Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Makolo Angachite Ngati Mwana Wawo Ali ndi Khansa

Zimene Makolo Angachite Ngati Mwana Wawo Ali ndi Khansa

Zimene Makolo Angachite Ngati Mwana Wawo Ali ndi Khansa

“Mwana wanga atapezeka ndi khansa, nzeru zinandithera. Ndinkaona ngati nthaka ikung’ambika ndipo ineyo ndikulowa pang’onopang’ono. Ndinali ndi chisoni chachikulu chifukwa ndinkaona ngati mwana wanga wafa kale.”—Anatero Jaílton, mwana wake atapezeka ndi khansa.

KUNENA zoona, kuuzidwa kuti mwana wanu ali ndi khansa kungakuchititseni mantha kwambiri. Kodi matendawa ndi ofala bwanji? Bungwe lina lolimbana ndi khansa linanena kuti, ngakhale kuti “khansa imakonda kugwira anthu akuluakulu, chaka chilichonse ana oposa 160,000 [padziko lonse] amapezeka ndi khansa. Ndipotu kupatula pa ngozi zapamsewu, khansa ndi imene imapha ana ambiri m’mayiko otukuka.” Mwachitsanzo, bungwe lina loona za khansa linanena kuti ku Brazil “ana oposa 9,000 amapezeka ndi khansa chaka chilichonse.”

Buku lina linanena kuti mwana akayamba kudwala khansa, “aliyense pabanja amakhudzidwa kwambiri.” (At the Bedside—The Mother and Child Cancer). Nthawi zambiri mwana akapezeka ndi khansa, amachitidwa opaleshoni komanso kupatsidwa mankhwala amphamvu kwambiri omwe amatha kuyambitsa mavuto ena. Ndipo makolo amasokonezeka maganizo, amakhala ndi mantha kwambiri, amakhala okhumudwa, amakhala ndi chisoni chachikulu, amadziimba mlandu ndiponso sakhulupirira kuti zachitika. Kodi makolo angatani ngati mwana wawo ali ndi khansa?

Chinthu chimodzi chimene chingawathandize kwambiri ndi kupeza madokotala abwino. Dokotala wina wa mumzinda wa New York, yemwe wathandiza anthu ambiri odwala khansa, anati: “[Madokotala abwino] amanena zinthu zolimbikitsa, komanso amafotokoza momveka bwino mavuto amene mungawayembekezere. Zimenezi zingathandize makolo kuti asakhale ndi mantha kwambiri.” Anthu enanso amene ana awo anadwalapo khansa angathandize makolo omwe ana awo akudwala matendawa. Pa chifukwa chimenechi, Galamukani! inafunsa mafunso makolo asanu otere amene amakhala ku Brazil.

Jaílton ndi Néia “Tinazindikira kuti mwana wathu ali ndi khansa ali ndi zaka ziwiri ndi theka.”

Kodi analandira chithandizo cha mankhwala kwa nthawi yaitali bwanji?

“Ankapatsidwa mankhwala enaake amphamvu kwambiri kwa zaka ziwiri ndi theka.”

Kodi mankhwalawo anali ndi vuto lililonse?

“Ankasanza kwambiri ndipo tsitsi lake linkathothoka. Mano ake ankathimbirira. Ndipo katatu konse anadwala kwambiri chibayo.”

Kodi pa nthawi imeneyi inuyo munkamva bwanji?

“Poyamba, tinkachita mantha chifukwa tinkaganiza kuti amwalira. Koma titaona kuti wayamba kusintha, tinalimba mtima kuti achira. Panopa ali ndi zaka pafupifupi 9.”

N’chiyani chinakuthandizani kuti musataye mtima?

“Tikuona kuti kudalira Yehova Mulungu n’kumene kunatithandiza kwambiri. Malinga ndi zimene Baibulo limanena pa 2 Akorinto 1:3, 4, iye ‘anatitonthoza m’masautso athu onse.’ Komanso anzathu a Mboni za Yehova anatithandiza kwambiri. Ankatilembera makalata otilimbikitsa, kutiimbira foni, kupemphera nafe ndiponso kutipempherera. Nthawi zinanso ankatipatsa ndalama. Nthawi ina mwana wathu atamusamutsa kuti azikalandirira mankhwala kuchipatala cha mumzinda wina, a Mboni anzathu kumeneko anatipatsa malo ogona komanso ankatipititsa kuchipatala mosinthanasinthana. Tikaganizira chithandizo chonse chimene anatipatsa, timasowa chonena.”

Luiz ndi Fabiana “Mu 1992, tinazindikira kuti mwana wathu ali ndi khansa yoopsa kwambiri imene imagwira akazi. Pa nthawiyi n’kuti iye ali ndi zaka 11.”

Kodi koyambirira kwenikweni munamva bwanji?

“Zinkativuta kuvomereza. Sitinkakhulupirira kuti mwana wathu ali ndi khansa.”

Kodi kuchipatala anamuthandiza bwanji?

“Anamuchita opaleshoni komanso anamupatsa mankhwala amphamvu omwe ankamufoola kwambiri, ndipo zimenezi zinachititsa kuti ifeyo tizingokhala okhumudwa. Kawiri konse anadwala kwambiri chibayo. Ulendo wachiwiriwo anatsala pang’ono kufa. Analinso ndi vuto lomangotuluka magazi pakhungu ndi m’mphuno ndipo ankati akayamba sankasiya. Atalandira mankhwala vutoli linachepa.”

Kodi analandira chithandizo cha mankhwala kwa nthawi yaitali bwanji?

“Kuyambira pamene anamupeza ndi matendawa mpaka pamene anamaliza kulandira mankhwala amphamvu kwambiri, zinatenga pafupifupi miyezi 6.”

Kodi mwana wanu anamva bwanji atapezeka ndi khansa?

“Poyambirira penipeni sankadziwa kuti chikuchitika ndi chiyani. Dokotala anamuuza kuti ali ndi ‘chotupa m’mimba chofunika kuti amuchotse.’ Kenako mwana wathuyu anazindikira kuti vutolo ndi lalikulu. Iye anandifunsa kuti, ‘Bambo, kodi ndili ndi khansa?’ Ndinavutika kwambiri kuti ndimuyankha bwanji.”

Kodi munkamva bwanji kuona mwana wanu akuvutika?

“N’zovuta kufotokoza ululu umene tinkamva mumtima mwathu. Zinali zopweteka kuona mwana wathu akuthandizana ndi nesi kupeza mtsempha woti am’baye mankhwala amphamvu kwambiri. Zikafika povuta kwambiri ndinkapita kubafa kukalira komanso kupemphera. Usiku wina ndinasokonezeka kwambiri maganizo moti ndinapempha Yehova kuti ndingofa ineyo m’malo mwa mwana wangayo.”

N’chiyani chinakuthandizani kuti musataye mtima?

“Akhristu anzathu anatithandiza kwambiri, ena ankatiimbira foni kuchokera kutali kwambiri. Tsiku lina m’bale wina atandiimbira foni anandipempha kuti nditenge Baibulo. Kenako iye anatiwerengera mosangalala mavesi angapo a m’buku la Masalimo. Mavesi amene anawerengawo ndi amene ine ndi mkazi wanga tinkafunikira kwambiri. Pa nthawiyi n’kuti mwana wathu atadwala kwambiri chifukwa cha mankhwala amene amalandira.”

Rosimeri “Mwana wanga anali ndi zaka zinayi pamene anamupeza ndi khansa.”

Kodi koyambirira kwenikweni munamva bwanji?

“Zinkandivuta kukhulupirira. Ndinkalira usana ndi usiku ndiponso ndinkapempha Mulungu kuti andithandize. Mwana wanga winanso ankakhumudwa kwambiri kuona mchemwali wake akudwala kwambiri. Chifukwa cha zimenezi, ndinamutumiza kwa mayi anga kuti azikakhala komweko.”

Kodi mankhwala amene ankalandira anali ndi mavuto alionse?

“Ankalandira mankhwala amphamvu kwambiri tsiku lililonse zomwe zinkachititsa kuti magazi ake azichepa. Chifukwa cha zimenezi madokotala ankamupatsa mankhwala owonjezera magazi. Tinkada nkhawa kwambiri magazi ake akachepa. Nthawi zinanso ankakomoka.”

Kodi analandira chithandizo cha mankhwala kwa nthawi yaitali bwanji?

“Anapatsidwa mankhwala amphamvu kwambiri kwa zaka ziwiri ndi miyezi inayi. Pa nthawi imeneyi tsitsi lake linathothoka ndipo ananenepa kwambiri. Komabe timayamikira kuti sankadandaula kwambiri chifukwa chakuti anali wanthabwala. Patatha pafupifupi zaka 6 adokotala ananena kuti mwana wanga sakusonyezanso zizindikiro zilizonse za matendawa.”

Kodi n’chiyani chinakuthandizani kuti musataye mtima kwambiri pa nthawi yovuta imeneyi?

“Ine ndi mwana wanga tinkapemphera limodzi nthawi zambiri ndipo tinkakambirana za anthu okhulupirika a m’Baibulo amene anapirira mayesero osiyanasiyana. Mawu a Yesu a pa Mateyu 6:34 akuti tisamalole nkhawa za tsiku lotsatira kutisokonezera moyo wathu, anatithandiza kwambiri. Tinathandizidwanso kwambiri ndi Akhristu anzathu, anthu a m’Komiti Yolankhulana ndi Achipatala, ndiponso madokotala ndi manesi, amene amakumana ndi anthu odwala khansa nthawi zambiri.”

Kodi m’banja mwanu muli mwana amene akudwala khansa, kapena mukudziwa mwana winawake amene akudwala khansa? Ngati ndi choncho, zimene ena anenazi zingakuthandizeni kumvetsa kuti m’pake kumva chisoni kwambiri ngati mwana wapezeka ndi khansa. Ndipo mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, pali “nthawi yolira.” (Mlaliki 3:4) Komabe, dziwani kuti Mulungu woona, Yehova, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” adzakulimbikitsani ngati mutamuuza nkhawa zanu.—Salimo 65:2.

[Bokosi patsamba 13]

Malemba Amene Angakulimbikitseni

“Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.”—Mateyu 6:34.

“Atamandike Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.”—2 Akorinto 1:3, 4.

“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.

‘Mutulireni [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’—1 Petulo 5:7.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 14]

Makomiti Othandiza Kwambiri

Makomiti Olankhulana ndi Achipatala amene Mboni za Yehova zinakhazikitsa amathandiza kuti madokotala ndi odwala azimvana. Anthu a m’makomiti amenewa amathandiza anthu a Mboni za Yehova amene akudwala kuti apeze madokotala oyenera amene angawathandize popanda kugwiritsa ntchito magazi, potsatira lamulo la m’Baibulo lakuti ‘tizipewa magazi.’—Machitidwe 15:20.

[Chithunzi patsamba 13]

Néia, Sthefany ndi Jaílton,

[Chithunzi patsamba 13]

Luiz, Aline ndi Fabiana

[Chithunzi patsamba 13]

Aline ndi Rosimeri