Kuti Kuli Mulungu”

“Ndinakulira M’banja Losakhulupirira Kuti Kuli Mulungu”

“Ndinakulira M’banja Losakhulupirira Kuti Kuli Mulungu”

PULOFESA František Vyskočil, wapayunivesite yotchedwa Charles mumzinda wa Prague, m’dziko la Czech Republic, ndi wodziwika kwambiri padziko lonse chifukwa cha kafukufuku amene wachita wokhudza mmene ubongo umagwirira ntchito. Kale sankakhulupirira zoti kuli Mulungu, koma panopa sakayikira ngakhale pang’ono kuti kuli Mulungu. Wolemba Galamukani! anacheza ndi Pulofesa Vyskočil kuti afotokoze chimene chinam’chititsa kusintha. Tamvani zimene Pulofesayu ananena.

Musanakhale wasayansi, kodi chipembedzo munkachiona bwanji?

Ndinakulira m’banja losakhulupirira kuti kuli Mulungu, ndipo nthawi zambiri bambo anga ankanyoza azibusa. Ndinamaliza maphunziro anga a kuyunivesite m’chaka cha 1963. Kuyunivesiteku ndinkatenga maphunziro okhudza sayansi ya zinthu zamoyo ndiponso mmene zinthu zosiyanasiyana zinapangidwira. Pa zaka zonse zomwe ndinali kusukulu, ndinkakhulupirira kuti zamoyo zosiyanasiyana zimene timaona zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.

Tiuzeniko zinthu zingapo zokhudza ntchito yanu monga wasayansi

Nditamaliza maphunziro otengera digiri yapamwamba kwambiri, ndinachita kafukufuku wokhudza mmene ubongo umalandirira ndi kutumizira uthenga. Ndinachitanso kafukufuku wokhudza mapuloteni amene amachititsa kuti zinthu zithe kulowa kapena kutuluka m’maselo, sayansi imene imathandiza kuti zizikhala zotheka kuchotsa mnofu pa malo ena m’thupi n’kukauika pena, komanso mmene madokotala angathandizire anthu amene thupi lawo likudana ndi mankhwala enaake. Zinthu zambiri zimene ndinapeza pa kafukufukuyu zafalitsidwa m’mabuku, ndipo nkhani zina zinasankhidwa kuti n’zapamwamba kwambiri. Patapita nthawi, ndinasankhidwa n’kukhala m’gulu la asayansi otchuka kwambiri a ku Czech Republic. Asayansi a m’gulu limeneli amakhala ophunzira kwambiri ndipo amasankhidwa ndi asayansi anzawo. Pambuyo pa kutha kwa boma la chikomyunizimu mu December 1989, ndinakhala pulofesa payunivesite ya Charles, ndipo ndinkapatsidwa mwayi wopita kumayiko ena omwe sanali achikomyunizimu kukakumana ndi asayansi osiyanasiyana. Ena mwa asayansi amenewa analandirapo mphoto ya Nobel, yomwe imaperekedwa kwa anthu amene achita zinthu zazikulu.

Kodi pa nthawiyi munkaganizirako n’komwe zoti kuli Mulungu?

Osati kwenikweni. Komabe ndinkadabwa kuti n’chifukwa chiyani anthu ambiri ophunzira, kuphatikizapo aziphunzitsi anga, ankakhulupirira kuti kuli Mulungu. Iwo ankachita zimenezi mosaonetsera chifukwa choopa boma lachikomyunizimu. Koma ineyo ndinkaona kuti nkhani yakuti kuli Mulungu ndi yongopeka chabe. Komanso sindinkakhulupirira zoti kuli Mulungu chifukwa choona nkhanza zimene zinkachitika m’dzina la chipembedzo.

Kodi zinatani kuti musiye kukhulupirira kuti zamoyo zinangokhalapo zokha?

Ndinayamba kukayikira nkhani yakuti zamoyo zinangokhalapo zokha ndidakali kusukulu. Nditaphunzira za mmene ubongo umalandirira ndi kutumizira uthenga, ndinagoma kwambiri. Ndinkadzifunsa kuti: ‘Kodi zingatheke bwanji kuti zinthu zogometsa ngati zimenezi komanso malangizo a mu DNA zingokhalapo mwangozi?’ Ndinkaona kuti n’zosatheka.

Kenako chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1970, ndinamvera nkhani ya pulofesa wina wa ku Russia, yemwe anali wasayansi wotchuka kwambiri. Iye ananena kuti zamoyo zimene timaona sizinachite kusintha pa zifukwa zosiyanasiyana kuchokera ku zamoyo zina. Kenako munthu wina pagulupo anafunsa pulofesayo kuti afotokoze kumene zamoyo zinachokera. Iye anangotenga kabaibulo kakang’ono kachirasha m’thumba la jekete lake n’kukaimika m’mwamba, n’kunena kuti: “Muziwerenga Baibulo, makamaka nkhani ya ku Genesis yonena za kulengedwa kwa zinthu.”

Pulofesayo atamaliza kuphunzitsa, ndinakumana naye pamalo ofikira alendo n’kumufunsa ngati ankakhulupiriradi zimene ananena zokhudza Baibulo. Iye anayankha kuti: “Pa mphindi 20 zilizonse, bakiteliya amagawanika pawiri ndipo bakiteliya aliyense amakhala ndi mapuloteni mahandiredi ambiri. Komanso puloteni iliyonse imakhala ndi tinthu tinanso tatitali kwambiri tokwana 20 tomwe timayalana bwinobwino ngati tcheni. Kuti bakiteliya mmodzi asinthe n’kukhala wamtundu wina zingatenge nthawi yaitali kwambiri, kuposa zaka 3 biliyoni kapena 4 biliyoni zimene asayansi amakhulupirira kuti zamoyo zakhalapo padzikoli.” Choncho pulofesayo ankaona kuti buku la Genesis limanena zomveka.

Nanga zimene pulofesayo ananena zinakukhudzani bwanji?

Zinthu zimene pulofesayo anatulukira komanso zimene ankakayikira, zinandichititsa kuti ndikambirane nkhaniyi ndi anthu angapo ogwira nawo ntchito komanso anzanga opemphera, koma zimene anandiuza sizinandikhutiritse. Kenako ndinakambirana ndi katswiri wina wazamakhwala, yemwe anali wa Mboni za Yehova. Kwa zaka zitatu iye anafotokozera ineyo ndi mkazi wanga, Ema, zimene Baibulo limanena. Tinachita chidwi ndi zinthu ziwiri. Choyamba, tinazindikira kuti zipembedzo zambiri zachikhristu zimaphunzitsa zinthu zimene sizili m’Baibulo. Chachiwiri, tinazindikira kuti Baibulo limagwirizana ndi sayansi yeniyeni ngakhale kuti si buku la sayansi.

Kodi ntchito yanu ngati wasayansi sinasokonezedwe chifukwa choyamba kukhulupirira zoti kuli Mulungu?

Ayi. Wasayansi aliyense wodziwa ntchito yake akamafufuza zinthu, ayenera kutsatira njira za sayansi m’malo motsatira zikhulupiriro zake. Koma ineyo ndinasintha kwambiri chifukwa cha zimene ndinayamba kukhulupirira. Mwachitsanzo, m’malo mokhala munthu wodzidalira kwambiri, wokonda mpikisano, komanso wonyada chifukwa cha zimene ndachita zokhudza sayansi, ndimayamikira Mulungu chifukwa cha nzeru zilizonse zimene ndili nazo. Komanso m’malo monena kuti zinthu zogometsa zimene timaona m’chilengedwe zinangokhalapo mwangozi, ineyo ndi asayansi ena ambiri timadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu anapanga bwanji zimenezi?’

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Ineyo ndi asayansi ena ambiri timadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu anapanga bwanji zimenezi?’