Kuchokera kwa Owerenga
Kuchokera kwa Owerenga
M’nkhalango ya Amazon Muli Zamoyo Zambiri (April 2010) Nkhani yanu inanena kuti anthu a mtundu wa Awajun (Aguaruna) amalambira milungu isanu. Ine ndi wa mtundu wa Awajun ndipo ndikuona kuti zimene munanena si zoona. Ndikuona kuti munalakwitsa chifukwa anthu ambiri a mtundu wa Awajun amanena kuti ndi Akhristu ndipo sitimalambira milungu isanu imene munatchula m’magazini anu. Popeza kuti anthu ambiri a mtundu wa Awajun amawerenga magazini anu, chonde konzani zimenezi.
T.P.T., Peru
Yankho la “Galamukani!”: Amene analemba nkhani imeneyi anafunsa mafunso anthu a mtundu wa Aguaruna komanso anafufuza nkhaniyi m’mabuku osiyanasiyana. Limodzi la mabuku amenewa, lakuti Atlas Regional del Perú, lolembedwa mu 2004, linatchula komanso kufotokoza milungu isanu ya anthu a mtundu wa Aguaruna. Komabe, zimene munanena ndi zoona kuti anthu ena a mtundu wa Aguaruna anayamba Chikhristu. Tikupepesa chifukwa chakuti zimene tinalemba zinakukhumudwitsani komanso mwina zinakhumudwitsa anthu ena.
Kodi Mungatani Kuti Muchepetse Vuto Lochita Chibwibwi? (May 2010) Tikukuthokozani kwambiri chifukwa cholemba nkhani imeneyi. Inenso ndimachita chibwibwi ndipo poyamba zinkandivuta kwambiri kucheza ndi anthu. Koma nditawerenga nkhani imeneyi, ndinaona kuti si ine ndekha amene ndili ndi vutoli. Panopa ndatsimikiza mtima kuti chibwibwi chisamandilepheretse kuchita zinthu zofunikira kwambiri pa moyo wanga. Ndipo, mofanana ndi Rafael, ndimati “ndikalephera kutchula mawu enaake, . . . ndimadziseka” kenako n’kunena zinthu zina zanthabwala.
Y. S., Japan
Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndingatani Kuti Ndisamadziderere? (May 2010) Panopa ndili ndi zaka 12 ndipo ndimakhala ndi mayi anga amene akudwala kwambiri. Nditawerenga funso lakuti, “Kodi mumaona kuti anthu amakukondani?” Ndinayankha mosazengereza kuti “Ayi.” Zimenezi zinandikhumudwitsa kwambiri. Choncho, ndinalankhulana ndi Akhristu ena odalirika komanso mayi anga kuti andithandize maganizo. Nkhani imeneyi inandithandiza kuona kuti palibe chifukwa choganizira kuti anthu ena samandikonda. Panopa ndazindikira kuti anthu ambiri amandikonda. Zikomo kwambiri chifukwa chotithandiza achinyamatafe kuona kuti Yehova amatikonda kwambiri.
C. H., France
Nkhani imeneyi inandithandiza kuti ndisamadandaule kwambiri ndikakumbukira zinthu zopweteka zimene zinachitika pa moyo wanga komanso kuti ndisamakhale ndi maganizo akuti ndine wachabechabe. Sindidzaiwala zinthu zitatu zimene zinatchulidwa m’nkhaniyi zothandiza kuti ndisamadzione kuti ndine wosafunika. Chitsanzo cha ndalama yong’ambika chimene munatchula chinandithandiza kwambiri. Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani yabwino kwambiri imeneyi.
S. W., South Korea