Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mabuku Oti Ana Aziphunzira Pamene Akukula

Mabuku Oti Ana Aziphunzira Pamene Akukula

Mabuku Oti Ana Aziphunzira Pamene Akukula

“Tili ana, tinkasangalala kuwerenga Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Panopa ifeyo tili ndi mwana wamiyezi 6, dzina lake Joshua. Timagwiritsa ntchito bukuli pomuphunzitsa ndipo iye amalikonda kwambiri. Ngakhale kuti ndi wamng’ono kwambiri, Joshua amatha kutchula mayina a anthu a m’Baibulo opitirira 35 amene ali m’bukuli. Iye amakonda kutchula mayina amenewa akamalankhula.”—Anatero Timothy ndi mkazi wake Ann.

“Mwana wanga wazaka zisanu amakonda kuona zithunzi za m’buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, ndipo panopa amatha kuzindikira zithunzi zambiri za m’bukuli. Bukuli limandithandiza kukambirana naye za mavuto amene angakumane nawo kusukulu kapena kumalo ena. Ndikuona kuti buku limeneli ndi lothandiza kwambiri.”—Anatero Jennifer.

“Buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, limafotokoza zinthu zosiyanasiyana zimene achinyamata amakumana nazo. Ineyo ndili ndi zaka 19. Bukuli landithandiza kukhala ndi zolinga pa moyo wanga, kusankha zinthu mwanzeru pa nkhani yokhudza kukhala ndi chibwenzi, komanso landithandiza kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Mulungu. Ndikuona kuti bukuli ndi lothandiza kwa aliyense, ana ndi akulu omwe.”—Anatero Courtney.

Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo

Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso

Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli (mabukuwa). Mungatumize pepalali pogwiritsa ntchito adiresi yoyenera yomwe ili patsamba 5 m’maganizo ino.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.