“Ndinangopitira Kukatenga Makalata Basi”
“Ndinangopitira Kukatenga Makalata Basi”
ANDRE, yemwe ndi mzungu wobadwira ku South Africa, koma amakhala ku Namibia, anati: “Sindidzaiwala zimene zinachitika tsiku lina m’mawa nditapita kukatenga makalata ku positi ofesi. Tsiku limeneli, pamalopa panadzaza anthu ambiri. Ndinaona chikwama chinachake chili poteropo chimene chimaoneka kuti chilibe mwiniwake. Ineyo ndinangotenga makalata anga n’kukwera galimoto kumapita. Nditangoyenda kwa mphindi zitatu zokha, ndinamva chiphokoso chachikulu. Phokosolo linali la bomba lomwe linaphulika m’positi ofesi muja.”
Andre anafotokoza kuti: “Ndinangopitira kukatenga makalata basi. Koma ndinachita mantha kwambiri nditamva kuti bomba lapha anthu osalakwa, ena owadziwa. Zimenezi zimandichititsabe mantha ngakhale kuti zinachitika zaka 25 zapitazo. Nthawi zina zimene zinachitikazo ndimaziona m’maganizo mwanga ndipo ndimaona kuti inenso ndinangotsala pang’ono kufa.”
Uchigawenga Ndi Vuto la Padziko Lonse
Zinthu ngati zimenezi zimachitika kwambiri m’madera osiyanasiyana padziko lapansi, ngakhale kuti mwina inuyo simunayambe mwazionapo zikuchitika. Anthu ambiri masiku ano akuchita zauchigawenga n’cholinga chokwaniritsa zofuna zawo.—Onani bokosi lakuti, “Kodi Zigawenga Zimatani?”
Mtolankhani wina atapanga kafukufuku anapeza kuti mu 1997, “mu mayiko anayi okha ndi mmene munkachitika nkhani zambiri zokhudza mabomba a tinkenawo.” Koma m’chaka cha 2008 mtolankhani yemweyu anapeza kuti, “mu mayiko oposa 30 padziko lonse, kupatulapo a ku Australia ndi ku Antarctica, munkachitika
nkhani zambiri zokhudza mabomba a tinkenawo.” Iye anamaliza n’kunena kuti “magulu amene amachita zauchigawenga akuwonjezereka ndipo zimenezi zikuchititsa kuti anthu ambiri aziphedwa chaka ndi chaka.”—The Globalization of Martyrdom.Ganizirani chiwembu chimene chinachitika ku positi ofesi chija. Anthu amene anatchera bombalo ankaona kuti akumenyera ufulu wa dziko lawo. Iwo sankafuna kuti azilamulidwa ndi boma limene linalipo pa nthawiyo. Koma kodi n’chiyani kwenikweni chimene chimalimbikitsa anthu kuchita zinthu zankhanzazi? Taganizirani za Hafeni.
Hafeni anabadwira ku Zambia kumalo a anthu othawa kwawo ndipo anakulira kumalo osiyanasiyana a anthu othawa nkhondo kwawo. Iye analowa m’gulu linalake la zigawenga limenenso makolo ake anali m’mbuyomo. Hafeni ananena kuti analowa m’gulu limeneli “chifukwa chokwiya ndi nkhanza zimene abale [ake] anakumana nazo.”
Pokumbukira nthawi imeneyo, Hafeni anati: “Chinthu chimene chimandipweteka kwambiri ndi chakuti ndinakulira m’malo a anthu othawa kwawo. Ana ankakula opanda mayi, bambo kapena achibale awo. Akuluakulu anali komenya nkhondo. Ambiri sanabwerere, moti ineyo sindinawaoneko bambo anga ngakhale pa chithunzi. Chimene ndikudziwa n’chakuti anafera kunkhondo. Zimenezi zimandipwetekabe mpaka pano.”
Choncho pali zifukwa zambirimbiri zimene zimachititsa anthu kuchita zauchigawenga. Kumvetsa zifukwa zimenezo kungatithandize kudziwa ngati anthu adzathetse uchigawenga kapena ayi.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 4]
KODI ZIGAWENGA ZIMATANI?
Katswiri wina wofufuza nkhani zosiyanasiyana, dzina lake Mark Juergensmeyer, anafotokoza kuti: “Kuti munthu anene kuti zachiwawa zinazake zimene zachitika ndi ‘uchigawenga,’ zimadalira mmene munthuyo akuzionera komanso kumene zachitikira. Mwachitsanzo, ngati zachiwawa zachitika kumalo kumene kuli mtendere, anthu amati ndi uchigawenga, koma ngati zachitika kumene kuli nkhondo anthu amaona kuti umenewu si uchigawenga.”
Choncho anthu amaona uchigawenga mosiyanasiyana. Magulu ambiri amene amachita zachiwawa amaona kuti iwo si zigawenga koma anthu omenyera ufulu wawo. Koma malinga ndi zimene munthu wina wolemba mabuku ananena, zigawenga zimachita zotsatirazi: (1) zimalimbana kwambiri ndi anthu wamba osati asilikali komanso (2) zimachita zinthu zachiwawa popanda chifukwa chenicheni, mwina kungofuna kuti anthu azikhala mwamantha. Choncho magulu a anthu amene amachita zachiwawa, kaya akhale opandukira boma kapena otumidwa ndi boma, akhoza kutchulidwa kuti zigawenga.