Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ankaphunzirira Limodzi ndi Ana Ake

Ankaphunzirira Limodzi ndi Ana Ake

Ankaphunzirira Limodzi ndi Ana Ake

● Mayi wina wazaka za m’ma 30, amene amakhala ndi mwamuna wake ndi ana awo atatu ku Kentucky, m’dziko la U.S.A. analemba kuti: “Banja lathu lathandizidwa kwambiri ndi mabuku onse a Mboni za Yehova amene tili nawo.” Iye anafotokoza kuti: “Buku limene ndimakonda kwambiri kuwerengera ana anga ndi lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.” Iye ananenanso kuti akamawerengera anawo “ankaphunzirira limodzi ndi ana ake.”

Bukuli lili ndi zithunzi zokongola ndipo limafotokoza nkhani za m’Baibulo motsatira nthawi imene zinachitika. Mwachitsanzo, Gawo 2 la bukuli lili ndi nkhani monga zakuti “Mfumu Yoipa Ilamula Igupto,” “M’mene Mose Anapulumutsidwira,” “Chifukwa Chake Mose Akuthawa,” “Mose ndi Aroni Aona Farao,” “Miriri 10,” ndiponso “Kuoloka Nyanja Yofiira.”

Gawo 6 la bukuli lili ndi mutu wakuti “Kubadwa kwa Yesu Mpaka pa Imfa Yake” ndipo lili ndi nkhani zosiyanasiyana zokhudza moyo wa Yesu, kuyambira kubadwa kwake mpaka imfa yake. Zina mwa nkhanizi n’zakuti, “Yesu Abadwira m’khola,” ndiponso “Amuna Atsogozedwa ndi Nyenyezi.” Nkhani yomalizayi imasonyeza kuti “anzeru,” amene kwenikweni anali anthu okhulupirira nyenyezi, ‘analowa m’nyumba’ kuti aone Yesu, chifukwa iye anali atachoka m’khola mmene anabadwira. M’nyumbamo, iwo “anaona mwanayo ndi mayi ake Mariya.” Amunawa anachenjezedwa ndi Mulungu kuti asapitenso kwa Herode, yemwe ankafuna kupha Yesu. Kodi nkhani imeneyi ikusonyeza kuti nyenyezi imene inawatsogolera ija inatumizidwa ndi ndani?—Mateyu 2:1, 11, 12.

Inunso mungaphunzirire limodzi ndi ana anu mukamawawerengera Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Bukuli lili ndi nkhani 116 zonena za anthu ndi zochitika zimene zinatchulidwa m’Baibulo. Ngati mukufuna bukuli, lembani adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yoyenera pa maadiresi omwe ali patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.