Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Zikusiyana Pati?

Kodi mungatchule zinthu zitatu zimene zikusiyana pakati pa chithunzi A ndi chithunzi B? Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo malizitsani zithunzizi pozikongoletsa ndi chekeni.

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Ekisodo 25:10-22.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

4. Kodi chithunzi cholondola n’chiti, A kapena B?

KAMBIRANANI:

Kodi likasa linkaimira chiyani kwa Aisiraeli?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Ekisodo 25:22; Levitiko 16:2.

Kodi n’chiyani chinali chofunika kwambiri kuposa likasalo?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Yoswa 7:1-6, 11, 12.

Ngati mukufuna kukondweretsa makolo anu ndi Yehova, kodi n’chifukwa chiyani muyenera kukhala omvera?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Samueli 15:22, 23; Aefeso 6:1-3.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Munthu aliyense m’banja mwanu afufuze zinthu zosiyanasiyana zokhudza likasa la pangano. Kenako mukumane pamodzi n’kukambirana zimene mwapeza. Mwachitsanzo, kodi patapita nthawi mu likasamo ankasungamo chiyani? Jambulani zinthuzo ndipo kambiranani kufunika kwake.

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Aheberi 9:4.

Kodi likasa linkayenera kunyamulidwa bwanji? Kodi chinachitika n’chiyani Davide atalephera kutsatira malangizo amene Yehova anapereka onyamulira likasa?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Ekisodo 37:5; 1 Mbiri 13:7, 9-14; 15:12-15.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 6 ABELE

MAFUNSO

A. Kodi Abele anaphedwa ndi ndani?

B. Kodi Yehova anaiona bwanji nsembe imene Abele anapereka?

C. Lembani mawu amene akusowekapo. Abele ankagwira ntchito ․․․․․.

[Tchati]

4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.

Kulengedwa Anakhala ndi moyo Baibulo linamalizidwa

kwa Adamu cha m’ma 3900 B.C.E. kulembedwa

[Mapu]

Anakhala kunja kwa munda wa Edeni

Munda wa Edeni?

ABELE

ANALI NDANI?

Anali mwana wachiwiri wamwamuna wa Adamu ndi Hava komanso munthu woyamba kutchulidwa m’Baibulo kuti ndi wokhulupirika. Abele anasonyeza kuti ankafuna kuyanjidwa ndi Mulungu popereka nsembe yabwino. Ngakhale kuti mawu amene Abele ananena sanalembedwe m’Baibulo, zimene iye anachita komanso chikhulupiriro chake ndi chitsanzo chabwino kwa ife.​—Genesis 4:1-11; Aheberi 11:4.

MAYANKHO

A. Ndi m’bale wake, Kaini.—1 Yohane 3:11, 12.

B. “Anakondwera” nayo.—Genesis 4:4.

C. Yoweta nkhosa.—Genesis 4:2.

Anthu ndi Mayiko

5. Mayina athu ndi Jennifer ndi Dean, ndipo zaka zathu ndi 7 ndi 10. Timakhala ku Australia. Kodi ku Australia kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 36,400; 63,400 kapena 93,400?

6. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ifeyo timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Australia.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 15

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 ndi 31

1. Zitsulo zonyamulira.

2. Mapiko a Akerubi.

3. Nkhope za akerubi.

4. B.

5. 63,400.

6. C.