Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungapewere Ngozi Zapamsewu

Mmene Mungapewere Ngozi Zapamsewu

Mmene Mungapewere Ngozi Zapamsewu

KODI mungaganize chiyani ngati mutamva phokoso la mateyala akukhwekhwerezeka, zitsulo zikuphwanyika, magalasi akuyoyoka, komanso anthu akukuwa? Ngati munachitapo ngozi, mwina phokoso lotere si lachilendo kwa inu. Bungwe lina la ku America loona za umoyo ndi chiwerengero cha anthu, linanena kuti padziko lonse “anthu pafupifupi 1.2 miliyoni amafa pa ngozi zapamsewu chaka chilichonse, ndipo anthu enanso 50 miliyoni amavulala.”

Komatu ngati mutayesetsa kukhala wosamala, mukhoza kupewa ngozi. Tiyeni tione mmene mungachitire zimenezi.

Kuthamanga, Kusamanga Lamba ndi Kugwiritsa Ntchito Foni

Misewu ina imakhala ndi zikwangwani zosonyeza liwiro lovomerezeka, koma ena amaona kuti liwiro limenelo lingawachedwetse. Komabe dziwani kuti kupitirira liwiro limenelo n’kosathandiza kwenikweni chifukwa nthawi imene mungakafike kumene mukupita sisiyana kwenikweni. Mwachitsanzo, ngati mutawonjezera liwiro kuchoka pa makilomita 100 pa ola n’kufika pa makilomita 120 pa ola, pa mtunda wamakilomita 80, mungafike mofulumira ndi mphindi 7 zokha. Kodi n’zomveka kulolera kuchita ngozi chifukwa chofuna kufulumira ndi mphindi zochepazi?

Lamba amathandiza kwambiri pa ngozi. Dipatimenti ina ya boma ku America inanena kuti kuyambira chaka cha 2005 mpaka 2009, anthu 72,000 m’dzikolo anapulumuka pa ngozi zapamsewu chifukwa chakuti anamanga lamba. Kodi ngati galimoto yanu ili ndi air bag * (kathumba ka mpweya) ndiye kuti simufunika kumanga lamba? Muyenerabe kumanga, chifukwa kathumba kameneka kamagwira bwino ntchito mukamanga lamba. Ndipotu ngati simunamange lamba, kathumbaka kakhoza kupangitsa kuti muvulale kwambiri. Choncho muzimanga lamba mukangokwera galimoto ndipo muzionetsetsanso kuti anthu ena amene akwera m’galimotomo amanga lamba wawo. Chenjezo lina: Ngati mukuyendetsa galimoto, musayerekeze ngakhale pang’ono kulankhula, kuwerenga kapena kulemba uthenga pafoni.

Muziona Mmene Msewu Ulili Komanso Muzikonzetsa Galimoto Yanu

Mateyala a galimoto sagwira bwino msewu ngati msewuwo ndi wonyowa, uli ndi mchenga, fumbi, kapena timiyala. Kuti galimoto isaterereke pomanga mabuleki m’misewu yotere, pamafunika kuyenda pang’onopang’ono.

Komanso oyendetsa galimoto ayenera kusamala kwambiri akafika pamphambano. Katswiri wina ananena kuti nyale yobiriwira ikayaka, muzidikira kaye pang’ono musananyamuke. Kudikira kwa nthawi yochepa chabe kungakutetezeni kuti musawombedwe ndi galimoto imene ikuthamangira kuti idutse nyale yofiira isanayake.

Kukonza galimoto yanu pafupipafupi kumathandizanso kupewa ngozi. Taganizirani zimene zingachitike ngati mabuleki ataduka mukuyendetsa. Kuti apewe zimenezi, anthu ena amakhala ndi munthu amene amawakonzera galimoto yawo nthawi ndi nthawi. Anthu enanso amakonza okha zinthu zina ndi zina. Kaya mumakonza nokha kapena munthu wina amakukonzerani, muzionetsetsa kuti galimoto yanu ikukonzedwa pafupipafupi.

Musamayendetse Mutamwa

Ngakhale munthu amene amayendetsa bwino galimoto, akhoza kuchita ngozi mosavuta ngati wamwa mowa. M’chaka cha 2008, ku America anthu oposa 37,000 anafa pa ngozi zapamsewu. Pa anthu amenewa, anthu oposa 12,300 anafa chifukwa chakuti oyendetsa anali atamwa. Ngakhale kumwa pang’ono chabe kungachititse kuti musayendetse bwino galimoto. Choncho, anthu ena amaona kuti sayenera kumwa ngakhale pang’ono ngati ayendetse galimoto.

Kutsatira malamulo apamsewu, kumanga lamba, kukonzetsa galimoto yanu pafupipafupi ndiponso kupewa kuyendetsa galimoto mutamwa, kungakupulumutseni inuyo ndi anthu ena. Malangizo amenewa angakuthandizeni kwambiri kupewa ngozi pokhapokha ngati mukuwatsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Air bag ndi kathumba kamene kamakhala pafupi ndi chiwongolero ndipo kanapangidwa kuti galimoto ikamenyetseka mwamphamvu kutsogolo, kathumbako kazikhuta mpweya n’kufwamphuka. Izi zimateteza woyendetsayo kuti asamenye chiwongolero.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

MUSAYENDETSE GALIMOTO NGATI MULI NDI TULO

Mkulu wa bungwe lina la ku America loona za mmene tulo timakhudzira anthu, anati: “Munthu akamayendetsa galimoto ali ndi tulo, amafanana ndi munthu amene akuyendetsa galimoto ataledzera.” Mawu amenewa akusonyeza kuti n’zoopsa kwambiri kuyendetsa galimoto muli ndi tulo. Bungweli linanena kuti munthu sayenera kuyendetsa galimoto ngati ali ndi zizindikiro zotsatirazi:

Kulephera kuona bwinobwino, kuphethira kawirikawiri kapena kumva kuti zikope zikulemera

Kulephera kudzutsa mutu chifukwa cha tulo

Kuyasamula pafupipafupi

Kuiwala kuti mwayenda ulendo wautali bwanji

Kusocherasochera kapena kulephera kuona zizindikiro zapamsewu

Kuyandikira kwambiri galimoto yakutsogolo, kuyenda mbali yolakwika, kapena kuyenda kumbali kwambiri kwa msewu

Ngati mukumva zizindikiro zimenezi, sinthanani ndi munthu wina kuti iye ayendetse, kapena imani pamalo abwino kuti mugone kaye pang’ono. Ndi bwino kuchedwa kusiyana n’kusakafika n’komwe kumene mukupita.