Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Makhalidwe Amene Amatisiyanitsa ndi Nyama

Makhalidwe Amene Amatisiyanitsa ndi Nyama

Makhalidwe Amene Amatisiyanitsa ndi Nyama

TSIKU lina munthu wina wazaka 50 wogwira ntchito ya zomangamanga ankadikirira sitima pamalo ena okwerera sitima mumzinda wa New York. Mwadzidzidzi mnyamata wina yemwe anali pafupi anaterereka n’kugwera munjanji. Mmene zimenezi zimachitika n’kuti sitima ikubwera. Poona zimenezi, mkuluyo msangamsanga anam’thamangira mnyamatayo n’kumugwetsera pansi. Onse anagona pakati pa njanji ndipo sitimayo inawadutsa bwinobwino popanda kuwaponda.

Pa nthawi inanso pamene chipani cha Nazi chinkalamulira boma la Germany, Mboni za Yehova ku Ulaya zinkakana kunena mawu akuti “Heil Hitler!” chifukwa mawu achijeremani akuti “Heil” amatanthauza “mpulumutsi.” Iwo ankakhulupirira kwambiri kuti Yesu Khristu ndi Mpulumutsi wawo ndipo “chipulumutso sichipezeka mwa munthu wina aliyense” kupatulapo mwa iye. (Machitidwe 4:12) Chifukwa chokana kulambira Hitler, ambiri anaponyedwa kundende zozunzirako anthu. Komabe iwo anapitiriza kutsatira mfundo zawo zachikhristu kundendeko.

Zitsanzo ziwirizi zikusonyeza kuti anthu amalolera kufera anthu ena, mwina oti sakuwadziwa n’komwe, chifukwa chowakonda, komanso amalolera kuvutika chifukwa chofuna kutsatira mfundo zolondola. Tikaganizira zimene anthu amachitazi, kodi n’zomveka kunena kuti anthu anachita kusintha kuchokera ku nyama? Yesani kuyankha funso limeneli pamene mukuganizira mafunso otsatirawa:

● Kodi n’chifukwa chiyani anthufe tili ndi chikumbumtima, chimene chimatithandiza kudziwa kuti izi n’zolakwika, izi n’zabwino?

● N’chifukwa chiyani timachita chidwi kwambiri ndi zinthu zachilengedwe?

● N’chifukwa chiyani timasangalala tikamamvetsera nyimbo, tikaona chithunzi chokongola, tikamamvetsera ndakatulo komanso tikamaona zinthu zina zopangidwa mwaluso? Chifukwatu n’zotheka kukhala ndi moyo popanda zinthu zimenezi.

● N’chifukwa chiyani anthu, pafupifupi a zikhalidwe zonse, amakhala ndi mtima wofuna kulambira?

● N’chifukwa chiyani timakonda kufunsa kuti, ‘Kodi moyo wathu unayamba bwanji?’ ‘Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?’

● N’chifukwa chiyani munthu akamwalira, anthu amachita mwambo wamaliro?

● Nanga n’chifukwa chiyani pafupifupi anthu onse padzikoli amakhulupirira kuti tikamwalira, n’zotheka kudzakhalanso ndi moyo? Tikanakhala kuti anthufe tinachita kusintha kuchokera ku nyama, kodi bwenzi tili ndi maganizo ofuna kukhala ndi moyo kwamuyaya?

Kumene Mungapeze Mayankho

Mayankho ogwira mtima a mafunso amenewa amapezeka m’buku lofala kwambiri padziko lonse, Baibulo. Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhani zotsatirazi.

Makhalidwe athu. Anthu analengedwa ‘mu chifaniziro cha Mulungu,’ kutanthauza kuti anthufe timatha kusonyeza makhalidwe amene Mlengi wathu ali nawo. (Genesis 1:27) N’chifukwa chake munthu woyambirira, Adamu, ankatchedwa kuti “mwana wa Mulungu.”—Luka 3:38.

Anthufe timafuna kukondedwa. Lemba la 1 Yohane 4:8 limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi.” Popeza kuti tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, anthufe timafuna kukondedwa kungoyambira pamene tabadwa mpaka pa nthawi yomwalira. Mtumwi wachikhristu, Paulo, analemba kuti ngati “ndilibe chikondi, sindili kanthu.” (1 Akorinto 13:2) Iye ananenanso kuti: “Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.”—Aefeso 5:1.

Timafunika zinthu zauzimu. “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mateyu 4:4) “Mawu” a Yehova amenewa amapezeka m’Baibulo ndipo amatiuza za makhalidwe ake komanso cholinga chake potilenga. N’zosatheka kukhala ndi moyo wosangalala popanda kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu.

Chifukwa chake timafa. “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha.” (Aroma 6:23) Uchimo umatanthauza kuchita zinthu zotsutsana ndi mfundo komanso malamulo a Mulungu. Komabe, Mulungu ali ndi cholinga chodzachotseratu uchimo, kudalitsa anthu amene amamukonda ndi kumvera malamulo ake, ndiponso kuwapatsa moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi.—Salimo 37:10, 11, 29; Luka 23:43.

Kodi mumafuna kukhala ndi moyo wosangalala, mwinanso kuphunzira luso linalake lomwe mumalikhumbira kwambiri? Kodi mumafuna kudziwa zambiri zokhudza Mlengi wanu komanso za zinthu zimene iye akufuna kudzachitira anthu m’tsogolo? Ngati ndi choncho, tikukupemphani kuti muziphunzira Baibulo, lomwe ndi nkhokwe ya choonadi. Palibenso chinthu china chimene chingakuthandizeni kukhala wosangalala panopa komanso m’tsogolo kuposa kuphunzira Baibulo.—Mateyu 5:3; Yohane 17:3.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

TIMAFUNA KUKONDEDWA KUNGOYAMBIRA PAMENE TABADWA

Gerald L. Schroeder, anati: “Mwana amafunika kukondedwa kwambiri komanso kusamaliridwa kuti akule bwino.” Choncho, makolo ayenera kutsatira lamulo la m’Baibulo limene linaperekedwa, makamaka kwa azimayi, la “kukonda ana awo.”—Tito 2:4.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Timakonda zinthu zosiyanasiyana, ngakhale kuti tikhoza kukhala ndi moyo popanda zinthu zimenezi

[Chithunzi patsamba 9]

Chakudya ndi madzi n’zosakwanira kuti anthufe tikhale ndi moyo. Timafunikanso kutsogoleredwa ndi Mlengi wathu