Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

3—Muzichita Masewera Olimbitsa Thupi

3—Muzichita Masewera Olimbitsa Thupi

3​—Muzichita Masewera Olimbitsa Thupi

“Masewera olimbitsa thupi akanakhala mankhwala, bwenzi akuperekedwa kwa anthu ambiri kuposa mankhwala alionse,” inatero nkhani ina yolembedwa kuyunivesite yophunzitsa za mankhwala ya Emory, ku America. Pa zinthu zonse zimene tingachite kuti tikhale ndi thanzi labwino, n’zochepa zimene zingakhale zothandiza kwambiri kuposa kuchita masewera olimbitsa thupi.

Muzichita zinthu zokhetsa thukuta. Kuchita zinthu zina ndi zina zokhetsa thukuta kungatithandize kuti tizikhala osangalala, tiziganiza bwino, tikhale amphamvu, ndiponso kuti tizigwira ntchito molimbika. Komanso kudya zakudya zoyenera, kungatithandize kuti tisanenepe kwambiri. Kuti tikhale athanzi, sizilira kuchita masewera olimbitsa thupi mopitirira malire moti mpaka kumamva kupweteka. Chofunika kwambiri n’kuchita mosadumphadumpha ndiponso maulendo angapo mlungu uliwonse.

Kuthamanga, kuyenda ndawala, kupalasa njinga ndiponso kuchita nawo masewera ena ndi ena olimbitsa thupi, omwe angachititse mtima wanu kugunda mofulumira ndiponso kukuchititsani kutuluka thukuta, kumathandiza kuti mukhale amphamvu komanso kuti mupewe matenda a mtima ndiponso opha ziwalo. Kuphatikiza masewera olimbitsa thupi ngati amenewa ndi masewera ena onyamula zitsulo ndiponso ena ndi ena olimbitsa mbali zosiyanasiyana za thupi, kumalimbitsa mafupa, minofu ya m’kati mwa thupi, miyendo, ndi manja. Masewera amenewa amathandizanso kuti thupi lanu lizigwira ntchito bwino kwambiri, komanso kuti musanenepe kwambiri.

Muziyendako nthawi zina. Masewera olimbitsa thupi amathandiza anthu a misinkhu yonse, ndipo simuchita kufunikira kukhala membala wa malo enaake ochitira masewera olimbitsa thupi kuti muyambe. Mukhoza kuyamba n’kuyenda wapansi m’malo mokwera galimoto, basi, kapena chikepi. Ngati kumene mukupita si kutali kwambiri, bwanji osangoyenda m’malo modikirira galimoto kapena basi? Mwina mukhozanso kukafika msanga kuposa amene akuyenda pa galimotowo. Makolo, muzilimbikitsa ana anu kusewera ndi anzawo, ndipo muziwalimbikitsa kusewera panja ngati zingatheke. Masewera amenewa amalimbitsa matupi awo ndipo amawathandiza kuphunzira kugwiritsira ntchito bwino mbali zosiyanasiyana za thupi lawo. Koma masewera ochita atangokhala pansi, monga masewera a pakompyuta, sangawathandize mwanjira imeneyi.

Kaya muli ndi zaka zingati pa nthawi imene mukufuna kuyamba kuchita masewera olimbitsa thupi, dziwani kuti masewerawa angakuthandizeni kwambiri. Ngati ndinu wokalamba, mumadwala matenda enaake, kapena mwakhala musakuchita masewera olimbitsa thupi, ndi bwino kukaonana kaye ndi dokotala musanayambe. Pambuyo poonana ndi dokotala, yambani. Kuyamba pang’onopang’ono ndiponso mosapitirira malire kungathandize ngakhale anthu okalamba kuti akhale amphamvu. Kungathandizenso anthu okalamba kuti asamangogwa chisawawa.

Masewera olimbitsa thupi ndi amene anathandiza Rustam, yemwe tamutchula m’nkhani yoyambirira ija. Zaka 7 zapitazo, iye ndi mkazi wake anayamba kumathamanga kwa nthawi yochepa m’mawa uliwonse, masiku asanu pa mlungu. Rustam anati: “Poyamba tinkapeza tizifukwa tolepherera kukathamanga. Koma kupita kokathamanga tili awiri kunatithandiza kuti tizilimbikitsana. Panopa tinazolowera ndipo timasangalala kwambiri tikamathamanga.”

[Chithunzi patsamba 6]

Mukhoza kumasangalala ndi masewera olimbitsa thupi