Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chiyani Chingakuthandizeni Ngati Mwaferedwa?

N’chiyani Chingakuthandizeni Ngati Mwaferedwa?

N’chiyani Chingakuthandizeni Ngati Mwaferedwa?

“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.”—Salimo 34:18.

NGATI wachibale wanu wamwalira, mungasokonezeke maganizo. Mwina mungamadandaule kwambiri, mungamadziimbe mlandu komanso mungamakhale wokwiya kwambiri. Monga tinafotokozera m’nkhani yapitayi, imfa imakhudza anthu mosiyanasiyana. Choncho mwina pa zimene tafotokozazi, si zonse zimene zingakuchitikireni komanso mwina simungasonyeze chisoni mofanana ndi anthu ena. Koma dziwani kuti sikulakwa kusonyeza chisoni.

“Ngati Mukufuna Kulira, Lirani”

Heloisa, dokotala yemwe tinamutchula uja, anayesetsa kwambiri kuti asasonyeze kuti ali ndi chisoni mayi ake atamwalira. Iye anati: “Mayi atangomwalira ndinalira, koma kenako ndinkadzikakamiza kuti ndisalire. Ndinkayesetsa kuchita zimenezi chifukwa n’zimenenso ndinkachita wodwala amene ndimamusamalira akamwalira. Koma zimenezi zachititsa kuti ndisakhale ndi thanzi labwino. Malangizo anga kwa anthu amene aferedwa ndi akuti: ‘Ngati mukufuna kulira, lirani. Kulira kungakuthandizeni kuti mupezeko bwino.’”

Komabe, m’kupita kwa nthawi mungamamve ngati mmene ankamvera Cecília, yemwe mwamuna wake anamwalira ndi khansa. Iye anati: “Nthawi zina ndimakhumudwa kwambiri chifukwa ndimaona kuti chisoni changa chikuchedwa kutha. Chimene chimachititsa kuti ndikhumudwe kwambiri n’chakuti anthu amayembekezera kuti panopa ndikanakhala nditaiwala kalekale za imfayo.”

Ngati inunso mumakhala ndi maganizo amenewa, kumbukirani kuti anthu amasonyeza chisoni mosiyanasiyana ndipo palibe njira yabwino kwambiri yosonyezera chisoni. Ena chisoni chawo sichichedwa kutha, pamene ena chimatenga nthawi. Choncho musadzipanikize. Si bwino kudziikira tsiku loti chisoni chanu chidzakhale chitatha. *

Koma bwanji ngati chisoni chanu sichikutha, ndipo thanzi lanu likuwonongeka chifukwa cha nkhawa? Mwina mungamamve ngati mmene ankamvera Yakobo, munthu wolungama amene atauzidwa kuti mwana wake Yosefe wamwalira, ‘ankakana kutonthozedwa.’ (Genesis 37:35) Ngati inunso chisoni chanu sichikutha, kodi n’chiyani chimene mungachite kuti moyo wanu usasokonekere?

Samalirani thanzi lanu. Cecília, anati: “Nthawi zina ndimamva kuti ndatopa kwambiri ndipo zikatere ndimadziwa kuti zimenezi zachitika chifukwa chodandaula mopitirira malire.” Zimene Cecília ananenazi zikusonyeza kuti chisoni chimatha kusokoneza kwambiri thanzi komanso maganizo athu. Choncho, muyenera kusamalira kwambiri thanzi lanu. Muzionetsetsa kuti mukugona mokwanira komanso mukudya chakudya choyenera.

N’kutheka kuti simungafune kudya, kukagula zinthu kumsika kapena kuphika ndipo m’pake kutero. Komabe kunyalanyaza kudya zakudya zoyenera kungachititse kuti muzidwaladwala ndipo zimenezi zingangowonjezera nkhawa yanu. Choncho, muziyesetsa kudya ngakhale pang’ono chabe kuti mukhale ndi thanzi labwino. *

Ngati n’kotheka, muzichita zinthu zina ndi zina zokuthandizani kulimbitsa thupi lanu, ngakhale kungoyenda chabe. Zinthu zimenezi zingakuthandizeni kuti musamangokhala m’nyumba. Ndiponso kuchita zinthu zolimbitsa thupi mosapitirira malire kumathandiza kuti ubongo wanu uzitulutsa makemiko enaake amene amathandiza munthu kumva bwino.

Lolani kuti ena akuthandizeni. Zimenezi n’zofunika kwambiri makamaka ngati amene wamwalirayo anali mkazi kapena mwamuna wanu. Mwina pali ntchito zimene mnzanuyo ankachita ndipo panopa ntchitozo sizikugwiridwa. Mwachitsanzo, ngati mkazi kapena mwamuna wanu ankaona kayendetsedwe ka ndalama kapena ntchito zapakhomo, koyambirira zingamakuvuteni kugwira ntchito zimenezi. Pa zinthu zoterezi, malangizo anzeru a anzanu angakuthandizeni kwambiri.—Miyambo 25:11.

Baibulo limafotokoza kuti bwenzi lenileni ‘linabadwira kuti litithandize pakagwa mavuto.’ (Miyambo 17:17) Choncho, musamadzipatule chifukwa choopa kuti muwalemetsa anzanuwo. Iwo angakuthandizeni kuiwala. Mayi wina wachitsikana, dzina lake Sally, anaona kuti kucheza ndi ena kunamuthandiza kwambiri mayi ake atamwalira. Iye anati: “Anzanga ambiri ankandiitana akakhala ndi zochitika zosiyanasiyana. Zimenezi zinandithandiza chifukwa poyamba ndinkasungulumwa kwambiri. Ndinkamvako bwino anzanga akamandifunsa mafunso monga akuti, ‘Panopa n’chiyani chikukuthandiza kuti uiwale imfa ya mayi ako?’ Ndinaona kuti kufotokoza za mayi anga kunandithandiza kuti ndisamakhale ndi chisoni chachikulu.”

Sikulakwa kuganizira zakale. Muziyesa kuganizira zinthu zakale zimene munkachitira limodzi ndi munthu womwalirayo. Mwina mungakumbukire zinthu zakalezo poyang’ana zithunzi. N’zoona kuti poyamba, kuganizira zinthu ngati zimenezi kungamakupwetekeni koma m’kupita kwa nthawi zingakuthandizeni kuti chisoni chanu chichepe.

Mungayesenso kukhala ndi buku lolembamo zinthu zosangalatsa zimene zinachitika pa moyo wanu. M’bukuli mungalembemonso zinthu zimene mukuona kuti mukanachita bwino kumuuza munthu womwalirayo pa nthawi imene anali moyo. Kulemba m’buku zinthuzo kungakuthandizeni kuti muzimvetsa zimene zikukuchitikirani. Kulemba kungakuthandizeninso kuti chisoni chanu chichepe.

Nanga bwanji kusunga zinthu zokukumbutsani munthu womwalirayo? Anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani imeneyi, ndipo zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa anthu amakhudzidwa ndi imfa mosiyanasiyana. Ena amaganiza kuti kusunga zinthu ngati zimenezi kungawachititse kuti asaiwale mwamsanga imfa ya munthuyo pamene ena amaona kuti zimawathandiza kwambiri. Sally, yemwe tinamutchula kale uja, anati: “Ndimasunga zinthu zambirimbiri zimene zinali za mayi anga. Kuchita zimenezi kumandithandiza kupirira imfa yawo.” *

Muzidalira “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” Baibulo limati: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.” (Salimo 55:22) Kupemphera n’kofunika kwambiri chifukwa kumakuthandizani kulankhulana ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.”—2 Akorinto 1:3, 4.

Mawu a Mulungu, Baibulo, amatitonthoza kwambiri. Mtumwi Paulo anati: “Ndili ndi chiyembekezo mwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Kuganizira za chiyembekezo chimene Baibulo limapereka chakuti akufa adzauka kumatitonthoza kwambiri tikaferedwa. * Lauren, yemwe mchimwene wake anamwalira pa ngozi ya galimoto asanakwanitse zaka 20, anaona kuti Baibulo ndi lothandiza kwambiri. Iye anati: “Kaya ndikhumudwe bwanji, ndinkayesetsa kutenga Baibulo n’kuwerenga ngakhale vesi limodzi lokha. Ndinkakonda kuwerenga mavesi otonthoza, ndipo ndinkawawerenga mobwerezabwereza. Mwachitsanzo, mawu amene Yesu anauza Marita pa imfa ya Lazaro amandilimbikitsa kwambiri. Yesu anamuuza Marita kuti: ‘Mlongo wako adzauka.’”—Yohane 11:23.

“Pewani Kumangoganizira za Imfayo”

Ngakhale kuti n’zovuta, kuyesetsa kuiwala imfa ya munthu amene munkamukonda n’kofunika kwambiri kuti muyambirenso kuchita zinthu zofunika pa moyo wanu. Kuchita zimenezi sikutanthauza kuti simunkamukonda munthuyo kapena kuti mwamuiwaliratu. Zoona zake n’zakuti mulimonse mmene zingakhalire simudzamuiwaliratu munthuyo. Nthawi ndi nthawi mungamakumbukire zinthu zimene zingakuchititseni kuti mukhale ndi chisoni chachikulu, komabe m’kupita kwa nthawi zoterezi zingadzachepe.

Mungathenso kumasangalala mukakumbukira zinthu zina zimene zinachitika munthuyo asanamwalire. Mwachitsanzo, Ashley amene tinamutchula m’nkhani yapita ija, anati: “Ndimakumbukira zimene zinachitika pa tsiku limene mayi anga anamwalira. Anayamba kupezako bwino ndipo ngakhale kuti sankadzuka pa bedi, tsiku limenelo anadzuka. Ndimakumbukira kuti mkulu wanga ankawapesa tsitsi, ndipo ineyo, iyeyo ndi mayi athuwo tinkakambirana nkhani inayake yosangalatsa n’kumaseka. Kenako ndinaona mayi anga akumwetulira. Ndinasangalala kwambiri chifukwa kwa nthawi yaitali ndinali ndisanawaone atasangalala choncho. Ankaoneka kuti akusangalala kwambiri kucheza ndi ana awofe.”

Mungathenso kumakumbukira zinthu zofunika kwambiri zimene munaphunzira kwa munthuyo asanamwalire. Mwachitsanzo, Sally anati: “Mayi anga anali munthu wodziwa kuphunzitsa. Popereka malangizo ankayesetsa kuti asatikhumudwitse ndipo anandiphunzitsa ineyo kuchita zinthu mwanzeru pamene ndikusankha zochita. Iwo sankakonda kuti tizingotsatira zimene iwowo ndi bambo anena.”

Kukumbukira zinthu zokhudza munthu amene anamwalirayo kungakuthandizeni kuti mupitirizebe kukhala munthu wosangalala. Mnyamata wina dzina lake Alex, anaona kuti zimenezi n’zoona. Iye anati: “Bambo anga atamwalira, ndinkayesetsa kwambiri kutsatira zimene anandiphunzitsa. Ali moyo iwo ankakonda kunena kuti osamataya nthawi n’kudandaula. Kwa amene mayi kapena bambo awo anamwalira, ndingawalangize kuti: “N’zosatheka kuiwaliratu imfa ya mayi kapena bambo anu, koma si bwino kumangokhalira kudandaula. Lirani mmene mungathere koma musaiwale kuti mufunikiranso kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni pa moyo wanu.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Munthu amene mumam’konda akamwalira, ndi bwino kupewa kuchita zinthu mopupuluma, monga kusamukira nyumba ina kapena kuganiza zokwatiranso. Muyenera kuchita zinthu zimenezi patapita nthawi yokwanira.

^ ndime 10 Ngakhale kuti kumwa mowa kungachititse kuti muiwaleko imfa ya munthu amene mumam’konda, dziwani kuti mowa ndi wosathandiza kwenikweni. Mowa umangokuthandizani kuiwala kwa nthawi yochepa koma m’kupita kwa nthawi, sungakuthandizeninso ndipo mukhoza kukhala ndi chizolowezi chodalira mowa.

^ ndime 16 Popeza kuti anthu amakhudzidwa ndi imfa mosiyanasiyana, si bwino kuti achibale kapena anzake a munthu woferedwayo azimuuza zochita pa nkhani imeneyi.—Agalatiya 6:2, 5.

^ ndime 18 Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene zimachitika munthu akamwalira komanso lonjezo la Mulungu lakuti akufa adzauka, onani mutu 6 ndi 7 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

“Kaya ndikhumudwe bwanji, ndinkayesetsa kutenga Baibulo n’kuwerenga ngakhale vesi limodzi lokha”—Anatero Lauren

[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]

MUSAMADZIIMBE MLANDU

Mwina mukuganiza kuti munthuyo sakanafa mukanayesetsa kuchita zinazake. Kaya zimene mukuganizazo n’zoona kapena ayi, simungapeweretu maganizo amenewa ndipo nthawi zina maganizo amenewa angakuthandizeni kuti muchepetse nkhawa. Komabe musamangosunga maganizo amenewa mumtima mwanu. Kuuza anthu ena mmene mukumvera kungakuthandizeni kwambiri.

Koma dziwaninso kuti ngakhale titamukonda kwambiri munthu winayo, tilibe mphamvu yoletsa kuti zinthu zina zisachitike pa moyo wake komanso sitingaletse ‘nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka kumugwera.’ (Mlaliki 9:11) Komanso n’zosakayikitsa kuti inuyo munalibe cholinga chakuti munthuyo amwalire. Mwachitsanzo, ngati munachedwa kumupititsa kuchipatala, si ndiye kuti munali ndi cholinga chakuti amwalire. Choncho palibe chifukwa choganizira kuti mwamupha ndinu.

Mayi wina amene mwana wake anafa pa ngozi ya galimoto anaona kuti si bwino kumangodziimba mlandu. Iye anati: “Ndinkaona kuti sindinachite bwino kumulola kuti apite ndi bambo ake kokagula zinthu. Koma kenako ndinaona kuti si bwino kuganiza choncho chifukwa ngozi ndi ngozi basi.”

Koma mwina munganene kuti, ‘Ndikanachita zakuti, zimenezi sizikanachitika.’ Mwina zimenezi zingakhale zoona, koma kumbukirani kuti palibe munthu amene samalakwitsa zinazake. Baibulo limatikumbutsa kuti: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri. Ngati wina sapunthwa pa mawu, ameneyo ndi munthu wangwiro.” (Yakobo 3:2; Aroma 5:12) Choncho vomerezani mfundo yakuti inuyo si munthu wangwiro. Kumangokhalira kunena kuti, ‘Ndikanatere, ndikanatere,’ n’kosathandiza ndipo kungangochititsa kuti zikuvuteni kwambiri kuiwala. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 36 Mawu amene ali m’bokosili achokera m’kabuku kakuti, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 6]

Nthawi zina kholo lokalamba lingafunike kutonthoza mwana wake wachikulire amene waferedwa

[Zithunzi patsamba 9]

Kulemba mmene mukumvera, kuona zithunzi komanso kulola kuti anthu ena akuthandizeni kungachititse kuti muiwale imfa ya munthu amene munkamukonda