Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Uchigawenga Udzatha Padzikoli?

Kodi Uchigawenga Udzatha Padzikoli?

Kodi Uchigawenga Udzatha Padzikoli?

“TIKUFUNIKA kuchita khama kwambiri . . . kuti tikwanitse kusintha mitima ndi maganizo a zigawenga.” Zimenezi ndi zimene akatswiri anaona kuti zingathandize, atafufuza moyo wa zigawenga zosiyanasiyana kwa zaka 20.

Koma kodi n’chiyani chingasinthe mitima ndi maganizo a anthu amene akhala akuchita zinthu zauchigawenga kwa zaka zambiri?

Buku Limene Limasintha Mitima ya Anthu

M’zaka za m’ma 1990, Hafeni anasintha moyo wake. Iye anayamba kuunikanso bwinobwino zinthu zimene ankakhulupirira ndipo anaganiza zoti apeze Baibulo. Hafeni anati: “Ndinayamba ndi kuwerenga nkhani za m’Mauthenga Abwino [Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane], zokhudza moyo wa Yesu. Powerenga nkhanizi ndinkachita chidwi kwambiri ndi umunthu wa Yesu, chifundo chake komanso moyo wake wopanda tsankho. Zimenezi zinandikhudza kwambiri.”

Hafeni anafotokozanso kuti: “Nditapitiriza kuwerenga Baibulo, lemba la Machitidwe 10:34 ndi 35 linandikhudza kwambiri.” Lembali limati: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”

Iye ananenanso kuti: “Ndinafika pozindikira kuti anthu, osati Mulungu, ndi amene amasokoneza mtendere chifukwa chosankhana mitundu. Ndinazindikiranso kuti uthenga wa m’Baibulo ukhoza kusintha mmene munthu amaganizira ndiponso kuti chinthu chofunika kwambiri pamoyo wathu ndi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Ndinaona kuti zimenezi ndi zofunika kwambiri kusiyana ndi kumenyera ufulu anthu a mtundu kapena fuko linalake.”

Joseba, yemwe tinamutchula m’nkhani yapita ija, anali mtsogoleri wa gulu linalake la zigawenga limene linakonza zokaphulitsa polisi inayake. Joseba ananena kuti: “Tisanakaphulitse polisiyo ndinamangidwa ndipo ndinakhala m’ndende zaka ziwiri.” Kenako mkazi wake, dzina lake Luci, anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Patapita nthawi nayenso Joseba anayamba kuphunzira nawo Baibulo.

Joseba akukumbukira kuti: “Pamene ndinkaphunzira zambiri zokhudza Yesu, m’pamenenso ndinkafuna kuti ndizimutsanzira. Mawu amene iye ananena akuti ‘onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga,’ anandigwira mtima kwambiri. Ndinakhulupirira kuti zimene ananenazo ndi zoona.” (Mateyu 26:52) Joseba anati: “Zimene zimachitika n’zakuti munthu akapha munthu mnzake, zimayambitsa chidani ndipo zimachititsa kuti achibale ake a munthuyo abwezere. Chiwawa chimabweretsa mavuto, osati mtendere.” Choncho Joseba anayamba kusintha moyo wake.

Anthu awiri onsewa, Hafeni ndi Joseba, anafika pozindikira kuti Baibulo lili ndi mphamvu yosintha moyo wa munthu. Baibulo limanena kuti “mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu” ndipo amathanso “kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” (Aheberi 4:12) Mawu a Mulungu athandiza anthu ambiri kusintha maganizo komanso zochita zawo. Koma kodi pali umboni uliwonse wosonyeza kuti anthu amene amatsatira zimene Baibulo limaphunzitsa amakhala mogwirizana?

Gulu Limene Anthu Ake Amagwirizana Kwambiri

Hafeni atayamba kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova, anachita chidwi kwambiri kuti anthu amitundu yosiyanasiyana ankakhala limodzi mogwirizana. Iye ananena kuti: “Kukhala moyandikana ndi mzungu chinali chinthu chosayembekezereka kwa ine. Sindinkaganiza kuti nthawi ina pa moyo wanga ndingatchule mzungu kuti m’bale wanga. Zimenezi zinanditsimikizira kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova ndi choona. Iwo ankagwirizana komanso ankakondana ngakhale kuti anali ochokera m’mitundu yosiyanasiyana. Zimenezi n’zimene ndinkalakalaka kwa nthawi yaitali.”

Yesu ananena kuti otsatira ake adzadziwika ‘akamakondana.’ (Yohane 13:34, 35) Iye anakana kulowerera m’mikangano ya ndale ndipo anawauza ophunzira ake kuti: “Simuli mbali ya dzikoli.” (Yoh. 6:15; 15:19; Mat. 22:15-22) Chikondi ndi kusalowerera ndale ndi zizindikiro za Akhristu oona masiku ano ngati mmene zinalili kalelo.

Kutsatira Zimene Yesu Anaphunzitsa

Koma kodi n’zotheka anthu kumakondana tikaganizira kuti masiku ano pali zinthu zambiri zimene zimagawanitsa anthu? Chifukwa chosiyana maganizo pa nkhani za ndale anthu a mitundu yosiyanasiyana amatha kudana kapena kuphana.

Mwachitsanzo, m’chaka cha 1914, maganizo a tsankho anachititsa mnyamata wina, dzina lake Gavrilo Princip, kupha Francis Ferdinand, yemwe amayembekezeka kukhala mfumu ya dziko la Austria ndi Hungary. Princip anali m’gulu la zigawenga lotchedwa Black Hand. Gululi linkanena kuti ukafuna kukwaniritsa zimene ukufuna, “uyenera kuchita zinthu zachiwawa m’malo motsatira mfundo za chikhalidwe.” Imfa ya Ferdinand inayambitsa nkhondo m’mayiko amene amati ndi achikhristu, zomwe zinachititsa kuti nkhondo yoyamba ya padziko lonse iulike. Nkhondoyi inaphetsa asilikali mamiliyoni ambiri, omwe ankanena kuti amatsatira Yesu, “Kalonga Wamtendere.”—Yesaya 9:6.

Nkhondoyo itatha, m’busa wina wodziwika kwambiri, dzina lake Emerson Fosdick, anadzudzula atsogoleri a matchalitchi achikhristu chifukwa cholephera kuphunzitsa anthu awo kutsanzira Yesu. Iye ananena kuti: “Taphunzitsa anthu kumenya nkhondo. Asilikali athu timawatamanda kuti ndi ngwazi zodziwa kumenya nkhondo, ndipo ngakhale m’matchalitchi mwathu taikamo mbendera zankhondo.” Fosdick anamaliza n’kunena kuti: “Mbali imodzi ya mlomo wathu taigwiritsa ntchito potamanda Kalonga Wamtendere, ndipo mbali ina taigwiritsa ntchito potamanda nkhondo.”

Mosiyana ndi zimene matchalitchi achikhristu amachita, lipoti la kafukufuku wina amene anafalitsidwa m’chaka cha 1975, linati: “Kuyambira kale, a Mboni za Yehova salowerera nkhondo. Iwo sanamenye nawo nkhondo ziwiri zikuluzikulu zimene zinachitika padziko lonse, komanso sanalowerere nawo pa mikangano ya ndale imene inkachitika nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itatha.” Ngakhale kuti anthu ambiri a Mboni za Yehova ankazunzidwa komanso kumangidwa, iwo “sankabwezera kapena kuchita zachiwawa zilizonse.” Lipotilo linamaliza ndi kuti: “Zimene Mboni za Yehova zimaphunzitsa n’zozikika pa mfundo yakuti Baibulo ndi mawu ouziridwa a Mulungu.”

Ubwino Wotsatira Zimene Baibulo Limanena

Munthu wina yemwe kale anali nduna yaikulu ya dziko la Belgium, anapatsidwa ndi munthu woyandikana naye nyumba buku lonena za moyo wa Yesu, lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ataliwerenga, iye anakhudzidwa kwambiri ndipo analembera kalata munthu amene anam’patsa bukulo, yomwe inati: “N’zoonekeratu kuti ngati anthu akanati aziwerenga zimene zili m’Mauthenga Abwino, n’kumayesetsa kutsatira mfundo zimene Yesu Khristu anaphunzitsa, dziko likanakhala losiyana kwambiri ndi mmene lililimu.”

Iye ananenanso kuti: “Si bwenzi pali magulu achitetezo komanso zinthu zachiwawa ndi zauchigawenga.” Komabe iye anamaliza ndi mawu akuti: “Zimenezi n’zongolakalaka chabe, sizingatheke.” Koma kodi n’zoona kuti sizingatheke? Ngakhale kuti masiku ano m’dziko mwadzaza chiwawa, Baibulo lathandiza anthu osiyanasiyana kusiya moyo wachiwawa komanso kuchotsa mkwiyo mumtima mwawo umene anali nawo chifukwa cha nkhondo.

Monga momwe tinafotokozera m’nkhani yoyambirira ija, Andre anatsala pang’ono kuphedwa ndi bomba lomwe linapha anthu ambiri odziwana nawo. Bombalo linatcheredwa ndi gulu linalake la zigawenga. Patapita nthawi, iye anaphunzira zimene Baibulo limanena zoti ‘tizikhululukirana ndi mtima wonse’ ndipo anayamba kutsatira malangizo amenewa. (Akolose 3:13) Kenako Hafeni, yemwe patapita zaka analowa m’gulu la zigawengazo, anaphunzira Baibulo ndipo anasiya zachiwawa. (Salimo 11:5) Panopa, Andre ndi Hafeni ndi a Mboni za Yehova. Iwo akugwira ntchito limodzi yomanga ofesi yomasulira mabuku ya Mboni za Yehova m’dziko linalake ku Africa.

Musakayikire Zoti Uchigawenga Udzatha

Anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse akuona kuti kuphunzira Baibulo kukuwathandiza kukhala ndi chiyembekezo. Mwachitsanzo, tsiku lina Andre ankakambirana ndi munthu wina woyandikana naye nyumba za lonjezo la m’Baibulo, lonena za dziko latsopano lachilungamo. (Yesaya 2:4; 11:6-9; 65:17, 21-25; 2 Petulo 3:13) Koma mwadzidzidzi asilikali okhala ndi zida zoopsa anazungulira nyumbayo n’kulamula kuti Andre atuluke n’cholinga choti amufunse mafunso okhudza nkhani zimene amalalikira. Ataona kuti Andre akuyamikiridwa kwambiri ndi munthu amene ankamuphunzitsayo, asilikaliwo anamusiya.

Pamene asilikali aja amafika panyumbapo, n’kuti Andre atangomaliza kumene kumufotokozera munthuyo kuti Mulungu adzakonza zinthu padzikoli ngati mmene anachitira m’nthawi ya Nowa pamene dziko “linadzaza ndi chiwawa.” (Genesis 6:11) Mulungu anawononga dziko pa nthawi imeneyo ndi madzi ndipo anapulumutsa munthu wokonda mtendere, Nowa, ndi banja lake. Kenako anamuuza munthuyo zimene Yesu ananena, kuti: “Monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire.”—Mateyu 24:37-39.

“Mwana wa munthu” amene akutchulidwa palembali ndi Yesu ndipo Mulungu anamusankha kuti akhale Mfumu ya Ufumu wake. Iye posachedwapa adzatsogolera magulu a nkhondo akumwamba podzachotsa zinthu zonse zoipa padziko lapansi. (Luka 4:43) Monga Mfumu yakumwamba, Yesu adzakomera mtima munthu aliyense. Komanso adzawombola anthu ake ku “chipsinjo ndi chiwawa.”—Salimo 72:7, 14.

Kenako, anthu onse amene amakonda chilungamo komanso amene adzakhala nzika za Ufumu wakumwamba, adzaona dziko likusintha kukhala paradaiso. (Luka 23:42, 43) Baibulo limalonjeza kuti mtendere ndi chilungamo zidzakhala pa mapiri ndi zitunda.—Salimo 72:1-3.

Kodi inuyo simungakonde kukhala m’dziko lolamulidwa ndi mfumu imeneyi? M’dziko limeneli simudzakhala zauchigawenga.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Anthu awiri onsewa, Hafeni ndi Joseba, anafika pozindikira kuti Baibulo lili ndi mphamvu yosintha moyo wa munthu

[Mawu Otsindika patsamba 9]

‘Ngati anthu akanati azitsatira mfundo zimene Yesu Khristu anaphunzitsa, dziko likanakhala losiyana kwambiri ndi mmene lililimu. Si bwenzi pali magulu achitetezo komanso zinthu zachiwawa ndi zauchigawenga.’—Nduna yaikulu yakale ya dziko la Belgium

[Chithunzi patsamba 8]

Kutsatira mfundo za m’Baibulo kwathandiza Hafeni ndi Andre kuti azikondana kwambiri