Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Maganizo Olondola Ndi Ati?

Kodi Maganizo Olondola Ndi Ati?

Kodi Maganizo Olondola Ndi Ati?

PALIBE munthu amene analipo pamene dziko linkalengedwa. Ndipo palibe amene anaonapo zamoyo zikusintha. * Choncho kuti tidziwe kuti zamoyo zinakhalapo bwanji, timadalira umboni umene ulipo. Ndipo sitiyenera kusintha umboniwo kuti ugwirizane ndi zimene ifeyo timakhulupirira.

Anthu ambiri amene sakhulupirira kuti kuli Mlengi, safuna kumva maganizo ena kusiyapo akuti zamoyo zinachita kusintha. Mwachitsanzo wasayansi wina, dzina lake Richard C. Lewontin, ananena kuti: “Timakhulupirira ndi mtima wonse kuti zamoyo zinachita kusintha. Mfundo imeneyi ndi yosatsutsika ndipo ifeyo sitingavomereze zoti kuli Mlengi.”

Koma si asayansi okha amene safuna kumva maganizo osiyana ndi zimene amakhulupirira. Anthu enanso achipembedzo amachita zimenezi. Mwachitsanzo, monga tinanena kale, anthu ena achipembedzo amakakamira mfundo yakuti Mulungu analenga dziko m’masiku 6 enieni, zaka masauzande angapo zapitazo. Chifukwa chosafuna kumva maganizo ena, amayesetsa kutanthauzira molakwika zimene Baibulo limanena kuti zigwirizane ndi zimene iwowo amakhulupirira. (Onani bokosi lakuti  “Kodi Mulungu Analenga Dziko M’masiku 6 Enieni?” patsamba 9.) Anthu amene samvetsa Baibulo komanso sayansi, sapeza umboni wogwira mtima wokhudza mmene zamoyo zinayambira.

Kodi Inuyo Mungafune Kutsatira Ziti?

Anthu amene amati zamoyo zinangokhalapo zokha amakhulupirira zotsatirazi:

1. Zinthu zinazake zinangosakanikirana n’kupanga zinthu zimene zimafunika kuti moyo upangike.

2. Kenako zimenezi zinalumikizana pamodzi n’kupanga selo lokhala ndi DNA, RNA, komanso mapulotini ena omwe amatha kusunga malangizo ofunika kwambiri kuti pakhale zamoyo.

3. M’kupita kwa nthawi, selo limenelo linayamba kugawanika n’kupanga maselo ena. Popanda kugawanika kumeneku, sipakanakhala zamoyo.

Ngati zimenezi zili zoona, kodi zinthu zoyambirirazo kwenikwenizo zinakhalapo bwanji zokha, popanda winawake kuzipanga? Anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha amakanika kufotokoza momveka bwino yankho la funso limeneli. Mwachidule tinganene kuti anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinangokhalapo zokha safuna kuvomereza mfundo yakuti kuli Mlengi.

Koma kodi umboni umasonyeza zotani? Umboni umene ulipo umasonyeza kuti zamoyo sizinasinthe kuchokera ku zinthu zina. Chifukwatu zinthu zikasiyidwa kwa nthawi yaitali popanda wozisamalira, zimawonongeka. Mwachitsanzo, ngati nyumba kapena makina asiyidwa okha kwa nthawi yaitali amawonongeka. Koma anthu amene amanena kuti zamoyo zinachita kusintha amaphunzitsa zosiyana ndi zimenezi. Iwo amaphunzitsa kuti zinthu zikasiyidwa kwa nthawi yaitali, siziwonongeka koma zimayamba kusintha zokha n’kupanga zinthu zapamwamba kwambiri. Mwachitsanzo, buku lina lolimbikitsa maganizo amenewa, linati: “Mphamvu yochokera ku dzuwa ndi imene imachititsa kuti zinthu zizisintha n’kukhala zapamwamba kwambiri.”—Evolution for Dummies.

N’zoona kuti mphamvu za dzuwa zimathandiza poumitsa njerwa, matabwa ndi zina zotero. Koma ngati zinthu zimenezi zitakhala padzuwapo kwa zaka zambiri, zikhoza kuwonongeka. * Amene amakhulupirira kuti zinthu zinachita kusintha amalephera kufotokoza momveka bwino zimene zimachititsa kuti mphamvu ya dzuwa isachuluke kapena kuchepa popanga zinthu zapamwambazo.

Koma ngati timakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa ndi Mulungu, amene ali ndi mphamvu zochuluka, tingathe kufotokoza mosavuta mmene moyo unayambira. Komanso tingathe kufotokoza momveka bwino malamulo a m’chilengedwe amene zinthu zazikulu kwambiri zakuthambo komanso zinthu zing’onozing’ono kwambiri za padziko lapansi, zimayendera. *Yesaya 40:26.

Kukhulupirira kuti kuli Mlengi kumagwirizana ndi mfundo imene anthu ambiri amaikhulupirira, yopezeka pa Genesis 1:1 yakuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”

N’zochititsa chidwi kuti zinthu zatsopano zimene asayansi akutulukira zikusonyeza kuti zamoyo sizinachite kusintha kuchokera ku zinthu zina, zomwe zikuchititsa kuti anthu amene kale ankanena kuti kulibe Mulungu asinthe maganizo awo. * Ena mwa anthu amenewa afika pozindikira kuti zinthu za m’chilengedwe zimasonyeza “makhalidwe a Mulungu” komanso “mphamvu zake zosatha.” (Aroma 1:20) Inunso mungachite bwino kufufuza nkhaniyi bwinobwino kuti mudziwe zolondola chifukwa imeneyi ndi nkhani yofunika kwambiri. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Wasayansi wina, dzina lake Ernst Mayr, ngakhale kuti amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha, ananena kuti: “Mafupa a nyama ofukulidwa pansi sasonyeza kuti zamoyo zinkasintha pang’onopang’ono n’kukhala za mtundu wina.”

^ ndime 12 N’zoona kuti mphamvu yochokera ku dzuwa komanso makemikolo imatha kusintha DNA. Koma kusintha kumeneku sikumachititsa kuti zamoyo zisinthe n’kukhala zamtundu wina. Onani nkhani yakuti “Kodi Chisinthiko Chinachitikadi?” mu Galamukani! ya September 2006.

^ ndime 13 Onani buku lachingelezi la mutu wakuti Is There a Creator Who Cares About You? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 15 Onani nkhani yakuti “Ndinakulira M’banja Losakhulupirira Kuti Kuli Mulungu,” mu Galamukani! ya November 2010.

^ ndime 15 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani yakuti zinthu zinachita kulengedwa osati kusanduka, onani kabuku kachingelezi kakuti Was Life Created? ndi kakuti The Origin of Life—Five Questions Worth Asking, omwe ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi patsamba 8]

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHUFE TILIBE THUPI LANGWIRO?

Asayansi ena akuda nkhawa kuti matupi a anthu akutha mphamvu pang’onopang’ono chifukwa cha kusintha kwa DNA. Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti mfundo yakuti zamoyo zimasintha n’kukhala zapamwamba ndi yabodza. Komano ngati anthufe tinachita kulengedwa ndi Mulungu, n’chifukwa chiyani iye akulola kuti matupi athu azitha mphamvu pang’onopang’ono? Baibulo limayankha funso limeneli. Limanena kuti uchimo ndi umene unachititsa kuti tisakhale ndi matupi angwiro. Lemba la Aroma 5:12 limati: “Monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” Choncho, mfundo yakuti matupi athu akutha mphamvu ndi yogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, osati zimene anthu ena amanena kuti zamoyo zimasintha n’kukhala zapamwamba kwambiri. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti matupi athu adzapitiriza kutha mphamvu mpaka kalekale? Ayi, chifukwa Mulungu walonjeza kuti adzachotsa mavuto onse amene anabwera chifukwa cha kuchimwa kwa makolo athu oyambirira.—Chivumbulutso 21:3, 4.

[Bokosi patsamba 9]

KODI MULUNGU ANALENGA ZINTHU M’MASIKU 6 ENIENI?

 M’Baibulo mawu akuti “tsiku” amanena za nthawi yotalika mosiyanasiyana. Mwachitsanzo, pa Genesis 2:4, masiku onse 6 amene Mulungu analenga zinthu amatchulidwanso kuti “m’tsiku limene Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi kumwamba.” Apa n’zoonekeratu kuti tsiku lililonse likuimira nthawi yaitali ndithu, osati maola 24. Chochititsa chidwi n’chakuti ngakhale kuti Baibulo limanena za kutha kwa tsiku lililonse la masiku 6 amenewa, silinena za kutha kwa tsiku la 7. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti tsiku limeneli silinathe mpaka pano.—Genesis 2:3; Aheberi 4:4-6, 11.

[Chithunzi patsamba 8]

Ngati zinthu zangosiyidwa opanda wozisamalira, m’kupita kwa nthawi zimawonongeka

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Zinthu za m’chilengedwe zimasonyeza makhalidwe a Mulungu komanso mphamvu zake