Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ubongo wa Mwana Umaphunzira Zinthu Mogometsa Kwambiri

Ubongo wa Mwana Umaphunzira Zinthu Mogometsa Kwambiri

Ubongo wa Mwana Umaphunzira Zinthu Mogometsa Kwambiri

A KATSWIRI ena amanena kuti “ubongo wa mwana umatha kuphunzira zinthu mogometsa kwambiri kuposa chinthu china chilichonse padziko lonse.” Mwana akangobadwa, ubongo wake umakhala uli wokonzeka kuphunzira zinthu. Mwachitsanzo, amayamba kusiyanitsa zinthu zimene akuona, zimene akumva komanso zimene akugwira.

Komanso, mwana wongobadwa kumene amatha kusiyanitsa nkhope ndiponso mawu a anthu osiyanasiyana. Amakhudzidwanso kwambiri anthu akamunyamula kapena kungomugwira. Buku lina, lolembedwa ndi Penelope Leach, linati: “Akatswiri ambiri ochita kafukufuku apeza zinthu zosiyanasiyana zimene mwana wakhanda amakonda kuona, kumva komanso kugwira. Malinga ngati pali munthu wachikulire amene akumusamalira, mwana amaona kuti zofuna zake zonsezi zikukwaniritsidwa.” Choncho pamene mwana adakali wakhanda, makolo amakhala ofunikira kwambiri pa moyo wamwanayo.—Babyhood.

‘Ndinkalankhula Ngati Kamwana’

Makolo ndi madokotala amachita chidwi kwambiri kuona kuti mwana amatha kuphunzira kulankhula pomvetsera ena akamalankhula. Akatswiri ochita kafukufuku apeza kuti mwana akangotha masiku ochepa amazolowera mawu a mayi ake ndipo amasangalala kwambiri akamva mawuwo kusiyana ndi mawu a munthu wina. Pakangotha milungu yochepa chabe, amatha kusiyanitsa mawu a m’chinenero cha makolo ake ndi mawu a m’zinenero zina. Pakatha miyezi ingapo, amatha kuzindikira mawu paokhapaokha, ndipo zimenezi zimamuthandiza kuti azitha kudziwa ngati mawu amene munthu akulankhula ndi omveka kapena ayi.

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana.” (1 Akorinto 13:11) Kodi mwana amalankhula bwanji? Nthawi zambiri amalankhula zinthu zosamveka. Koma kodi zimene amalankhulazo zimakhala zopanda tanthauzo? Ayi. Buku limene Dr. Lise Eliot analemba, linanena kuti: “Kuti munthu atulutse mawu, milomo, lilime ndi nsagwada zimagwira ntchito mothandizana, ndipo zimenezi zimachitika m’njira yogometsa kwambiri.” Bukuli linanenanso kuti: “Ngakhale kuti zimene mwana amalankhula zimakhala zosamveka, zimamuthandiza kuti azolowere kugwiritsa ntchito milomo, lilime ndi nsagwada zake pokonzekera kulankhula.”—What’s Going On in There?—How the Brain and Mind Develop in the First Five Years of Life.

Ngakhale pamene mwana akulankhula zosamveka, makolo ayenera kupitirizabe kulankhula naye chifukwa zimenezi zimamulimbikitsa kuti azifunabe kulankhula. Ndipo kulankhulana kotere kumamuthandiza kwambiri, chifukwa luso limene amaliphunzira nthawi imeneyi amadzaligwiritsa ntchito kwa moyo wake wonse.

Nthawi Yosinthana Zochita

Makolo amene ali ndi mwana wakhanda amayesetsa kuchitira mwana wawo chilichonse chimene akufuna. Mwanayo akangolira, amamupatsa chakudya, kumusintha thewera kapena kumunyamula. Kuchitira zimenezi mwanayo n’kofunika kwambiri ndipo umenewu ndi udindo wawo.1 Atesalonika 2:7.

Chifukwa chakuti pa nthawi imeneyi makolo amachitira mwana wawo chilichonse chimene akufuna, iye amaganiza kuti ndi munthu wofunika kwambiri padziko lonse ndipo anthu ena, makamaka makolo ake, ntchito yawo n’kumutumikira basi. Maganizo amenewo ndi olakwika koma n’zomveka kuganiza choncho, chifukwa makolowo akhala akumuchitira chilichonse chimene iye akufuna kwa chaka chimodzi. Iye amadziona ngati mfumu yolamulira dera lalikulu lokhala ndi anthu akuluakulu, omwe ntchito yawo n’kuchita zimene iye wawatuma. Mlangizi wina, dzina lake John Rosemond, analemba kuti: “Zimatenga zaka ziwiri zokha kuti makolo achititse mwana wawo kukhulupirira kuti iye ndi bwana, koma zimatenga zaka pafupifupi 16 kuti makolowo achotse maganizo olakwika amenewa. Zimenezi n’zochititsa chidwi kwambiri: M’kanthawi kochepa makolowo amachititsa mwana wawo kuganiza kuti iye ndi bwana, ndipo zimawatengera nthawi yaitali kuti iwo omwewo achotse maganizo olakwikawo.”

Mwanayo akamafika zaka ziwiri, amayamba kuzindikira kuti maganizo amene anali nawo oti iye ndi mfumu ndi olakwika. Tsopano mwanayo amayamba kuzindikira kuti sangauze makolo ake zochita, koma iwo ndi amene afunika kumuuza zochita. Pa nthawiyi, mwanayo amaona kuti ufumu wake watha ndipo amavutika kutsatira malamulo a makolo ake. Chifukwa chokwiya ndi kusintha kumeneku, nthawi zina amakakamira kuti azichita zofuna zake. Kodi iye amachita zimenezi motani?

Amayamba Kuvuta

Akafika zaka ziwiri, ana ambiri amayamba kuvuta ndipo nthawi zambiri sachedwa kupsa mtima. Makolo amaona kuti nthawi imeneyi ndi yovuta kwambiri kulera mwana kuposa nthawi iliyonse pa moyo wake. Pa nthawiyi ukamuuza kuti achite zinazake, amakonda kunena kuti, “Nono,” kapena “Sindikufuna.” Nthawi zina iye amakwiya chifukwa cha zochita zake zomwe kapena za makolo ake. Safuna kuti mukhale naye pafupi, koma mukamusiyanso amadandaula. Makolo akaona zimene mwana wawo akuchita amadabwa kwambiri, ndipo amavutika kuti amuthandiza bwanji. Koma n’chifukwa chiyani pa nthawiyi mwana amachita zimenezi?

Amachita zimenezi chifukwa cha kusintha kumene kwachitika kuja. Kumbukirani kuti poyamba amati akangolira pang’ono, inuyo munkathamanga kuti mumuchitire zimene akufuna. Koma pa nthawi imeneyi, amayamba kuzindikira kuti ufumu wake unali wakanthawi ndipo tsopano ayenera kudzichitira yekha zinthu zina ndi zina. Pang’ono ndi pang’ono, iye amayamba kudziwa kuti akufunika kugonjera makolo ake, mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti: “Ananu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse.”—Akolose 3:20.

Pa nthawi yovuta imeneyi, makolo sayenera kulekerera mwana wawo. Ngati makolo akulanga mwanayo mwachikondi, iye angasinthe n’kuyamba kuwamvera. Ndipo zikatero, sizikhala zovuta kwa makolowo kuti ayambe kumuphunzitsa zinthu zina zofunika kwambiri.

Kumuphunzitsa Makhalidwe Abwino

Anthu amasiyana ndi nyama chifukwa amatha kuganizira bwinobwino zochita zawo. N’chifukwa chake ngakhale mwana wazaka ziwiri kapena zitatu amatha kuchita manyazi, kudziimba mlandu, kapena kudziwa ngati wachita zinthu zosonyeza kunyada. M’kupita kwa nthawi zimenezi zimamuthandiza kuti akule ndi makhalidwe abwino ndiponso kuti azitha kukana kuchita zinthu zoipa, ngakhale pamene anthu ena akumukakamiza.

Chapanthawi yomweyi, makolo amanyadira kuona mwana wawo akuchita zinthu zina zochititsa chidwi. Iye amayamba kuganizira mmene ena akumvera. Pa nthawi imene anali ndi zaka ziwiri, mwanayo akamasewera ndi anzake ankangoganizira mmene iyeyo akumvera koma tsopano amayamba kuganizira mmene anzakewo akumvera. Amazindikiranso ngati makolo ake akusangalala ndi zimene iye wachita ndipo nthawi zina amachita zinthu zofuna kuwasangalatsa. Choncho, pa nthawi imeneyi sizikhala zovuta kumuphunzitsa.

Mosiyana ndi kale, mwana akafika zaka zitatu amayamba kuphunzira kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika. Choncho, imeneyi ndi nthawi yabwino yoti makolo aziphunzitsa ana awo makhalidwe abwino kuti anawo adzakhale anthu odalirika.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Mwana akangotha masiku ochepa amazolowera mawu a mayi ake ndipo amasangalala kwambiri akamva mawuwo kusiyana ndi mawu a munthu wina

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Mosiyana ndi kale, mwana akafika zaka zitatu amayamba kuphunzira kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika

[Bokosi patsamba 6]

ZIMENE ZINGACHITITSE KUTI MWANA ASASIYE KUVUTA

Mlangizi wina, dzina lake John Rosemond, analemba kuti: “Makolo ena amaganiza kuti mwana amayamba kuvuta kwambiri chifukwa chakuti sanamupatse zimene iye amafuna. Iwo amaganiza kuti ngati achita zinazake zimene zakhumudwitsa mwana wawo, ayenera kumuchitira zimene akufuna msangamsanga kuti asiye kuvuta. Nthawi zina zimachitika kuti amamupatsa zinthu zimene poyamba anamukaniza, kapena pambuyo poti amukwapula, amamupatsa zinthu zambirimbiri mwina kuposa zimene anapempha, n’cholinga choti iwo asamadziimbe mlandu. Poyamba zingaoneke ngati zikuthandiza chifukwa mwanayo amasiyadi kuvuta. Koma vuto ndi lakuti pakapita nthawi mwanayo amazolowera zimenezi ndipo akafuna chinachake amangoyamba kuvutitsa kwambiri.”—New Parent Power.