Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Zikomo Kwambiri Chifukwa cha Nkhani Zimenezi”

“Zikomo Kwambiri Chifukwa cha Nkhani Zimenezi”

“Zikomo Kwambiri Chifukwa cha Nkhani Zimenezi”

● Anthu padziko lonse akuyamikira nkhani za mu Galamukani! za mutu wakuti “Zoti Banja Likambirane,” zimene zimapezeka patsamba 30 ndi 31 m’magazini iliyonse. Nkhanizi zimakhala ndi mafunso, makadi a Baibulo, zithunzi zoti ana apeze ndiponso zoti banja lichitire pamodzi, zomwe n’zophunzitsa komanso zosangalatsa. Tamvani zimene ena anena.

“Ndimaphunzira Baibulo ndi adzukulu anga awiri, omwe ali ndi zaka 12, polemberana nawo makalata. Ndimawatumizira mapepala a ‘Zoti Banja Likambirane’ ndipo iwo akamaliza kulembapo mayankho awo amanditumiziranso mapepalawo. Iwo amaoneka kuti amasangalala ndi zimene amaphunzira, ndipo zimenezi zimathandiza kuti ndidziwe zinthu zina zofunika kuwafotokozera. Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani zimenezi.”

V. C., United States

“Posachedwapa mwana wanga wazaka zisanu anandipempha kuti asanagone tipange nkhani yakuti, “Kodi Chithunzichi Chalakwika Pati?” Ndinatenga magazini imodzi n’kuyamba kukambirana chithunzi chimene chinali m’nkhaniyo. Iye ankamvetsera mwatcheru pamene ndinkawerenga nkhani yokhudza chithunzicho m’Baibulo. Panopa, amafuna kuti pafupifupi tsiku lililonse tiziphunzira nkhanizo asanagone. Ine ndi banja langa tikukuthokozani kuchokera pansi pa mtima chifukwa chothandiza ana athu kuti azikonda kuphunzira Baibulo.”

M. F., France

“Ndinakumana ndi David wazaka 12, ndi Jennifer wazaka 6, pamalo okwerera basi. Bambo awo ataona kuti ndikugawira magazini a Galamukani! anawatuma kuti adzaone kuti magaziniwo anali otani. Pamene bamboyu amawerenga magaziniwo ndi mwana wawo David, ine ndi Jennifer, mwana wawo winayo, tinkaona zithunzi za mbalame ndi nyama. Ndinakambirana naye zinthu zosiyanasiyana zokongola zimene Yehova Mulungu analenga n’cholinga choti tizisangalala nazo. Titafika mbali yakuti ‘Zithunzi Zoti Ana Apeze,’ patsamba 31, tinayesa kufufuza zithunzizo. Ndisanapeze chithunzi choyamba, Jennifer anali atachipeza kale. Tinayesanso kufufuza chithunzi chachiwiri ndi chachitatu, ndipo iye anazipezanso msangamsanga. Jennifer ankafuna kuti tizingofufuzabe, moti tinamaliza kufufuza zithunzi m’magazini 10! Pomaliza, Jennifer anapempha kuti ndimupatse magazini awiri oti atenge. Pamene ndinkachoka pamalowa, anthu atatu onsewa anayamikira kwambiri chifukwa cha nkhani zabwino za m’magaziniwo.”

M. C., Ecuador