Mulungu Adzathetsa Mavuto Athu Onse
Mulungu Adzathetsa Mavuto Athu Onse
“[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
KODI zinthu zosangalatsa zimene Mulungu analonjezazi zidzachitikadi? Taganizirani za chenjezo limene Mulungu anauza munthu woyamba, Adamu. Mulungu anamuuza Adamu kuti ngati atapanda kumumvera, ‘adzafa ndithu.’ (Genesis 2:17) Ndipo Adamu anafadi. Mavuto komanso imfa zimene zafalikira m’dziko kuchokera kwa munthu woyamba Adamu, ndi umboni wakuti zimene Mulungu amanena zimachitikadi. Choncho, palibe chifukwa chokayikira kuti zimene Mulungu analonjeza zoti anthu adzakhala ndi moyo wopanda mavuto zidzachitika.
Taganiziraninso za makhalidwe a Mulungu amene tinakambirana m’nkhani yapita ija. Maganizo amene anthufe tili nawo ofuna kuti mavuto athe ndi umboni wakuti tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. Mofanana ndi Mulungu, anthufe timasonyeza chifundo, chikondi komanso chilungamo. Zimene zikuchitika masiku ano zikusonyeza kuti nthawi yoti Mulungu athetse mavuto athu yayandikira kwambiri.—Onani bokosi lakuti “Kodi Zinthu Zimenezi Zidzachitika Liti?”
Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti ndi Yehova Mulungu yekha amene angathetse mavuto athu? Taganizirani zimene iye, pogwiritsa ntchito Mwana wake Yesu, wakonza kuti athane ndi zinthu zimene zimachititsa kuti anthu azivutika.
Zosankha zathu. Zimene kholo lathu loyamba Adamu anachita posankha kusamvera Mulungu zinatibweretsera mavuto. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.” (Aroma 8:22) Komabe, Mulungu wakonza zochotsa ulamuliro wa Satana m’njira yachilungamo, yachifundo komanso yosavuta kumvetsa. Lemba la Aroma 6:23 limati: “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”
Yesu, yemwe anali munthu wangwiro, sanachite tchimo lililonse pa moyo wake, ndipo imfa yake pamtengo wozunzikirapo inachititsa kuti anthu omvera amasulidwe ku uchimo ndi imfa. Tsopano tili ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wamuyaya m’dziko latsopano. Pa nthawi imeneyo sitidzakhalanso ndi maganizo ofuna kuchita tchimo. Anthu amene mwadala amafuna kuti anzawo azivutika nawonso kudzakhala kulibe, chifukwa “ochita zoipa adzaphedwa.”—Salimo 37:9.
Zinthu zongotigwera komanso kupanda ungwiro kwathu. Yesu Khristu amene anasankhidwa ndi Mulungu kuti akhale Mfumu, ali ndi mphamvu yoletsa masoka achilengedwe. Mwachitsanzo, nthawi ina Yesu ndi atumwi ake atakwera ngalawa, anakumana ndi “chimphepo champhamvu chamkuntho, ndipo mafunde anali kuwomba ngalawayo, mwakuti ngalawayo inangotsala pang’ono kumira.” Atumwiwo atapempha Yesu kuti awathandize, Yesu “anadzuka ndi kudzudzula mphepoyo ndi kuuza nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!” Chotero mphepoyo inaleka. Kenako panachita bata lalikulu.” Atumwi akewo anadabwa kwambiri Maliko 4:37-41.
ndi zimene zinachitikazo. Iwo anati: “Ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera.”—Mu ulamuliro wa Khristu, anthu omvera “adzakhala mwabata ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.” (Miyambo 1:33) Tsoka limeneli likuphatikizapo masoka achilengedwe. Komanso, pa nthawi imeneyo, anthu azidzadziwa kusamalira dziko, kumanga nyumba zolimba ndiponso adzakhala ndi nzeru zodziwa mmene masoka achilengedwe amachitikira. Palibe aliyense amene adzakumane ndi tsoka chifukwa chakuti anali pamalo olakwika komanso pa nthawi yolakwika.
Yesu ali padziko lapansi ananena kuti akadzayamba kulamulira, adzachita chinthu china chodabwitsa chimene chidzathetse mavuto ambiri amene anthu amakumana nawo. Iye anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” (Yohane 11:25) Zoonadi, Yesu ali ndi mphamvu youkitsa anthu mamiliyoni ambiri amene anafa chifukwa cha masoka achilengedwe. Kodi zimene Yesu analonjezazi ndi nkhambakamwa chabe? Ayi. Chifukwatu Yesu ali padziko lapansi anaukitsa anthu mozizwitsa. Ndipo zimenezi zikutitsimikizira kuti zimene ananena zidzachitikadi. Nkhani za anthu atatu amene Yesu Khristu anawaukitsa zimapezeka m’Baibulo.—Maliko 5:38-43; Luka 7:11-15; Yohane 11:38-44.
“Wolamulira wa dzikoli.” Yesu Khristu wasankhidwa ndi Mulungu kuti “awononge Mdyerekezi, amene ali ndi njira yobweretsera imfa.” (Aheberi 2:14) Nthawi ina Yesu ananena kuti: “Tsopano dziko ili likuweruzidwa, wolamulira wa dzikoli aponyedwa kunja tsopano.” (Yohane 12:31) Yesu ‘adzawononga ntchito za Mdyerekezi’ pomuchotsa kuti asamasocheretsenso anthu. (1 Yohane 3:8) Tangoganizirani mmene zinthu zidzakhalire Mdyerekezi akadzachotsedwa! Anthu sadzakhalanso ndi moyo wadyera, wodzikonda komanso wachinyengo.
[Bokosi patsamba 9]
“Kodi Zinthu Zimenezi Zidzachitika Liti?”
Ophunzira a Yesu anafunsa kuti: “Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” (Mateyu 24:3) Zimene Yesu anayankha komanso maulosi ena amene analembedwa iye atafa, zimasonyeza kuti Mulungu watsala pang’ono kuchotsa mavuto amene anthu akukumana nawo. * Yerekezerani maulosi otsatirawa ndi zimene zikuchitika masiku ano.
● Nkhondo—Mateyu 24:7; Chivumbulutso 6:4.
● Njala ndi matenda—Luka 21:11; Chivumbulutso 6:5-8.
● Anthu “akuwononga dziko”—Chivumbulutso 11:18.
● Anthu “okonda ndalama”—2 Timoteyo 3:2.
● Ana “osamvera makolo”—2 Timoteyo 3:2.
● Anthu “okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu”—2 Timoteyo 3:4.
Ngati mungakonde, mungathe kufufuza a Mboni za Yehova m’dera lanu kuti akuthandizeni kuona kuti moyo wopanda mavuto wayandikira. Iwo angasangalale kwambiri kuti muziphunzira nawo Baibulo kunyumba kwanu pa nthawi imene mungasankhe.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 14 Ngati mukufuna kudziwa zambiri, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? pamutu 9 wakuti “Kodi Tili M’masiku Otsiriza?” Bukuli n’lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.