Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Buku la Mfundo Zakuya Koma Zolembedwa Mosavuta’

‘Buku la Mfundo Zakuya Koma Zolembedwa Mosavuta’

‘Buku la Mfundo Zakuya Koma Zolembedwa Mosavuta’

● Umu ndi mmene munthu wina ku Nebraska, U.S.A., analifotokozera buku limene anawerenga. Iye anati: “Ndili ndi zaka 56 ndipo sindili pabanja. Ndangomaliza kumene kuwerenga buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ndagoma kwambiri ndi mmene bukuli linalembedwera. Lili ndi mfundo zakuya koma zolembedwa mosavuta kumva.” Iye anapitiriza kuti: “Zithunzi za m’bukuli n’zochititsa chidwi kwambiri. Ndikanakhala ndi ana kapena zidzukulu, bwenzi tikuthera nthawi yaitali kuwerenga komanso kuona zithunzi za m’bukuli.”

Mayi wina wa ku Georgia, U.S.A., ananenanso zofanana ndi zimenezi. Iye analemba kuti: “Mwana wazaka 6 wa achemwali anga, dzina lake Avery, anatengera bukuli kusukulu kuti akaonetse anzake a m’kalasi. Iye atakambirana za m’bukuli ndi anzakewo, aphunzitsi ake anachita chidwi kwambiri, moti anakonza zoti Avery aziwerenga bukuli pamaso pa kalasiyo tsiku lililonse.” Mayiwa ananenanso kuti: “Zimenezi zathandiza kwambiri kuti iye azilalikira anzake komanso aphunzitsi akewo.”

Mungaitanitse buku lokhala ndi zithunzi zokongola limeneli, lomwe ndi lamasamba 256, polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi n’kutumiza ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.

[Chithunzi patsamba 32]

N’chifukwa chiyani tinganene kuti Msamariyayu anali munthu wabwino?