Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Ngati Muli ndi Matenda a Pulositeti

Zimene Mungachite Ngati Muli ndi Matenda a Pulositeti

Zimene Mungachite Ngati Muli ndi Matenda a Pulositeti

“Pamene ndinali ndi zaka 54, ndinayamba kukodza pafupipafupi, mwina pa mphindi 30 zilizonse. Zimenezi zinandichititsa kuti ndipite kuchipatala. Kuchipatalako anandiuza kuti ndikufunika kuchotsedwa kachiwalo kotchedwa pulositeti.” Nkhani ngati zimenezi sizachilendo m’zipatala zambiri padziko lonse. Kodi munthu angatani kuti apewe matenda a pulositeti? Ndipo kodi ndi nthawi iti imene amafunika chithandizo chakuchipatala?

PULOSITETI ndi kachiwalo kooneka ngati mtedza kamene kamakhala m’munsi mwa chikhodzodzo ndipo kamakuta mtsempha wonyamula mkodzo. (Onani chithunzi.) Nthawi zambiri, kachiwaloka kamalemera magalamu 20, ndipo kamakhala kakakulu masentimita anayi m’litali mwake, masentimita atatu m’lifupi mwake, ndi masentimita awiri kuchoka kona yam’mwamba kukafika kona yam’munsi yakumbali ina. Ntchito yake n’kutulutsa timadzi timene timapanga pafupifupi 30 peresenti ya umuna. Timadzi timeneti timakhala ndi mankhwala osiyanasiyana monga kashamu, asidi winawake, ndi mankhwala ena. Timadziti mwina timathandiza kuti umuna uziyenda mosavuta komanso kuti ukhale wamphamvu. Komanso, timadzi ta mu pulositeti timakhalanso ndi zinki, amene asayansi amati amateteza ku matenda opatsirana okhudza ziwalo zoberekera.

Kodi Mungadziwe Bwanji Ngati Pulositeti Ili ndi Matenda?

Pulositeti ikatupa kapena ikachita khansa, nthawi zambiri munthu amatentha thupi, amamva kupweteka pokodza, ndiponso amamva kupweteka m’chiuno kapena m’chikhodzodzo. Ngati pulositeti yatupa kwambiri, wodwalayo amalephera kukodza. Ndipo ngati pulositetiyo yatupa chifukwa cha bakiteriya, munthuyo akhoza kudwala kwambiri komanso sachira mwamsanga. Kawirikawiri nthenda yotereyi imayamba chifukwa chakuti mtsempha wonyamula mkodzo wagwidwa ndi matenda. Koma matenda a pulositeti amene anthu ambiri amadwala sadziwika bwinobwino kuti amayamba bwanji.

Zizindikiro zodziwika bwino za matenda a pulositeti ndi kukodza pafupipafupi, kutulukatuluka usiku, kukodza pang’onopang’ono, ndiponso kumva ngati mkodzo sunatheretu m’chikhodzodzo. Nthawi zambiri zizindikiro zimenezi zimangosonyeza kuti pulositeti yatupa koma osati ili ndi khansa. Nthawi zambiri matendawa amakhudza amuna a zaka zoposa 40. Matendawa amakonda kugwira anthu omwe ayamba kukalamba. Mwachitsanzo, pa amuna 100 alionse a zaka 55, amuna 25 ndi amene amadwala matendawa, koma pa amuna 100 alionse a zaka 75, amuna 50 ndi amene amadwala matendawa.

Pulositeti imathanso kuchita khansa. Nthawi zambiri madokotala amatulukira kuti munthu ali ndi khansa ya pulositeti akayeza pulositetiyo, ndipo nthawi zambiri anthu amene amawapeza ndi khansayi amakhala kuti samamva zizindikiro zilizonse za matendawa. Khansayi ikafika podetsa nkhawa, wodwalayo amalephera kukodza ndipo chikhodzodzo chake chimatupa. Khansayo ikagwiranso ziwalo zina, munthuyo amamva kupweteka msana, thupi lake limaphwanya, ndiponso miyendo yake imatupa chifukwa cha kutsekeka kwa mitsempha inayake imene imanyamula madzi m’thupi. M’chaka chinachake posachedwapa, dziko la United States lokha linalengeza kuti anthu pafupifupi 300,000 anayamba kudwala khansa ya pulositeti ndipo anthu 41,000 anamwalira ndi khansayo. Asayansi akuti pa amuna 100 alionse a zaka zapakati pa 60 ndi 69, amuna 30 adzadwala khansa ya pulositeti ndipo pa amuna 100 alionse a zaka za pakati pa 80 ndi 89, amuna 67 adzadwala khansa imeneyi.

Kodi Matendawa Amagwira Ndani Kwenikweni?

Kafukufuku akusonyeza kuti munthu akapitirira zaka 50, zimakhala zosavuta kuti adwale khansa ya pulositeti. Ku United States, anthu akuda amadwala kwambiri khansa imeneyi kuposa azungu, kuwirikiza kawiri. M’mayiko ena khansayi ndi yofala kwambiri kuposa ena. Mwachitsanzo, ku North America kuli anthu ambiri odwala matendawa kuposa ku Ulaya, ku South America anthu odwala matendawa ndi ocheperapo, ndipo ku Asia n’kumene kuli anthu ochepa kwambiri odwala matendawa. Zimenezi zikusonyeza kuti dziko limene munthu akukhala komanso zakudya zimachititsa kuti anthu ena adwale khansayi. Ngati munthu atapita kudziko kumene matendawa ndi ofala, akhoza kudwala mosavuta khansayi.

Kwa munthu amene ali ndi achibale amene anadwalapo matendawa, zimakhala zosavuta kuti nayenso adwale matendawa. Bungwe la American Cancer Society linati: “Ngati munthu ali ndi abambo kapena achimwene ake amene anadwalapo matendawa, zimakhala zosavuta kuti iyenso adwale matendawa.” Zinthu zina zimene zimachititsa kuti munthu adwale matendawa ndi zaka za munthu, fuko lake, dziko lake, ngati wachibale wake anadwalapo matendawa, zakudya, komanso kusachita masewera olimbitsa thupi. Anthu amene amadya zakudya zamafuta kwambiri ndipo sachita masewera olimbitsa thupi, akhoza kudwala mosavuta khansayi.

M’mene Mungapewere Matenda a Pulositeti

Ngakhale kuti asayansi sadziwa bwinobwino chimene chimayambitsa khansa ya pulositeti, iwo akuganiza kuti munthu amachita kutengera kwa makolo komanso amayamba chifukwa cha timadzi tinatake tam’thupi. Komabe tikhoza kupewa matendawa ngati titamadya chakudya choyenerera komanso kuchita masewera olimbitsa thupi. Bungwe la American Cancer Society linanena kuti munthu akhoza kupewa matendawa ngati “atachepetsa kudya zakudya zamafuta ambiri ndiponso atamadya zakudya zochokera kumunda.” Bungweli linanenanso kuti munthu angapewe matendawa ngati atamayesetsa “kudya ndiwo zamasamba komanso zipatso kasanu kapena kuposa pamenepo tsiku lililonse.” Zinthu monga buledi, nsima ya mgaiwa, mpunga, nyemba ndi zakudya zina zotero zimathandiza kwambiri kuti munthu asadwale matendawa. Tomato, mphesa, ndi mavwende zimathandiza kuti DNA isawonongeke ndiponso zingathandize kuchepetsa vuto la khansa ya pulositeti. Akatswiri ena amatinso zomera zina komanso mavitamini ena amathandiza.

Mabungwe a American Cancer Society ndi American Urological Association amanena kuti kupita kuchipatala pafupipafupi kukayezetsa n’kothandiza kwambiri chifukwa munthu amatha kuchira khansayo akaipeza mwamsanga. Bungwe la American Cancer Society limati n’zothandiza kwambiri kuti amuna a zaka zoposa 50, kapena zoposa 45 ngati ali m’gulu la anthu amene ali pangozi kwambiri, azipita kukayezetsa chaka chilichonse. *

Madokotala amayeza zinthu zosiyanasiyana kuti adziwe ngati munthu ali ndi khansa ya pulositeti. Mwachitsanzo, nthawi zina amayeza magazi kuti aone ngati ali ndi mapulotini enaake amene amapangidwa ndi maselo a pulositeti. Ngati m’magazi muli mapulotini amenewa ambiri, madokotala amadziwa kuti munthuyo ali ndi matenda a pulositeti. Bungwe la American Cancer Society linanena kuti: “Ngati munthu atapezeka kuti ali ndi mapulotini ambiri m’magazi mwake, ayenera kufunsa dokotala kuti adziwe kuti vuto lake ndi lalikulu bwanji komanso ngati angafunikire kuyezedwanso zinthu zina kuti aone ngati angadwale khansa.” Nthawi zinanso madokotala angadziwe ngati munthu ali ndi matenda a pulositeti polowetsa chala chawo kotulukira chimbudzi kuti aone ngati pali malo alionse otupa. (Onani chithunzi patsamba 13.) Ngati kuyeza kuwiri konseku kwasonyeza kuti penapake sipali bwino, madokotala amaona ngati angafunikire kutenga kachidutswa ka pulositeti n’kukakayeza kuti atsimikiziredi ngati munthuyo ali ndi matenda a pulositeti. Kuyeza kumeneku kumatenga pafupifupi mphindi 20.

Kuyeza pulositeti chaka ndi chaka kumathandiza kuti madokotala apeze ngati munthu ali ndi khansa. Kumathandizanso kuti apeze mwamsanga ngati pulositeti yatupa. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti matendawo awatulukire mwamsanga asanafike poopsa kwambiri. Makhalidwe abwino amateteza munthu kuti asadwale matenda opatsirana kudzera m’chiwerewere, amene angayambitse matenda a pulositeti.

Ndithudi pulositeti yanu iyenera kutetezedwa ndi kusamalidwa. Munthu amene tinamutchula kumayambiriro kwa nkhani ino uja ananena kuti anachiriratu atachitidwa opaleshoni. Iye akuona kuti zingakhale bwino ngati “amuna onse atamakayezetsa pulositeti kuchipatala chaka ndi chaka,” ngakhale alibe zizindikiro zilizonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Ngati muli ndi zaka zoposa 45, mungachite bwino kuwerenga zimene zili m’bokosi lakuti “Zizindikiro za Pulositeti Yotupa.”

[Bokosi patsamba 14]

Zizindikiro za Pulositeti Yotupa

Malangizo: Yankhani mafunso ali m’munsiwa polemba mzera wozungulira nambala ya yankho lanu.

Mafunso 1-6 ayenera kuyankhidwa motere:

0—Palibiretu

1—Osafika kamodzi pa maulendo asanu

2—Osafika theka la nthawi yonse

3—Pafupifupi theka la nthawi yonse

4—Kuposa theka la nthawi yonse

5—Pafupifupi nthawi zonse

1. M’mwezi wapitawu, kodi mutatha kukodza, ndi kangati pamene munamva ngati simunamalize kukodza? 0 1 2 3 4 5

2. M’mwezi wapitawu, kodi zinachitika kangati kuti mutamaliza kukodza, munkafunanso kukodza pasanathe maola awiri? 0 1 2 3 4 5

3. M’mwezi wapitawu, kodi ndi kangati pamene munaona kuti mwamaliza kukodza koma kenako n’kuyambanso kukodza, ndipo n’kuchita zimenezi maulendo angapo? 0 1 2 3 4 5

4. M’mwezi wapitawu, kodi ndi kangati pamene munaona kuti zinakuvutani kupirira kuti musakodze? 0 1 2 3 4 5

5. M’mwezi wapitawu, kodi ndi kangati pamene mkodzo wanu unkatuluka pang’onopang’ono pokodza? 0 1 2 3 4 5

6. M’mwezi wapitawu, kodi ndi kangati pamene munachita kudzikakamiza kuti muyambe kukodza? 0 1 2 3 4 5

7. M’mwezi wapitawu, kodi mumadzuka kangati usiku kukakodza kuyambira nthawi imene munapita kukagona mpaka nthawi imene munadzuka m’mawa? 0 1 2 3 4 5

Chiwonkhetso cha manambala amene mwazungulizawo ndi chizindikiro chosonyeza kukula kwa matenda anu. 0-7: Vuto likungoyamba kumene. 8-19: Lafika pakatikati. 20-35: Lafika podetsa nkhawa.

[Mawu a Chithunzi]

Kuchokera ku bungwe la American Urological Association

[Bokosi patsamba 15]

Mafunso Amene Mungafunse Dokotala Wanu Musanachitidwe Opaleshoni

1. Kodi mukufuna kuti ndipangidwe opaleshoni yamtundu wanji?

2. Kodi n’chifukwa chiyani ndikufunika opaleshoni imeneyi?

3. Kodi pali chithandizo china chimene ndingapatsidwe m’malo mwa opaleshoni?

4. Kodi ubwino wa opaleshoniyo ndi wotani?

5. Kodi kuopsa kochitidwa opaleshoniyo ndi kotani? (Mwachitsanzo, kutaya magazi kwambiri kapena kusabereka.)

6. Kodi pangakhale mavuto otani ngati n’tapanda kuchitidwa opaleshoniyi?

7. Kodi ndi kuti kwina kumene ndingakafunse kuti nditsimikiziredi kuti ndikufunika opaleshoni?

8. Kodi munachitapo opaleshoni imeneyi popanda kuika munthu magazi?

9. Kodi opaleshoni yake idzachitidwira kuti? Kodi madokotala ndi manesi ake amalemekeza ufulu wa wodwala pankhani ya kuikidwa magazi?

10. Kodi ndi mankhwala ati ogonetsa tulo amene ndidzafunikira kupatsidwa? Kodi dokotala kapena nesi amene adzandipatse mankhwala amenewo amatha kuwagwiritsa ntchito pa opaleshoni yopanda kuika munthu magazi?

11. Kodi ndidzatenga nthawi yaitali bwanji kuti ndichire?

12. Kodi ndidzafunika kulipira ndalama zingati kuti ndichitidwe opaleshoniyo?

[Chithunzi patsamba 13]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Chithunzi chosonyeza pamene pulositeti imakhala

Chikhodzodzo

Pulositeti

Potulukira chimbudzi

Mtsempha wodutsa mkodzo