Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nzeru za Mfumu Solomo

Nzeru za Mfumu Solomo

Nzeru za Mfumu Solomo

● Mphunzitsi wina anafunsa ana a m’kalasi yake ya sitandade 4 kuti afotokoze nkhani iliyonse imene akudziwa yokhudza Mfumu Solomo. Mtsikana wina wazaka 9 dzina lake Sheena anafotokoza kuti Solomo anali mfumu yanzeru kwambiri. Anafotokoza mmene mfumuyi inaweruzira nkhani ya amayi awiri omwe ankalimbirana mwana. Aliyense ankanena kuti mwanayo ndi wake. Poyambirira penipeni, anzake a mtsikanayo sanamvetse mmene Solomo anaweruzira nkhaniyo, koma aphunzitsiwo ananena kuti anaiweruza mwanzeru kwambiri.

Sheena anafotokoza kuti nkhaniyi anaitenga m’buku lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Iye anati: “Anzanga 6 a m’kalasi mwathu anapempha kuti ndiwapezere bukuli. Ngakhalenso aphunzitsi angawo anapempha lawo. Mabuku onse amene ndinagawira anakwana 7.”

Nanunso mukhoza kuitanitsa Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Bukuli lili ndi nkhani zokwana 116 zokhudza anthu ndi zinthu zosiyanasiyana za m’Baibulo. Kuti mupeze bukuli lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili patsamba 5 m’magazini ino.

❑ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

❑ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.