Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Pachithunzipa Pakusoweka Chiyani?

Werengani 2 Mafumu 4:8-10. Tsopano yang’anani chithunzichi. Kodi pakusoweka chiyani? Lembani mayankho anu pamizere ili m’munsiyi. Kenako jambulani mzere wolumikiza madontho amene ali pachithunzichi kuti muchimalizitse, kenako muchichekenire.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

[Chithunzi]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

KAMBIRANANI:

Kodi mzimayiyu anasonyeza bwanji kukoma mtima? Kodi Yehova anamudalitsa bwanji chifukwa chokomera mtima mneneri wake?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mafumu 4:32-37.

Kodi inuyo mungakomere bwanji mtima atumiki a Yehova masiku ano?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Aroma 12:13; Agalatiya 6:10.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Popanda kutulutsa mawu, munthu wina m’banja lanu ayerekezere kuti ndi mmodzi wa anthu a munkhani ya m’Baibulo ili pamwambayi. Ena nonsenu muone ngati mungathe kudziwa munthu amene akumuyerekezerayo.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 2 DANIELI

MAFUNSO

A. N’chifukwa chiyani Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango?

B. Kodi anzake atatu a Danieli mayina awo achiheberi anali ndani?

C. Kodi Danieli anagwira ntchito mu ulamuliro wa maufumu awiri ati omwe ankalamulira padziko lonse?

[Tchati]

4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.

Kulengedwa Anakhala ndi moyo Baibulo linamalizidwa

kwa Adamu cha m’ma 600 B.C.E kulemba

[Mapu]

Kutengedwa ku Yerusalemu kupita ku Babulo

Yerusalemu

Babulo

DANIELI

ANALI NDANI?

Zikuoneka kuti anali mwana wa mfumu ndipo anabadwira m’fuko la Yuda. Anali mneneri wokhulupirika amene anauziridwa kulemba buku la m’Baibulo lomwe limadziwika ndi dzina lake. Mwina Danieli anali ndi zaka zapakati pa 13 ndi 19 pamene iye limodzi ndi anthu ena a m’banja lachifumu ndiponso anthu ena olemekezeka, anagwidwa ndi Nebukadinezara n’kupita ku ukapolo ku Babulo.

MAYANKHO

A. Iye ankapemphera kwa Yehova ngakhale kuti lamulo linaletsa zimenezi.—Danieli 6:6-17.

B. Hananiya, Misayeli, Azariya.—Danieli 1:6, 7.

C. Babulo komanso Mediya ndi Perisiya.—Danieli 5:30; 6:8.

Anthu ndi Mayiko

4. Mayina athu ndi Jorge, Nicolas, ndi Priscilian. Timakhala ku Belize. Dzikoli lili ku Central America. Kodi ku Belize kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko pafupifupi 600, 2,000, kapena 3,500?

5. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ifeyo timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Belize.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

● Mayankho a Mafunso a Patsamba 30 ndi 31 pa tsamba 28

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Bedi.

2. Tebulo.

3. Mpando.

4. 2,000.

5. A.