Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ndingasankhe bwanji mafilimu, mabuku komanso nyimbo zabwino?

Kodi ndingasankhe bwanji mafilimu, mabuku komanso nyimbo zabwino?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi ndingasankhe bwanji mafilimu, mabuku komanso nyimbo zabwino?

Ngati ndinu Mkhristu, muyenera kusamala kwambiri ndi mafilimu amene mumaonera, mabuku amene mumawerenga komanso nyimbo zimene mumamvetsera. Muyenera kupewa kumangoyendera maganizo a anzanu pa nkhani imeneyi chifukwa masiku ano mafilimu, mabuku ndiponso nyimbo zambiri zimalimbikitsa zinthu zoipa monga chiwerewere, chiwawa komanso zamizimu. Komabe, sikuti palibe mafilimu, mabuku kapena nyimbo zabwino zimene mungasangalale nazo. Tiyeni tione zimene zingakuthandizeni kuti musankhe bwino zinthu zimenezi. *

MAFILIMU

Chongani chonchi ✔ mafilimu amene inuyo mumakonda.

○ Nkhani zongoseketsa

○ Zisudzo

○ Zochitika zoopsa

○ Nkhani zopeka zasayansi

○ Mafilimu ena

Kodi mukudziwa . . . ? Ku India amapanga mafilimu osiyanasiyana opitirira 1,000 pa chaka. Palibe dziko linanso limene limapanga mafilimu ochuluka choncho.

Zimene muyenera kupewa. Mafilimu ambiri amalimbikitsa makhalidwe amene sagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Mwachitsanzo, ena amasonyeza anthu akuchita zachiwerewere kapena akuchita zachiwawa, pamene ena amasonyeza zamizimu. Koma kumbukirani kuti Baibulo limati: “Zonsezo muzitaye kutali ndi inu. Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe, ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.” (Akolose 3:8) Ndiponso, Mulungu amanyansidwa ndi anthu amene amachita zilizonse zokhudzana ndi zamizimu.—Deuteronomo 18:10-13.

Mungasankhe bwanji? “Ngati zithunzi zosonyeza mbali zina ndi zina za filimuyo si zabwino, ndimapewa kuonera filimu yonseyo.”—Anatero Jerrine. *

“Sindionera filimu chifukwa chakuti munthu wina wanena kuti ndi yabwino. Ndimaonera filimuyo pokhapokha ngati munthu amene akundiuzayo amatsatira mfundo zofanana ndi zanga.”—Anatero Caitlyn.

“Ngati ndapita koonera filimu, kenako n’kupezeka kuti m’filimuyo ayamba kuonetsa zinthu zoipa, ndimatuluka.”—Anatero Marina.

“Kuti ndidziwe zambiri zokhudza filimu inayake, ndimaifufuza pa Intaneti. Zimenezi zimandithandiza kudziwa ngati filimu imene ndikufuna kuonera ili ndi mbali zosonyeza zachiwerewere, zachiwawa kapena zotukwana.”—Anatero Natasha.

Mfundo yothandiza: Muzisankha mafilimu amene akusonyeza kuti alibe zinthu zambiri zokayikitsa. Mtsikana wina, dzina lake Masami, anati:“Ndimakonda kuonera mafilimu okhudza zochitika za m’nthawi yamakedzana.”

Dzifunseni kuti,

‘Kodi mafilimu amene ndimaonera amandichititsa kuti ndizivutika kutsatira malamulo a Mulungu pa nkhani ya chiwerewere, chiwawa komanso zamizimu?’

MABUKU

Chongani chonchi ✔ mabuku amene inuyo mumakonda.

○ Mabuku a nkhani zopeka

○ Mabuku a zochitika zenizeni

○ Mabuku a anthu otchuka a makedzana

○ Mabuku ena

Kodi mukudziwa . . . ? Ku United States kumasindikizidwa mabuku opitirira 1,000 mlungu uliwonse.

Zimene muyenera kupewa. Mofanana ndi mafilimu, mabuku ambiri amalimbikitsa makhalidwe amene sagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Mwachitsanzo, m’mabuku ena amajambulamo zinthu zolaula kapena kufotokoza zolimbikitsa chiwerewere, pamene ena amalembamo zinthu zamizimu. Zimenezi n’zosagwirizana ndi zimene Baibulo limanena, kuti: “Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu.” (Aefeso 5:3) Baibulo limanenanso kuti zinthu zamizimu ndi “zoipa pamaso pa Yehova.”—2 Mafumu 17:17.

Mungasankhe bwanji? “Ndikafuna kugula buku, ndimawerenga kaye mawu ofotokoza mwachidule zimene zili m’bukulo opezeka kuchikuto, ndipo kenako ndimaona mofulumira mitu ya bukulo. Ngati ndaona zinazake zokayikitsa, sindigula.”—Anatero Marie.

“Ndili mwana sindinkaganizira kwambiri zochita zanga. Koma kenako zinthu zinasintha. Panopa ndinazindikira ubwino womvera zimene chikumbumtima changa chikundiuza. Mwachitsanzo, ndikaona kuti buku limene ndikuwerenga si labwino, ndimalisiya. Ndimatha kudziwa kuti buku ili silikugwirizana ndi zimene mawu a Mulungu amanena.”—Anatero Corinne.

Mfundo yothandiza: Muziwerenga mabuku osiyanasiyana. “Ndimaona kuti mabuku onena za zinthu zamakedzana ndi abwino kwambiri kuyerekeza ndi mabuku a nthano a masiku ano. Mawu amene amagwiritsa ntchito m’nkhaniyo, anthu a m’nkhaniyo komanso zochitika zosiyanasiyana za m’nkhani yonseyo zimakhala zosangalatsa kwambiri.”—Anatero Lara.

Dzifunseni kuti,

Kodi mabuku amene ndimawerenga amalimbikitsa makhalidwe amene Mulungu amadana nawo?’

NYIMBO

Chongani chonchi ✔ nyimbo zimene inuyo mumakonda.

○ Rock

○ Classical

○ Jazz

○ R&B

○ Hip-hop

○ Nyimbo zina

Kodi mukudziwa . . . ? Makampani anayi okha amatha kujambula zimbale za nyimbo pafupifupi 30,000 pa chaka.

Zimene muyenera kupewa. Mofanana ndi mafilimu komanso mabuku, nyimbo zambiri masiku ano zimalimbikitsa makhalidwe oipa. Mawu komanso zithunzi zake zimakhala zolaula ndipo zingalimbikitse munthu kuchita zachiwerewere. (1 Akorinto 6:18) Mtsikana wina wazaka 21, dzina lake Leigh, anati: “Nyimbo zambiri masiku ano zimalimbikitsa khalidwe losagwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Anthu ambiri amakopeka ndi nyimbo chifukwa chakuti anasakaniza bwino zida zake ndipo saganizira kwenikweni za mawu a nyimboyo.”

Mungasankhe bwanji? “Ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi Akhristu achikulire ataona nyimbo zanga, sindingachite manyazi?’ Zimenezi zimandithandiza kuti ndizisankha nyimbo mwanzeru.”—Anatero Leanne.

Mfundo yothandiza: Muzimverako nyimbo za mtundu wina. Mnyamata wina dzina lake Roberto anati: “Bambo anga amakonda nyimbo za classical, moti ineyo ndakula ndikumvetsera nyimbo zimenezi. Kudziwa mbiri ya nyimbo zimenezi kwinaku ndikuphunzira kuimba piyano, kwanditsegula m’maso.”

Dzifunseni kuti,

“Kodi nyimbo zimene ndimakonda zimandichititsa kuti ndizivutika kutsatira malamulo a Mulungu pa nkhani ya chiwerewere?

MUKAFUNA KUPEZA MFUNDO ZINA.

Onani buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, chaputala 31 ndi 32. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Galamukani! sisankhira anthu mafilimu, mabuku kapena nyimbo. Cholinga cha nkhaniyi n’kungokuthandizani kuti muziganizira mfundo za m’Baibulo posankha zinthu zimenezi.—Salimo 119:104; Aroma 12:9.

^ ndime 13 Tasintha mayina ena m’nkhaniyi.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

Amalonda amangofuna ndalama basi. Alibe nazo ntchito ngati mafilimu amene mumaonera, mabuku amene mumawerenga komanso nyimbo zimene mumamvetsera, zikugwirizana ndi mfundo za m’Baibulo kapena ayi.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]

“Mabuku ndiponso mafilimu ambiri amakhala ndi zinthu zoipa zosagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Koma ndikapeza buku kapena filimu yabwino, ndimasangalala kwambiri.” Adrian

[Bokosi patsamba 18]

FUNSANI MAKOLO ANU

Kodi mukayerekeza nthawi yanu ndi panopa, chasintha n’chiyani pa nkhani ya zisangalalo? Nanga zinthu zinali bwanji pamene makolo anu anali achinyamata?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 19]

“Nyimbo zina zingatichititse kulakalaka zinthu zomwe Akhristu amafunika kupewa. Si bwino kunyalanyaza chikumbumtima chathu chifukwa chakuti nyimbo ikumveka bwino.” Janiece