Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Imfa Yovuta Kwambiri Kuiwala

Imfa Yovuta Kwambiri Kuiwala

Imfa Yovuta Kwambiri Kuiwala

Nicolle anali kamtsikana kathanzi. Koma tsiku lina madzulo anayamba kudandaula kuti mutu ukumupweteka, choncho makolo ake anamutengera kuchipatala. Madzulo a tsiku lotsatira madokotala akumuyeza, Nicolle anadwala mwadzidzidzi matenda a mtima. Atamuyezanso zinthu zina anapeza kuti mapapo ake, impso komanso mtima wake zinali ndi matenda. Pasanathe masiku awiri, Nicolle anamwalira. Pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka zitatu zokha.

ZIMAKHALA zopweteka kwambiri munthu amene timamukonda akamwalira. Ndipo nthawi zambiri zimavuta kuiwala. Mwachitsanzo, mayi ake a Nicolle, a Isabelle, anati: “Zimandivuta kuiwala imfa ya mwana wanga Nicolle. Zimandipweteka ndikakumbukira nthawi imene ndinkamunyamula m’manja komanso kumukumbatira. Ndimakumbukira kuti tsiku lililonse ankabwera kwa ine atatenga maluwa m’manja n’kundipatsa. Nthawi zonse ndimaganiza za Nicolle.”

Kodi nanunso muli ndi wachibale amene anamwalira? N’kutheka kuti mwana wanu, mkazi kapena mwamuna wanu, mchimwene kapena mchemwali wanu, kapenanso mnzanu wa pamtima anamwalira. Ngati ndi choncho, kodi mungatani kuti muiwale?