Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwana Akamabadwa Pamachitika Zodabwitsa

Mwana Akamabadwa Pamachitika Zodabwitsa

Mwana Akamabadwa Pamachitika Zodabwitsa

MAYI wakhala ali woyembekezera kwa miyezi 9 ndipo tsopano nthawi yakuti mwana abadwe yakwana. * Khomo la chiberekero lakhala lili lotseka nthawi yonseyi, zomwe zathandiza kuti mwana akhale wotetezeka m’chiberekeromo. Koma tsopano minofu ya khomo la chiberekero yapyapyala, yafewa ndipo yayamba kutseguka. Kenako zimene zichitike n’zodabwitsa kwambiri.

Kodi n’chiyani chimachitika kuti mwana ayambe kubadwa? Pali zinthu zambiri, koma ziwiri n’zimene zili zodabwitsa kwambiri. Choyamba, ubongo umatulutsa mankhwala enaake (ubongo wa amuna umatulutsanso mankhwala amenewa koma ochepa). Pa nthawi imene mayi woyembekezera watsala pang’ono kubereka, ubongo wake umatulutsa mankhwala amenewa ochuluka zedi ndipo zikatero matenda amayamba. Zimenezi zimachititsa kuti khomo la chiberekero liyambe kutseguka ndipo chiberekerocho chimayamba kukungika n’kumakankha mwanayo.

Sizikudziwika kuti ubongo wa mayi woyembekezera umadziwa bwanji kuti nthawi yotulutsa mankhwala aja yakwana. Buku lina linati: “Mwanjira inayake ubongo wa mayi umadziwa kuti masiku akwana ndipo tsopano ndi nthawi yakuti chiberekero chigwire ntchito yake . . . yomwe imakhala ya kanthawi kochepa koma yofunika kwambiri.”—Incredible VoyageExploring the Human Body.

Chinthu chachiwiri chochititsa chidwi chimene chimachitika mwana akamabadwa n’chokhudzana ndi nsengwa. Nthawi yoti mwana abadwe ikakwana, nsengwa imasiya kutulutsa mankhwala enaake. Pa nthawi imene mayi ali woyembekezera, mankhwala amenewa ndi amene amachititsa kuti chiberekero chisamakungike kwambiri. Koma tsopano chiberekerochi chimayamba kukungika n’kumakankha mwana chifukwa chakuti nsengwa yasiya kutulutsa mankhwalawa. Nthawi zambiri pakadutsa maola 8 mpaka 13 kuchokera pamene matenda ayamba, mwana uja amayamba kutuluka pa khomo la chiberekero, limene limakhala litatseguka. Mwana akamaliza kutuluka, nsengwa ija imatulukanso.

Tsopano mwanayo amafunika kuzolowera moyo wina, womwe ndi wosiyana kwambiri ndi moyo umene iye anazolowera ali m’mimba mwa amayi ake. Mwachitsanzo, nthawi imene mwanayo ali m’chiberekero, m’mapapo ake mumadzaza madzi a m’chiberekero, omwe amatuluka okha mwanayo akamadutsa m’njira ya mwana. Koma akabadwa, m’mapapo mumayenera kulowa mpweya umene umathandizira kuti mwanayo azipuma. Monga chizindikiro chakuti wayamba kupuma, mwanayo amalira kwambiri. Mtima wake komanso mitsempha yodutsa magazi zimasintha kwambiri. Bowo limene limalumikiza mapampu awiri am’mwamba a mtima ndi mtsempha wodutsa magazi zimatsekeka, n’cholinga choti magazi asinthe njira imene amadzera n’kuyamba kufika m’mapapo. Zimenezi zimathandiza kuti magazi azitenga mpweya wa okosijeni. N’zodabwitsa kwambiri kuti zonsezi zimachitika mofulumira kwambiri mwanayo akangobadwa.

Zonse zimene zimachitika kuyambira pa kuyamba kwa matenda mpaka kubadwa kwa mwana, zimatikumbutsa mawu a m’Baibulo awa: “Chilichonse chili ndi nthawi yake, ndipo chilichonse chochitika padziko lapansi chilidi ndi nthawi yake.” Zimenezi zimaphatikizapo “nthawi yobadwa.” (Mlaliki 3:1, 2) N’zosakayikitsa kuti inunso mukuona kuti zinthu zodabwitsa zimene zimachitika kwa maola ochepa pamene mwana akubadwa, zimasonyeza kuti tinalengedwa mwanzeru kwambiri ndi Mlengi, amene Baibulo limati ndi “kasupe wa moyo.”—Salimo 36:9; Mlaliki 11:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Nthawi zambiri mayi woyembekezera amabereka pakadutsa milungu 37 mpaka 42.

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Zimene Zimachitika Mwana akamabadwa

1 Mmene mwana amakhalira matenda asanayambe

2 Mmene mwana amayendera akamabadwa

3 Khomo la chiberekero latseguka

4 Mwana akubadwa

[Chithunzi]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

1

nsengwa

njira ya mwana

khomo la chiberekero

2

3

4