Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
Ku Germany, makanda 7 pa makanda 10 alionse amakhala kuti ayamba kale kuonekera pa Intaneti. Makolo awo amawapangira malo pa Intaneti, pomwe amalembapo zambiri zokhudza iwowo monga adiresi yawo, zithunzi ndi zinthu zina zotero. Komabe akatswiri akuchenjeza makolo kuti ayenera kusamala chifukwa zimene amaika pa Intaneti zidzakhalapo mpaka kalekale.—BABY UND FAMILIE, GERMANY.
Malinga ndi kafukufuku wa boma, chaka chilichonse ku Russia akazi okwana 14,000 amafa chifukwa chochitidwa nkhanza ndi amuna awo.—RIA NOVOSTI, RUSSIA.
Chipale chofewa chimene chikumagwa kuchoka pamwamba pa phiri la Everest, pa mtunda wa mamita 6,858 ndi mamita 7,752, chikumakhala ndi poizoni yemwe akhoza kuipitsa madzi akumwa. Akuti poizoniyu akuchuluka chifukwa chakuti anthu akuwononga chilengedwe.—SOIL SURVEY HORIZONS, U.S.A.
Kampani imodzi yokha imene imaloledwa kusindikiza Mabaibulo ku China, akuti Mabaibulo onse amene yasindikiza tsopano akwana 80 miliyoni. Chaka chilichonse, kampaniyi imasindikiza Mabaibulo okwana 1 miliyoni. Ku China kumasindikizidwa 25 peresenti ya Mabaibulo onse amene amasindikizidwa padziko lonse.—XINHUA, CHINA.
“Posachedwapa anthu 10 pa anthu 100 alionse ku America amene anabadwira m’mabanja a Katolika anasiya tchalitchichi.”—NATIONAL CATHOLIC REPORTER, U.S.A.
Masoka Achilengedwe a M’chaka cha 2010
Kampani inayake yotchuka ya inshulansi inanena kuti m’chaka cha 2010 kunachitika masoka achilengedwe okwana 950 padziko lonse. Chimenechi chinali chiwerengero chokwera kwambiri tikaganizira kuti pa zaka 10 zapitazo, m’chaka chilichonse kunkachitika masoka achilengedwe okwana 785. Masoka asanu oopsa kwambiri anali zivomerezi zimene zinachitika ku Chile, China ndi ku Haiti; kutsefukira kwa madzi kumene kunachitika ku Pakistan; ndi tsoka lomwe linachitika ku Russia, komwe anthu masauzande ambiri anafa chifukwa cha kutentha komanso kuipitsidwa kwa mpweya. Kumpoto kwa Ulaya, phulusa lomwe linabwera chifukwa cha ziphalaphala zimene zinaphulika m’nthaka ku Iceland, ngakhale kuti silinawononge kwenikweni zinthu, linachititsa kuti ndege zisiye kuyenda kwa kanthawi. Ku Australia, mvula yamatalala inawononga katundu wa ndalama zoposa madola 2 biliyoni. Nyuzipepala ina ya ku London inanena kuti: “Ndalama zonse zimene zinawonongeka padziko lonse, kuphatikizapo zimene makampani a inshulansi analephera kulipira, zinakwera kuchoka pa madola 50 biliyoni m’chaka cha 2009 n’kufika pa 130 biliyoni m’chaka cha 2010.”—The Telegraph.
Kodi Anthu Amene Amajambulidwa m’Mabuku a Mbiri Yakale Anali Ofanana ndi Ife?
Magazini ya New Scientist inanena kuti: “Maganizo amene anthu akhala nawo kwa nthawi yaitali akuti anthu akale anali otsika kwambiri poyerekeza ndi ifeyo akusintha, chifukwa asayansi akupeza umboni wosonyeza kuti anthu amenewa ankatha kuchita zinthu zimene ifeyo timachita masiku ano.” Akuti zimene asayansi apeza posachedwapa zikusonyeza kuti anthu akalewa, ankatha kumanga nyumba, malo osonkhapo moto, kuzimitsa moto, kuvala zovala, kuphika chakudya, kupanga zida zogwiritsa ntchito, ndiponso kupanga guluu womatira mikondo. Akuti pali umboni wosonyeza kuti anthu amenewa ankatha kusamalira wodwala, ankavala zovala za pamaliro, komanso ankaika munthu amene wamwalira m’manda. Malinga ndi zimene ananena pulofesa wa payunivesite ya Washington ku St. Louis, Missouri, m’dziko la America, dzina lake Erik Trinkaus, “anthu akalewa ankachita zinthu ngati anthu ndithu ndipo zikuoneka kuti anali ndi nzeru ngati zathu.”