Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiyembekezere Zivomezi Zinanso Zikuluzikulu

Tiyembekezere Zivomezi Zinanso Zikuluzikulu

Tiyembekezere Zivomezi Zinanso Zikuluzikulu

KUNGOYAMBIRA pamene asayansi anapanga zipangizo zoyezera mphamvu ya chivomezi, iwo ayeza mphamvu ya zivomezi zambirimbiri zikuluzikulu. Zivomezi zimene zimachitikira kutali kwambiri ndi kumene anthu amakhala, sizidetsa nkhawa, ndipo nthawi zambiri anthu olemba nkhani sazitchula n’komwe. Koma zimene zimachitikira m’mizinda ikuluikulu zimawononga kwambiri. Anthu ambiri amafa ndiponso katundu wambiri amawonongeka, makamaka ngati anthuwo sanakonzekere bwino.

Pa January 12, 2010, ku Haiti kunachitika chimodzi mwa zivomezi zowononga kwambiri m’mbiri yonse ya anthu, tikatengera chiwerengero cha anthu amene anafa komanso katundu amene anawonongeka. Koma chimenechi sichinali chivomezi chachikulu choyamba, komanso sichinali chomaliza chaka chino. M’munsimu muli zina mwa zivomezi zimene zinachitika kumayambiriro kwa chaka cha 2010. Zina mwa zivomezi zimenezi zinali zofanana kapena zamphamvu kwambiri kuposa chivomezi chimene chinawononga kwambiri likulu la dziko la Haiti, chomwe chinali ndi mphamvu zokwana 7.0, pa sikelo yoyezera zivomezi.

January 3: Chivomezi Champhamvu Zokwana 7.1, Solomon Islands

Chivomezichi chinali chachikulu kwambiri ndipo mphamvu zake zimakwana 7.1 pa sikelo yoyezera zivomezi. Chinachititsa kuti madzi asefukire, ndipo “mafunde amene amachokera kunyanja kupita kumtunda anali aatali mamita pafupifupi atatu.” Munthu wina yemwe amagwira ntchito ku dipatimenti yoona za mavuto ogwa mwadzidzidzi, dzina lake Loti Yates, ananena kuti ali mundege ankaona kuti “dera lonselo lamiriratu.” Malinga ndi zimene Yates ananena, nyumba 16 zinakokoloka ndipo zina zambiri zinawonongeka m’mudzi wina wotchedwa Bainara, womwe uli pachilumba cha Rendova.

Chivomezichi chisanachitike, kunachitika chivomezi china chocheperapo mphamvu, chokwana 6.6. Anthu ambiri anachita mantha ndi chivomezichi ndipo anathawira kumapiri. Zimenezi zinathandiza kuti chivomezi chachiwirichi chitayamba, chomwe chinachitika patapita maola awiri, anthu ambiri asafe ndi madzi amene anasefukira.

February 26: Chivomezi Champhamvu Zokwana 7.0, Zilumba za Ryukyu, ku Japan

Chivomezi chimenechi chinachitika nthawi ili 5:31 m’mawa, ndipo chinayambira pa mtunda wa makilomita 80 kuchokera ku Naha, m’chigawo cha Okinawa, pa chimodzi mwa zilumba za ku Japan za Ryukyu. Akuluakulu a boma anachenjeza anthu kuti madzi asefukira koma kenako ananena kuti zimenezi sizichitika. Mayi wina amene wakhala ku Okinawa kwa zaka zoposa 90, ananena kuti chivomezichi chinali champhamvu kwambiri kuposa zivomezi zonse zimene iye wazionapo pa moyo wake.

February 27: Chivomezi Champhamvu Zokwana 8.8, Chile

Chimenechi chinali chivomezi chachisanu pa zivomezi zamphamvu kwambiri zimene zakhala zikuchitika padziko lonse kuyambira m’chaka cha 1900. Chivomezi champhamvu kwambiri pa zonse chinachitikiranso ku Chile komweko m’chaka cha 1960, ndipo chinali champhamvu zokwana 9.4. Chivomezichi, ndiponso china chimene chinawononga likulu la dziko la Chile mu 1985, chomwe chinali champhamvu zokwana 7.7, chinachititsa dziko la Chile kukhazikitsa malamulo okhwima kwambiri a kamangidwe ka nyumba.

Pa chifukwa chimenechi, nyumba zambiri za mumzinda wa Santiago ndi mizinda ina sizinagwe kutachitika chivomezi chaka chino. Komabe, anthu ambiri anavulala ndipo katundu wawo anawonongeka. Akuti pafupifupi anthu 500 anafa. Theka la anthu amenewa anafa ndi madzi osefukira amene anawononga kwambiri madera a m’mphepete mwa nyanja.

April 4: Chivomezi Champhamvu Zokwana 7.2, Baja California, ku Mexico

Chivomezichi chinachitikira pamalo omwe ali pa mtunda wa makilomita 18 kuchokera ku Guadalupe Victoria, m’dziko la Mexico, ndiponso mtunda wa makilomita 47 kuchokera ku Mexicali. Derali lili kutali kwambiri ndipo kumakhala anthu ochepa. Komabe, chivomezichi chinagwedeza kwambiri nthaka moti anthu anachimva m’mizinda yambiri ndi m’matawuni a ku Mexico ndiponso kum’mwera kwa dziko la United States.

May 9: Chivomezi Champhamvu Zokwana 7.2, Kumpoto kwa Sumatra, ku Indonesia

Chivomezichi chinachitika 12 koloko masana ndipo chinachitikira pansi pa nyanja, pa mtunda wa makilomita 217 kuchokera mu mzinda wa Banda Aceh, umene uli kumpoto kwambiri kwa dziko la Indonesia. Anthu ambiri anathawa m’nyumba zawo ndipo kwa nthawi ndithu ankakana kubwereranso chifukwa cha mantha. Koma akuti palibe amene anafa.

Tiyembekezerenso Zivomezi Zina

Popeza kuyambira kale, zivomezi zikuluzikulu zakhala zikuchitika padzikoli, m’pomveka kunena kuti tiyenera kuyembekezera zinanso m’zaka zikubwerazi. Bungwe loona za nthaka ndi miyala ku America linanena mosapita m’mbali kuti: “Zivomezi zikuluzikulu zipitirizabe kuchitika monga momwe zakhala zikuchitikira m’mbuyo monsemu.”

N’zochititsa chidwi kuti nyuzipepala ina posachedwapa inanena kuti: “Zivomezi zomwe zakhala zikuchitika pakatipa . . . n’zoti anthu sakanatha kuzipewa, ndipo zikungotikumbutsa za kuperewera kwa mphamvu za anthu. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti tisamachite zinthu zomwe tingathe kuti tidziteteze . . . , koma zikutanthauza kuti tiyenera kuyembekezera kuti kuzichitika masoka akuluakulu achilengedwe amene sitingathe kuwapewa.”

Anthu amene amaphunzira Baibulo mwakhama akaona zimenezi amakumbukira za maulosi a m’Baibulo amene amatchula mwachindunji kuti zivomezi ndi mbali imodzi ya chizindikiro cha masiku otsiriza a nthawi yathu ino.—Mateyu 24:3, 7; Maliko 13:8; Luka 21:11.

[Mapu pamasamba 2021]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Zina mwa zivomezi zamphamvu zokwana 7.0 kapena kuposa zomwe zachitika kuyambira mu January mpaka May chaka chino

Mexico

Haiti

Chile

Japan

Indonesia

Solomon Islands