Kodi Mulungu Ali Paliponse?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Mulungu Ali Paliponse?
ANTHU ambiri amakhulupirira kuti Mulungu amapezeka paliponse. Koma Solomo, mmodzi wa anthu amene analemba nawo Baibulo, anapemphera kwa Yehova kuti: “Mumve muli kumalo anu okhala, kumwamba.” (1 Mafumu 8:30, 39) Choncho, mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, Yehova ali ndi malo okhala. Solomo ananena kuti Yehova amakhala “kumwamba.” Koma kodi kumwamba kumene Mulungu amakhalako n’kuti?
Nthawi zina Baibulo likamanena za kumwamba limatanthauza kumwamba kumene timakuonaku ndi zinthu zonse zimene zili kumwambako. (Genesis 2:1, 4) Komabe, popeza kuti Mulungu ndi amene analenga zonse, malo ake okhala ayenera kuti analipo kale asanalenge kumwamba kumeneku. Choncho, Baibulo likamanena kuti Yehova Mulungu amakhala kumwamba, silitanthauza kumwamba kumene timakudziwaku, koma malo enaake auzimu.
Masomphenya Ochititsa Chidwi
Baibulo limafotokoza za masomphenya ochititsa chidwi amene Yohane anaona osonyeza malo amene Yehova amakhala. M’masomphenyawo Yohane anaona khomo lotseguka kumwamba kenako anamva mawu akuti: “Kwera kumwamba kuno.”—Chivumbulutso 4:1.
Kenako m’masomphenyawo iye anaona zinthu zinanso zochititsa chidwi kwambiri. Zina mwa zimene anaona ndi izi: “Mpando wachifumu unaoneka uli pamalo ake kumwamba, . . . Wokhala pampandoyo, anali wooneka ngati mwala wa yasipi, ndi mwala wofiira wamtengo wapatali. Utawaleza wooneka ngati mwala wa emarodi unazungulira mpando wachifumuwo. . . . Kumpando wachifumuko kunali kutuluka mphezi, mawu, ndi mabingu. . . . Patsogolo pa mpando wachifumuwo, panali nyanja yoyera mbee! ngati galasi, yooneka ngati mwala wa kulusitalo.”—Chivumbulutso 4:2-6.
Masomphenya amenewa akufotokoza bwino kwambiri mphamvu zimene Yehova ali nazo komanso kukongola kwa malo amene iye amakhala. Ndipo masomphenyawa akutithandiza kudziwa zinthu zimene zili kumpando wachifumu wa Yehova. Mwachitsanzo, utawaleza umasonyeza kuti kumalo kumene Yehova amakhala kuli mtendere wokhawokha. Mphezi, mawu ndi mabingu zimasonyeza mphamvu za Mulungu. Nyanja yoyera mbee ngati galasi imasonyeza kuti onse amene amayandikira mpando wachifumu wa Yehova ndi oyera.
Ngakhale kuti awa anali masomphenya chabe, akutithandiza kudziwa zambiri zokhudza malo amene Yehova amakhala. Mwachitsanzo, masomphenyawo amasonyeza kuti kumwamba kumachitika zinthu zadongosolo ndiponso kuti kulibe chisokosonezo.
Kodi Mulungu Amapezeka Kulikonse, Nthawi Iliyonse?
Mfundo yakuti Yehova ali ndi malo okhala ikusonyeza kuti sapezeka kulikonse nthawi iliyonse. Ndiye kodi amadziwa bwanji zimene zikuchitika? (2 Mbiri 6:39) Iye amadziwa pogwiritsa ntchito mzimu woyera kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito. Wamasalimo analemba kuti: “Ndingapite kuti kuthawa mzimu wanu, ndipo ndingapite kuti kuthawa nkhope yanu? Ngati ndingakwere kumwamba, inu mudzakhala komweko. Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda, taonani! inunso mudzakhala komweko.”—Salimo 139:7-10.
Kuti mumvetse mmene mzimu woyera wa Mulungu umagwirira ntchito, ganizirani za dzuwa. Dzuwa limakhala pamalo amodzi koma mphamvu yake imafika kumadera ambiri padziko lapansi. Mofanana ndi zimenezi, Yehova Mulungu ali ndi malo amodzi amene amakhala. Koma amatha kuchita chilichonse chimene akufuna kuchita kulikonse m’chilengedwechi. Kuwonjezera pamenepa, 2 Mbiri 16:9 limati: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.”
Yehova amagwiritsanso ntchito mzimu wake kuti adziwe zimene zikuchitika kulikonse, pa nthawi iliyonse. N’chifukwa chake lemba laMulungu amagwiritsanso ntchito angelo omwe ndi zolengedwa zake zauzimu. Baibulo limasonyeza kuti angelo alipo mamiliyoni ambirimbiri, mwinanso mabiliyoni ambirimbiri. * (Danieli 7:10) M’Baibulo muli nkhani zambiri zonena za angelo amene ankatumidwa ndi Mulungu kuti akachite zinthu zosiyanasiyana. Limanena za angelo amene anabwera padziko lapansi, kulankhula ndi anthu, n’kubwerera kumwamba kukafotokoza kwa Mulungu zimene apeza. Mwachitsanzo, m’nthawi ya Abulahamu, Mulungu anatuma angelo kuti akafufuze zimene zinkachitika m’mizinda ya Sodomu ndi Gomora, iye atamva kudandaula kwa anthu. Atamva zimene angelowo anapeza, Mulungu anawononga mizindayo.—Genesis 18:20, 21, 33; 19:1, 13.
Choncho, zimene Baibulo limanena zikusonyeza kuti palibe chifukwa choti Yehova Mulungu azipezeka paliponse. Iye amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera ndi angelo ake kuti adziwe zonse zimene zikuchitika m’chilengedwe chake.
Choncho mukhoza kuona kuti Baibulo limatithandiza kuti tim’dziwe bwino Mlengi wathu. Limatiuza kuti Mulungu amakhala kumalo auzimu kumwamba. Kumwamba kumene iye amakhala kulinso angelo amphamvu miyandamiyanda. Kumwambako zinthu zonse zimayenda bwino moti kulibe chisokonezo. Malo amene iye amakhala amasonyeza kuti ndi wamphamvu komanso woyera. Baibulo limatitsimikizira kuti nthawi ikadzakwana, padziko lapansi padzakhala mtendere ngati mmene kulili kumwamba.—Mateyu 6:10.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 13 Lemba la Chivumbulutso 5:11 limanena za angelo “miyanda kuchulukitsa ndi miyanda” amene azungulira mpando wachifumu wa Mulungu. Mwanda umodzi ndi 10,000. Ndiye 10,000 kuchulukitsa ndi 10,000 zimapanga 100 miliyoni. Koma onani kuti lembali likugwiritsa ntchito mawu akuti “miyanda kuchulukitsa ndi miyanda,” kusonyeza kuti chiwerengerochi chikhoza kukhala chachikulu kuposa 100 miliyoni.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
● Kodi Mulungu ali paliponse?—1 Mafumu 8:30, 39.
● Kodi mzimu woyera umagwira ntchito bwanji?—Salimo 139:7-10.
[Mawu Otsindika patsamba 29]
Dzuwa limakhala pamalo amodzi koma mphamvu yake imafika kumadera ambiri padziko lapansi. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu ali ndi malo amodzi amene amakhala. Koma mzimu wake woyera umatha kufika kulikonse kumene iye akufuna