Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Pa nsomba ndi nyama zina zam’nyanja zokwana matani 95.2 miliyoni zimene anthu amagwira chaka chilichonse, zokwana matani 38.5 miliyoni zimatayidwa. Katswiri wina yemwe amagwira ntchito ku bungwe losamalira nsomba ndi zinthu zina zachilengedwe, dzina lake Karoline Schacht, anati: “Tikapitiriza kutaya pafupifupi theka la zinthu zonse zimene timagwira m’nyanja, ndiye kuti sizingachulukanenso.”—BERLINER MORGENPOST GERMANY.

“Zingaoneke ngati anthu amalakwira ng’ombe, nkhosa ndi mbuzi akamazipha n’kudya. Koma . . . mpweya woipa umene ziwetozi zimatulutsa padziko lonse, umapanga 18 peresenti ya mpweya wonse umene umawononga chilengedwe. Mpweya umenewu ndi wambiri kuposa mpweya wonse woipa umene umatulutsidwa ndi magalimoto, sitima, ndege ndi zinthu zina zotero.”—NEW SCIENTIST, BRITAIN.

Guluu Wakale Kwambiri

Asayansi ena ku KwaZulu-Natal, ku South Africa, anapeza guluu wamphamvu kwambiri amene anthu ankamugwiritsa ntchito zaka masauzande ambiri apitawo. Nyuzipepala ya The Star ya ku Johannesburg, inati: “Guluu ameneyu . . . ndi wabwino kwambiri ndipo sakusiyana ndi guluu wamphamvu amene mungamupeze m’masitolo masiku ano.” Asayansiwa akukhulupirira kuti kale, alenje ankagwiritsa ntchito guluu ameneyu pomatira nsonga za mivi ndi mikondo ku zogwirira zake. Asayansiwa anayesera kupanga guluu ameneyu ngati mmene anthu ankapangira kalelo. Iwo anasakaniza dothi lofiira, mafuta a nyama, ulimbo ndi mchenga. Atachita zimenezi, anaumitsa guluuyo pamoto umene umafunika kuti usakhale wotentha kwambiri komanso usakhale wochepa mphamvu kwambiri. Atamaliza, asayansiwa ananena kuti kupanga guluu ameneyu si kophweka ngati mmene amaganizira poyamba, ndipo anati “awatayira kamtengo” anthu akalewo.

Anthu Amene Sagona Mokwanira Amadwaladwala Chimfine

Lipoti lina lochokera kuyunivesite ya Carnegie Mellon ku Pittsburgh, Pennsylvania, U.S.A, linati: “Anthu amene amagona maola osakwana 7 usiku, amadwaladwala chimfine kuwirikiza katatu kuposa amene amagona maola 8 kapena kuposa pamenepo.” Anthu “amene amati akapita kokagona n’kukhala maso kwa kanthawi ndithu asanagone kapena amadzidzimuka n’kukhala kanthawi ndithu asanagonenso, amadwaladwala chimfine kuwirikiza maulendo asanu ndi theka” kuposa amene amakhaladi mtulo kwa nthawi yonse imene akugona. Munthu amene anatsogolera kafukufukuyu, dzina lake Sheldon Cohen, anati: “Ngakhale kuti nkhani yoti kusagona mokwanira kumachepetsa mphamvu ya thupi lathu yolimbana ndi matenda ndi yodziwika bwino, kafukufukuyu ndi woyamba kusonyeza kuti kusokoneza tulo ngakhale pang’ono chabe, kumachititsa kuti thupi lisamadziteteze mokwanira ku tizilombo toyambitsa chimfine. Kafukufukuyu akungotsimikizira kuti n’zofunika kwambiri kuti anthu aziyesetsa kugona mokwanira tsiku lililonse.”

Malo Olima Adakalipo Ambirimbiri

Magazini ya New Scientist, inati: “Padziko lapansi pali malo okwanira oti n’kulimapo chakudya chambiri chokwana kudyetsa anthu, ngakhale kuti akuwonjezereka. Ndipo mosiyana ndi zimene anthu ankaganiza, chakudya chambiri chowonjezerachi chingamalimidwe ku Africa.” Magaziniyi inafotokoza za lipoti lotulutsidwa ndi mabungwe ena oona zachakudya, limene linanena kuti malo amene anthu akulimapo chakudya atha kuwonjezeredwa mpaka kuwirikiza kawiri. Lipotilo linati: “Malo opitirira theka a malo atsopanowa angapezeke ku Africa ndi ku Latin America.”