Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Makolo Ena Ananena

Zimene Makolo Ena Ananena

Zimene Makolo Ena Ananena

Makolo ambiri amakumana ndi mavuto atsopano pa nthawi imene ana awo akula n’kufika pa unyamata. Pa nthawi imeneyi mwana amasokonezeka maganizo, zomwe zimachititsanso kuti makolo asokonezeke maganizo. Ngati mwana wanu wafika msinkhu umenewu, kodi mungamuthandize bwanji? Taonani zimene makolo ena ochokera m’mayiko osiyanasiyana ananena.

AMASINTHA

“Mwana wanga ali wamng’ono, ankatsatira mosavuta malangizo aliwonse amene ndamuuza. Koma panopo amaoneka kuti sandikhulupirira. Amakayikira zimene ndamuuzazo komanso amati sindinamuuze mwaulemu.”—Anatero Frank, wa ku Canada.

“Mwana wanga wamwamuna sakonda kulankhula nane ngati mmene ankachitira kale. Masiku ano, ndimachita kumufunsa kuti ndidziwe zimene akuganiza m’malo moyembekezera kuti anene yekha. Komanso ndikamufunsa funso, safuna kuyankha. Nthawi zina pamapita nthawi yaitali kuti ayankhe funsolo.”—Anatero Francis, wa ku Australia.

“Polankhula ndi ana, kudekha n’kofunika kwambiri. Nthawi zina makolo angafune kuwakalipira koma kulankhula nawo modekha n’kothandiza kwambiri.”—Anatero Felicia, wa ku United States.

KULANKHULANA

“Nthawi zina ndikamalankhula ndi mwana wanga wamkazi amakonda kudziikira kumbuyo chifukwa amaona ngati ndikungomupezera zifukwa. Ndimachita kufunika kumukumbutsa kuti ndimamukonda komanso kuti ndimamufunira zabwino.—Anatero Lisa, wa ku United States.

“Ana anga ali aang’ono ankandimasukira, moti sizinkavuta kudziwa zimene akuganiza. Koma panopa kuti azindimasukira, ndimafunika kuyesetsa kuwamvetsa komanso kulemekeza zosankha zawo.”—Anatero Nan-hi, wa ku Korea.

“Kuletsa achinyamata kuchita zinazake sikokwanira. Timafunika kukambirana nawo bwinobwino komanso kuwapatsa zifukwa zomveka. Kuti zimenezi zitheke timafunika kukhala okonzeka kumva zimene akufuna kunena ngakhale kuti nthawi zina anganene zimene sitimayembekezera.”—Anatero Dalila, wa ku Brazil.

“Mwana wanga wamkazi akalakwitsa, ndimapewa kumudzudzula pagulu.”—Anatero Edna, wa ku Nigeria.

“Nthawi zina ndikamalankhula ndi mwana wanga wamwamuna, ndimayamba kuchita zinthu zina ndipo sindikhala tcheru kuti ndimve zimene akunena. Iye amaona zimenezo ndipo mwina n’chifukwa chake masiku ano sakonda kulankhulana nane. Ndikuona kuti ndifunika kusintha, n’kuyamba kumvetsera kwambiri iye akamalankhula kuti azimasuka nane.”—Anatero Miriam, wa ku Mexico.

KUKHALA NDI UFULU

“Ndinkaopa kupatsa ana anga ufulu wochita zinthu zimene akufuna, ndipo zimenezi zinkachititsa kuti tisamagwirizane. Koma tsiku lina ndinakambirana nawo za nkhaniyi. Ndinawafotokozera chifukwa chimene ndinkaopera kuwapatsa ufulu wowonjezereka, ndipo iwo anandifotokozera chifukwa chake ankaona kuti ankafunikira kupatsidwa ufulu wowonjezereka. Kenako tinafika pogwirizana chimodzi. Ndinayamba kuwapatsa ufulu koma ndinawauza kuti asamapitirire malire amene tinagwirizana.”—Anatero Edwin, wa ku Ghana.

“Mwana wanga wamwamuna ankafuna kuti ndimugulire njinga yamoto. Ine sindinkagwirizana nazo, moti nthawi ina ndinamukalipira kwambiri n’kumuuza kuipa kwa njinga, popanda kumupatsa mpata wofotokoza maganizo ake. Iye anakwiya kwambiri ndipo anapitiriza kundivutitsa. Choncho, ndinapeza njira ina yothetsera nkhaniyo. Ndinamuuza kuti afufuze zambiri zokhudza njingayo, monga kuopsa kwake, mtengo wake komanso zimene zimafunika kuti munthu apatsidwe laisensi. Ndinamuuzanso kuti angachite bwino kukambirana nkhaniyi ndi Akhristu amene amawadalira mumpingo. Ndinazindikira kuti kumulola kufotokoza nkhaniyi momasuka kunathandiza kwambiri kusiyana ndi kungomusankhira zochita. Pamapeto pake, iye anamvetsa chifukwa chake ndimakana.”—Anatero Hye-young, wa ku Korea.

“Timapatsa ana athu malamulo, koma pang’ono ndi pang’ono timawachotsera malamulo ena ndi ena. Ana athu akamagwiritsa ntchito bwino ufulu umene tawapatsawo, tinkawapatsanso ufulu wochita zinthu zina. Anali ndi mwayi woti akachita bwino zinthu apatsidwa ufulu wowonjezereka. Tinkayesetsa kuwasonyeza kuti timafuna kuti akhale ndi ufulu, koma akapezerapo mwayi wochita zosokonekera chifukwa cha ufulu umenewu, tiwalanga.”—Anatero Dorothée, wa ku France.

“Sindinkasintha mfundo zanga. Koma ngati ana anga akundimvera, ndinkatha kuwakhululukira akalakwitsa. Mwachitsanzo, nthawi zina ndinkawakhululukira akabwera kunyumba mochedwerapo. Koma ngati atachita zimenezi kangapo ndinkawapatsa chilango.”—Anatero Il-hyun, wa ku Korea.

“Wantchito akasonyeza kuti ndi womvera komanso wodalirika, bwana wake amamupatsa ufulu wowonjezereka. Mofanana ndi zimenezi, mwana wanga amadziwa kuti akamamvera komanso kuchita zinthu mosapitirira malire, pang’ono ndi pang’ono tidzamulola kuchita zinthu zina payekha. Iye amadziwanso kuti akhoza kulandidwa ufulu umene wapatsidwa ngati atayamba kuchita zinthu motayirira, monga mmene zimakhalira pantchito.”—Anatero Ramón, wa ku Mexico.

[Mawu Otsindika patsamba 22]

“Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”—Miyambo 22:6.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 23]

ZIMENE MABANJA AMAKUMANA NAZO

“Kulera Ana Achinyamata N’kosangalatsa Kwambiri”

Joseph: Ndili ndi ana awiri aakazi, wina wazaka 17 ndipo wina wazaka 13. Ndikamakambirana nawo, ndimamvetsera kwambiri zimene akunena komanso ndimayesetsa kuganizira mmene iwo akuonera nkhaniyo. Kulankhula nawo mwaulemu komanso kuvomereza ndikalakwitsa zinazake n’kumene kwathandiza kuti tizilankhulana momasuka. Mwachidule ndinganene kuti, kulera ana achinyamata n’kosangalatsa kwambiri. Ndipo ndimaona kuti Baibulo ndi limene latithandiza kwambiri.

Lisa: Mwana wathu wamkazi atakula ankafunika kumuthandiza kwambiri. Ndimakumbukira kuti tinkatha nthawi yaitali tikumvetsera zimene akunena, kulankhula naye ndiponso kumulimbikitsa. Ana athu amadziwa kuti akhoza kulankhula nafe momasuka ndiponso kuti ifeyo timalemekeza maganizo awo. Ndimayesetsa kutsatira malangizo a palemba la Yakobo 1:19, akuti “aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.”

Victoria: Ndimagwirizana kwambiri ndi mayi anga. Sindinakumanepo ndi munthu wabwino komanso wokoma mtima ngati mayi anga. Iwo amayesetsa kuchitira zabwino munthu aliyense, moti ndikuchita kusowa mawu owafotokoza kuti iwo ndi munthu wotani. Ndimathokoza kwambiri kukhala ndi mayi oterewa.

Olivia: Bambo anga ndi munthu woganizira ena komanso wopatsa. Iwo amakonda kuthandiza anthu ena ngakhale kuti nthawi zina timakhala ndi zinthu zochepa zoti n’kugawira ena. Bambo amakonda kucheza koma zinthu zikalakwika, sasekerera. Bambo anga ndi munthu wabwino kwambiri ndipo ndimayamikira kukhala ndi bambo ngati amenewa.

“Banja Lathu Silisowa Zochita”

Sonny: Ana athu aakazi akakhala ndi vuto linalake, timakhala pansi n’kukambirana. Aliyense amafotokoza maganizo ake momasuka ndipo timayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo tikamasankha zochita. Ine ndi mkazi wanga, Ynez, timaonetsetsa kuti ana athu akucheza ndi anthu okhwima mwauzimu. Anthu amene timacheza nawo iwonso amacheza nawo, ndipo anthu amene iwo amacheza nawo nafenso timacheza nawo.

Ynez: Banja lathu limakhala ndi zochita zambiri ndipo timakonda kuchitira zinthu pamodzi. Popeza kuti ndife a Mboni za Yehova, nthawi zambiri timatanganidwa ndi ntchito yolalikira, kuphunzira Baibulo ngati banja komanso payekhapayekha. Nthawi zinanso timapita kukagwira nawo ntchito yongodzipereka monga kumanga Nyumba za Ufumu kapena kuthandiza anthu m’madera amene mwachitika masoka achilengedwe. Ngakhale kuti timatanganidwa chonchi, timayesetsa kukhala ndi nthawi yosangalala. Banja lathu silisowa zochita.

Kellsie: Bambo athu amamvetsera kwambiri tikamalankhula nawo ndipo akamasankha zochita pa nkhani zikuluzikulu amafunsa banja lonse kuti aliyense apereke maganizo ake. Mayi anga amamvetsera kwambiri ndikamacheza nawo kapena ndikakhala ndi vuto linalake ndipo amafunitsitsa kundithandiza.

Samantha: Ndikakhala ndi mayi anga, ndimadziona kuti ndine munthu wofunika komanso wokondedwa kwambiri, ngakhale kuti nthawi zina iwo sadziwa zimenezi. Ndikamawauza nkhani amamvetsera kwambiri, komanso ndi munthu wachikondi. Ndimaona kuti ubwenzi wathu ndi wapamwamba kwambiri.

[Zithunzi]

Banja la a Camera: Joseph, Lisa, Victoria, Olivia, ndi Isabella

Banja la a Zapata: Kellsie, Ynez, Sonny, Samantha

[Chithunzi patsamba 22]

Makolo ayenera kupatsa ana awo ufulu, komabe ayeneranso kuwaikira malire