Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Zikomo Kwambiri Chifukwa Chondisonyeza Atate Wachikondi”

“Zikomo Kwambiri Chifukwa Chondisonyeza Atate Wachikondi”

“Zikomo Kwambiri Chifukwa Chondisonyeza Atate Wachikondi”

● Mtsikana wina wa zaka 19 amene amakhala kum’mwera kwa dziko la United States analemba kuti: “Ndinakulira m’banja lachikhristu ndipo ndinamulandira Khristu kukhala Mpulumutsi wanga. Koma kwa zaka zambiri ndakhala ndikuopa kuti Mulungu adzandilanga pondiwotcha kumoto. Kenako ndinayamba kuwerenga buku lanu lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

“Nditangowerenga machaputala ochepa, ndinayamba kukhala ndi mtendere wamumtima. Ndinamva ngati kuti njovu inanditsamira pachifuwa ndipo tsopano yachoka. Panopa ndikutha kuona kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi, wokoma mtima, komanso wachifundo. Iye amafuna kuti ndikhale naye paubwenzi, osati ndiziopa kuti adzandilanga. Lamlungu likubwerali ndikufuna ndipite ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Ndikungoona kuchedwa kuti tsikuli lifike. Zikomo kwambiri pondisonyeza Atate wachikondi, osati amene amawotcha anthu kumoto.”

Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani lilinso ndi nkhani zina zofunika kwambiri. Zina mwa nkhanizi n’zokhudza zimene zimachitika munthu akamwalira, chiyembekezo chakuti akufa adzauka, zimene tingachite kuti tikhale ndi banja losangalala, zoona zake zokhudza Mulungu ndi Yesu Khristu, ndiponso chifukwa chimene Mulungu walolera kuti anthu azivutika. Kuti muitanitse bukuli, lembani zofunika m’munsimu ndipo tumizani ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.