Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mavuto Adzatha?

Kodi Mavuto Adzatha?

Kodi Mavuto Adzatha?

Khieu anayamba kuvutika kwambiri bambo ake ataphedwa chifukwa chakuti ng’ombe zawo zinakalowa m’munda mwa eniake. Patapita nthawi, mayi ake ndi alongo ake awiri anaphedwa pa nthawi ya ulamuliro wankhanza wachipani cha Khmer Rouge ku Cambodia. Kenako Khieu anavulala kwambiri ataponda bomba lomwe linakwiriridwa pansi pa nthaka m’nkhalango. Anthu anabwera kudzamuthandiza patadutsa masiku 16 ndipo anafunika kudulidwa mwendo. Chifukwa cha mavuto onsewa, Khieu ananena kuti: “Ndinkangofuna kufa basi.”

MAVUTO saona nkhope. Nthawi iliyonse, munthu aliyense akhoza kukumana ndi mavuto monga masoka achilengedwe, kudwala, kulumala, kumenyedwa ndi achifwamba kapena mavuto ena. Mabungwe osiyanasiyana amagwira ntchito mwakhama kuti achepetse kapena kuthetsa mavuto amene anthu amakumana nawo. Koma kodi khama lawo limapindula?

Ganizirani za vuto la njala. Malinga ndi zimene nyuzipepala ya Toronto Star inanena, anthu ambiri akusowa chakudya komanso pokhala chifukwa cha masoka achilengedwe. Nyuzipepalayo inanenanso kuti “mabungwe osiyanasiyana akulephera kuthetsa njala chifukwa chakuti m’madera ambiri momwe muli njala mumachitikanso zinthu zachiwawa.”

Atsogoleri andale, akatswiri azachipatala komanso anthu ena amtima wabwino ayesetsa kuti athetse mavuto amene anthu akukumana nawo koma alephera. Ntchito zosiyanasiyana zimene mabungwe azachuma akhazikitsa zalephera kuthetsa umphawi. Katemera, mankhwala komanso zipangizo zotsogola zachipatala sizingathetseretu matenda onse. Nthawi zina apolisi ndi asilikali okhazikitsa mtendere amalephera kuthetsa zachiwawa.

N’chifukwa chiyani mavuto sakutha? Kodi Mulungu amamva bwanji akamaona anthu akuvutika? Monga mmene tionere m’nkhani zotsatira, anthu mamiliyoni ambiri amatonthozedwa akapeza mayankho a mafunso amenewa kuchokera m’Baibulo.