Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Chithunzichi Chalakwika Pati?

Werengani Esitere 5:9–6:14. Tchulani zinthu zitatu zomwe zalakwika pachithunzichi. Lembani mayankho anu m’munsimu. Ndipo malizitsani kujambula chithunzichi komanso chikongoletseni ndi chekeni.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi n’chifukwa chiyani Hamani ankadana ndi Moredekai?

Zokuthandizani: Werengani Esitere 5:9.

Kodi mtima wodzikuza unachititsa Hamani kuganiza chiyani?

Zokuthandizani: Werengani Esitere 6:6.

Kodi n’chiyani chinachitikira Hamani?

Zokuthandizani: Werengani Esitere 7:9, 10.

Kodi mungatani kuti musakhale ngati Hamani?

Zokuthandizani: Werengani Miyambo 16:18, 19; Yakobo 4:6.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Werengani pamodzi nkhaniyi m’Baibulo. Ngati n’kotheka, sankhani munthu mmodzi kuti akhale munthu wofotokoza nkhaniyo, wina akhale Hamani, ndipo wachitatu akhale Zeresi komanso atumiki, ndipo wachinayi akhale mfumu.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 4 ESITERE

MAFUNSO

A. Tchulani dzina la mkazi wa mfumu amene analowedwa m’malo ndi Esitere?

B. Malizitsani mawu a m’Baibulo awa: “Esitere anali kukondedwa ndi . . . ”

C. Lembani mawu oyenerera m’mipatayi. Dzina la Chiheberi la Esitere linali ․․․․․, ndipo msuweni wake wamkulu dzina lake ․․․․․, anakhala womuyang’anira.

[Tchati]

4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.

Kulengedwa

kwa Adamu Anakhala ndi Baibulo

moyo cha m’ma linamalizidwa

400 B.C.E. kulembedwa

[Mapu]

Esitere ankakhala ku Susani, mzinda wa ufumu wa Mediya ndi Perisiya

MEDIYA

Susani

PERISIYA

ESITERE

ANALI NDANI?

Mwana wamasiye amene anadzakhala mkazi wa mfumu Ahasiwero, ya ku Perisiya. Esitere anaika moyo wake pangozi poulula chiwembu chofuna kupha Ayuda onse. (Esitere 4:11, 15, 16) Kulimba mtima kwake, nzeru komanso mtima wogonjera zinali zofunika kwambiri kuposa kukongola kwake.—Esitere 2:7; 1 Petulo 3:1-5.

MAYANKHO

A. Vasiti.—Esitere 1:12; 2:16, 17.

B. “. . . aliyense womuona.”—Esitere 2:15.

C. Hadasa, Moredekai.—Esitere 2:7.

Anthu ndi Mayiko

4. Dzina langa ndine You-Jin. Ndili ndi zaka 7 ndipo ndimakhala m’dziko la Korea, ku Asia. Kodi mukudziwa kuti ku Korea kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 9,700, 37,900, kapena 96,600?

5. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ndimakhala? Jambulani mzere wozungulira kadonthoko, ndipo kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Korea.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

● Mayankho a mafunso a patsamba 30 ndi 31 ali patsamba 15.

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Moredekai anafunika kukwera hatchi ya mfumu, osati galeta.

2. Moredekai anafunika kuvala zovala zachifumu, osati zovala wamba.

3. Moredekai anayenda mkati mwa mpanda wa mzindawo, osati kunja kwake.

4. 96,600.

5. D.