Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Simunataye Mtima”

“Simunataye Mtima”

“Simunataye Mtima”

● Camila ali ndi vuto la kuperewera kwa magazi m’thupi, matenda okhudzana ndi ubongo, komanso vuto lochedwa kukula. Chifukwa cha matendawa pofika zaka 8, Camila anali wamtali masentimita 75 okha. Makolo a Camila ndi a Mboni za Yehova ndipo amakhala ku Argentina. Tsiku lina anapita naye ku msonkhano wazachipatala umene unkachitikira muholo inayake yoonetsera zisudzo m’tawuni imene akukhala. Iwo anakhala mzere wachiwiri kuchokera kutsogolo, ndipo muholomo munali anthu 500.

Dokotala wina akukamba nkhani yake, analoza Camila n’kunena kuti iye ndi chitsanzo chabwino cha munthu wathanzi. Dokotalayo sankadziwa kuti Camila ndi wamkulu ndiponso kuti ali ndi matenda. Choncho anafunsa mayi ake kuti: “Kodi mwanayu ali ndi miyezi ingati?”

Amayi ake a Camila, a Marisa, anayankha kuti: “Ali ndi zaka 8.”

Dokotalayo anafunsa kuti: “Mwati zaka 8, kapena miyezi 8?”

“Ali ndi zaka 8,” anayankha choncho mayiwo.

Dokotalayo anadabwa kwambiri ndipo anapempha mayiwo ndi mwana wawo kuti apite kutsogolo akawafunse mafunso ena. Amayi a Camila anafotokoza kuti madokotala osiyanasiyana ayesetsa kufufuza mmene angamuthandizire mwanayo, ndipo amupatsa chithandizo chosiyanasiyana, koma sizinathandize. Kenako dokotalayo anati: “Azimayi ena amalira mwana wawo akangodwala chimfine. Koma inuyo, ngakhale kuti mwakhala mukuyenda m’zipatala kwa zaka 7, ndipo mwayesetsa kuchita zonse zimene mukanatha kuti muthandize mwana wanu, simunataye mtima. Kodi n’chiyani chakuthandizani?”

Poyankha, amayi a Camila anauza anthu amene anasonkhana pamalopo za chiyembekezo chimene ali nacho chofotokozedwa m’Baibulo choti kukubwera dziko latsopano limene lidzakhale labwino kwambiri. M’dziko limeneli, simudzakhala matenda, kuvutika kulikonse, ngakhale imfa. (Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:3, 4) A Marisa anafotokoza kuti Mboni za Yehova padziko lonse ndi zogwirizana ndiponso zimakondana kwambiri. Chifukwa cha chikondi chimenechi, zimathandizana kulimbana ndi mavuto alionse amene zimakumana nawo pa moyo wawo.—Yohane 13:35.

Msonkhanowu utatha, mayi wina anapempha amayi a Camila kuti amufotokozere zambiri zokhudza mfundo zimene ananena zija. Mayiyu ankafunitsitsa kudziwa zambiri, ndipo anavomera kuti aziphunzira Baibulo kwaulere. Mboni za Yehova padziko lonse zimaphunzitsa Baibulo anthu amene amafuna kumvetsetsa zimene Baibulo limanena komanso kudziwa zinthu zabwino zimene Mulungu wakonzera anthu.

[Chithunzi patsamba 25]

Camila ndi mayi ake. Apa n’kuti Camila ali ndi zaka 8