Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chakumwa cha ku Mexico

Chakumwa cha ku Mexico

Chakumwa cha ku Mexico

● Anthu a ku Spain amene ankalanda madera ena atafika ku Mexico chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1500, anayamba kupanga chakumwa chinachake chotchedwa pulque, kuchokera ku zomera zooneka ngati khonje. Chakumwachi chinkamveka ngati mowa kungoti sichinali choledzeretsa kwenikweni. Chinkakhala ndi zinthu zina zofunika kwambiri m’thupi monga mapulotini, mavitamini, mchere, komanso zinthu zina zopatsa mphamvu, ndipo chifukwa cha zimenezi anthu ambiri ankachikonda.

Popeza kuti anthu a ku Spain anazolowera kuti pa chakudya chawo payenera kukhalanso mowa, pasanapite nthawi anayamba kufulula mowa wotchedwa mescal kuchokera ku zomera zomwe zija. Mowa umenewu unali waukali kuposa chakumwa choyamba chija. Kenako patapitanso nthawi anayamba kupanga mowa wotchedwa tequila, womwe mpaka pano ukupangidwabe. Masiku ano anthu ambiri ku Mexico amafulula mowa umenewu, moti m’chaka chimodzi chokha ku Mexico kumafululidwa mowa wokwana malita 189 miliyoni. Dzikoli limatumiza pafupifupi theka la mowa umenewu kumayiko ena.

Zomera zimene amapangira mowawu zilipo zamitundu yosiyanasiyana. Zina mwa zomerazi zimakhala za bluu, ndipo zimalimidwa m’madera okwera a dziko la Mexico, makamaka ku Jalisco, pafupi ndi tawuni ya Tequila komwe kunatengedwa dzina la mowawu. * Zomera zimenezi zimatenga zaka pafupifupi 12 kuti zikhwime. Pa nthawi imeneyi zimayamwa mchere wosiyanasiyana m’nthaka. Akamakolola, amachotsa masamba a zomerazi omwe amakhala ndi minga kunsonga kwake n’kuwataya ndipo amatsala ndi chimtima chake chokha. Chimtima chakecho chimatha kulemera makilogalamu 50, ndipo chimakhala ndi madzi ambiri. Chimtima chimodzi cholemera makilogalamu 7, chimatha kutulutsa lita imodzi ya mowa.

Anthu ambiri a ku Mexico amakonda kumwa mowa wa tequila, womwe amathiramo kamchere pang’ono komanso chipatso chinachake chokhala ngati mandimu. Anthu ochokera m’mayiko ena akapita ku Mexico, amakonda mowa winawake wotchedwa margarita, womwe umapangidwa akasakaniza mowa wa tequila ndi mandimu kapena malalanje. Mowawu amamwera m’makapu enaake apadera momwe amaikamonso ayisi ndi kamchere pang’ono. * Mowa wa tequila ndi wotchuka chifukwa umapezeka m’mayiko opitirira 90. M’pake kuti anthu ambiri m’mayiko amenewa amati mowawu ndi chakumwa chapamwamba kwambiri cha ku Mexico.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Ku Mexico kuli mitundu 136 ya zomera zimenezi. Mitundu ingapo amaigwiritsa ntchito pofulula mowa wa pulque ndi zakumwa zina zaukali. Koma mtundu wa bluu wokha wa zomerazi ndi umene amapangira mowa wa tequila.

^ ndime 5 Baibulo sililetsa kumwa mowa pang’ono. (Salimo 104:15; 1 Timoteyo 5:23) Komabe, limaletsa kumwa mowawo mopitirira malire komanso kuledzera.—1 Akorinto 6:9, 10; Tito 2:3.