Agogo Ake Anali Atangomwalira Kumene
Agogo Ake Anali Atangomwalira Kumene
● Bambo wina analembera kalata ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Mexico ndipo anati: “Ine si wa Mboni za Yehova koma ndaona kuti magazini anu ndi abwino kwambiri. Magazini yanu ina imene ndinachita nayo chidwi kwambiri inali yonena za kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Pa nthawi imene ndimawerenga magaziniyi n’kuti agogo anga atangomwalira kumene. Ndikupempha kuti munditumizire timabuku timeneti tokwana 8 kuti ndipatse achibale anga n’cholinga choti atonthozedwe.”
Kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira kamayankha funso lakuti, Kodi ndingatani ngati ndikumva chisoni kwambiri? Komanso lakuti, Kodi akufa ali ndi chiyembekezo chotani? Kabukuka kamafotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza imfa komanso zimene zimachitikira munthu amene wamwalira. Kamafotokozanso mmene Mulungu adzakwaniritsire lonjezo lake, kudzera mwa Yesu Khristu, loukitsa anthu akufa n’kudzakhala ndi moyo m’dziko labwino kwambiri la paradaiso.
Ngati mukufuna kuitanitsa kabukuka, lembani zofunika m’munsimu ndipo tumizani ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 5 m’magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire kabukuka.
□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.