Zoti Banja Likambirane
Zoti Banja Likambirane
Kodi Pachithunzipa Pakusoweka Chiyani?
Werengani Danieli 6:1-24. Ndiyeno onani chithunzichi. Kodi pakusoweka chiyani? Lembani mayankho anu pamizere imene ili m’munsiyi. Kenako malizitsani kujambula chithunzichi pojambula zinthu zimene zikusowekapo komanso muchichekenire.
1. ․․․․․
2. ․․․․․
KAMBIRANANI:
N’chifukwa chiyani Danieli anaponyedwa m’malo amenewa? Kodi munayamba mwavutikapo chifukwa chochita zabwino? Fotokozani zimene zinachitika. Kodi n’chifukwa chiyani ndi bwinobe kuchita zabwino ngakhale kuti zingakupezetseni mavuto?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Petulo 2:19-21.
KODI MUKUDZIWA ZOTANI ZOKHUDZA MTUMWI MATEYU?
3. Kodi Mateyu ankadziwikanso ndi dzina lotani?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mateyu 9:9; Maliko 2:14.
․․․․․
4. Kodi Mateyu analolera kusiya chiyani kuti akhale wotsatira wa Yesu?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Luka 5:27, 28.
․․․․․
KAMBIRANANI:
Kodi mungafunike kusiya chiyani kuti mukhale wophunzira wa Yesu? Ndipo kodi mungapeze zinthu zotani?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Maliko 10:28-30.
ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE
Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Kenako fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
KUCHOKERA M’MAGAZINI INO
Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.
TSAMBA 6 Kodi ndani anapanga zinthu zonse? Aheberi 3:․․․
TSAMBA 7 Kodi anthu oipa chidzawachitikire n’chiyani? Miyambo 2:․․․
TSAMBA 20 Kodi anthu amafika kwa Atate kudzera mwa ndani? Yohane 14:․․․
TSAMBA 21 Kodi tizipempherera ndani? Yakobo 5:․․․
● Mayankho ali pa tsamba 12
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
1. Mikango.
2. Mngelo.
3. Levi.
4. Anasiya zonse.