Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kodi Anthu Saliwonongeratu Dziko Lapansili?”

“Kodi Anthu Saliwonongeratu Dziko Lapansili?”

“Kodi Anthu Saliwonongeratu Dziko Lapansili?”

● Munthu akakhala m’mlengalenga, amaona kuti dziko lapansili ndi lokongola kwambiri. Limaoneka ngati mpira wokhala ndi mwina moyera, mwina mwa buluu. Koma kwa munthu amene ali padzikoli amaona kuti lili pa mavuto aakulu. N’chifukwa chiyani dzikoli lili pa mavuto? Yankho lake ndi losavuta: Anthu akulephera kulisamalira. Anthu akuwononga dzikoli poipitsa mpweya ndi madzi, podula mitengo ndi zinthu zina zotero. Komanso kuwonjezera pamenepa, dziko lawonongeka chifukwa cha chiwawa, kuphana ndiponso chiwerewere.

Zinthu zokhumudwitsa zimenezi zinaloseredwa zaka 2,000 zapitazo, m’maulosi ochititsa chidwi kwambiri a m’Baibulo. (2 Timoteyo 3:1-5; Chivumbulutso 11:18) Baibulo linaloseranso kuti Mulungu, osati anthu, ndi amene adzakonze zinthu padziko lapansili. Mfundo zimenezi zidzafotokozedwa mwatsatanetsatane m’nkhani yakuti, “Kodi Anthu Saliwonongeratu Dziko Lapansili?” Nkhaniyi idzakambidwa pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa mutu wakuti, “Ufumu wa Mulungu Ubwere.” Ku United States msonkhanowu udzayamba m’mwezi wa May ndipo kenako udzachitika padziko lonse lapansi.

Mukuitanidwa kuti mudzapezeke pamsonkhano umene udzachitike kufupi ndi kwanu. Ngati mukufuna kudziwa zambiri, funsani Mboni za Yehova za m’dera lanu kapena lemberani kalata ofalitsa a magazini ino. Mungapezenso malo amene misonkhanoyi idzachitikire ku United States ndi ku Canada pa adiresi iyi: www.pr418.com.