Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Sindinkafuna Kulisiya”

“Sindinkafuna Kulisiya”

“Sindinkafuna Kulisiya”

● Achinyamata osiyanasiyana padziko lonse akuyamikira buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri. * Taonani zimene ena ananena:

“Ndimalikonda kwambiri bukuli chifukwa limathandiza achinyamatafe kuti tizilankhulana momasuka ndi makolo athu. Ndimayesetsa kutsatira malangizo ake, ndipo panopa sizindivuta kukambirana ndi makolo anga.”—Anatero Roberto, wa ku Mexico.

“Nditayamba kuwerenga bukuli, sindinkafuna kulisiya. Ndimakonda kwambiri mbali yakuti ‘Zoti Ndichite!’ yomwe imapezeka pafupi ndi kumapeto kwa mutu uliwonse, ndi mbali yakuti ‘Mfundo Zanga’ yomwe imapezeka kumapeto kwa chigawo chilichonse. Bukuli landithandiza kwambiri kuti ndikakhala kusukulu, ndisamaope kufotokoza mfundo zimene ndimakhulupirira.”—Anatero Joelah, wa ku United States.

“Nthawi zonse pamene ndawerenga bukuli, mfundo zake zimandikhudza kwambiri. Ndimachita chidwi kwambiri ndi mawu amene achinyamata ambiri m’bukuli ananena, ndiponso ndi bokosi lakuti ‘Kodi Mukudziwa . . . ?’ komanso lakuti ‘Mfundo Yothandiza.’ Bukuli likusonyezeratu kuti Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limatikonda achinyamatafe.”—Anatero Hui-won, wa ku South Korea.

“Pa mabuku onse amene atulutsidwa ndi Mboni za Yehova, buku limeneli ndi limene limandisangalatsa kwambiri. Inuyo mumadziwadi zimene achinyamata amaganiza ndiponso mavuto amene amakumana nawo kunyumba, kusukulu komanso akamacheza ndi anzawo.”—Anatero Shana, wa ku Canada.

“Nthawi zonse makolo anga akakangana, ndinkapita kuchipinda kwanga n’kuyamba kulira. Koma nditawerenga mutu 24, wakuti ‘Kodi Ndingatani Makolo Anga Akamakangana?,’ ndinafotokozera makolo angawo mmene ndimamvera akamakangana. Iwo anadabwa kudziwa kuti zinkandipweteka kwambiri. Choncho, nawonso anawerenga mutu umenewu. Panopa amandimvetsa kusiyana ndi kale, ndipo anachepetsa kwambiri zokangana.”—Anatero Mariana, wa ku Czech Republic.

“Nkhani za m’bukuli zakuti ‘Chitsanzo Chabwino’ zandikhudza kwambiri ndipo zandithandiza kuti ndiyesetse kukonza mbali zimene sindichita bwino. Mwachitsanzo, zimandivuta kuti ndidziwane bwino ndi anthu atsopano amene abwera kumpingo kwathu chifukwa choopa kuti ndiyambira pati. Koma patsamba 97 la bukuli pali nkhani ya Lidiya amene anadziwana bwino ndi Paulo ndi anzake chifukwa chowaitanira kunyumba kwake. Panopa ndimayesetsa kutsatira chitsanzo chake.”—Anatero Mónika, wa ku Hungary.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 25]

“N’CHIFUKWA CHIYANI SI BWINO KUGONANA MUSANAKWATIRANE?”

Katrina, mtsikana wazaka 16 wa ku United States, anauzidwa ndi aphunzitsi ake kuti akapereke lipoti m’kalasi pa nkhani iliyonse imene wasankha. Iye anagwiritsa ntchito buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri. Lipoti lakelo linali ndi mutu wakuti, “N’chifukwa Chiyani si Bwino Kugonana Musanakwatirane?” Makolo ake anati: “M’lipoti lake, Katrina anafotokoza tanthauzo la mawu akuti ‘kupewa.’ Anafotokozanso kuopsa kogonana musanakwatirane, komanso zinthu zosiyanasiyana zoopsa zimene munthu angakumane nazo chifukwa chophwanya malamulo a Mulungu okhudza makhalidwe abwino. Katrina anawerenganso zimene achinyamata ena otchulidwa m’bukuli ananena, zokhudza mmene anamvera pambuyo pakuti aphwanya malamulo a Mulungu. Kenako iye anapereka mwayi kwa ana a sukulu anzake woti afunse mafunso ndipo iye anakwanitsa kuyankha mafunsowo. Atamaliza kupereka lipoti lakeli, aphunzitsi ake anamulembera kakalata, komwe mwa zina kanati: ‘Zikomo kwambiri ponena choonadi komanso chifukwa chotitsegula m’maso. Pitirizabe kutsatira kwambiri zimene umakhulupirirazi.’”